Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu’

‘Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu’

Olengeza Ufumu Akusimba

‘Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu’

ANTHU ambiri pachilumba chotentha cha Jamaica panyanja ya Caribbean amalidziŵa bwino Baibulo. Ndipo Baibulo la King James Version limapezeka pafupifupi m’nyumba iliyonse. Anthu ena adzionera okha kuti “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita [“amphamvu,” NW].” (Ahebri 4:12) Mphamvu imeneyi imasintha miyoyo ya anthu monga momwe chitsanzo chotsatirachi chikusonyezera.

Mwamuna wina dzina lake Cleveland anali atangofika kunyumba kuchokera kuntchito, pamene wa Mboni za Yehova anafika kudzacheza naye. Atakambirana mfundo zina za m’Malemba, Mboniyo inamusiyira Cleveland buku lothandiza kuphunzira Baibulo lakuti Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Iye sanadziŵe mmene Mawu a Mulungu angasinthire moyo wake.

Cleveland ankapemphera kwa Mulungu katatu patsiku kuti amuthandize kupeza njira yolondola yomulambirira. Iye anaona kuti makolo ake sanali kulambira m’njira yolondola. Ndiyeno anafufuza zipembedzo zina, koma anakhumudwa nazo kwambiri. Ngakhale anali atamvapo za Mboni za Yehova, iye ankakayikira ngati zingakhale ndi choonadi. Komabe, Cleveland anavomera kuphunzira Baibulo ndi Mboni yomwe inafika kunyumba kwake ija. N’chifukwa chiyani anavomera? Chifukwa chakuti ankafuna kuzisonyeza Mbonizo kuti si zolondola.

Posakhalitsa Cleveland anazindikira kuti khalidwe la chiwerewere lomwe ankachita ndi akazi aŵiri ndi losakondweretsa Mulungu. (1 Akorinto 6:9, 10) Atangophunzira maulendo aŵiri okha, iye analimba mtima kukathetsa ubwenzi wake ndi akaziwo. Ndipo anayamba kupita kumisonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu. Koma kupita kumisonkhano kunalinso kovuta.

Cleveland ankaseŵera bwino kwambiri mpira wamiyendo m’timu ya m’deralo, ndipo kupita kumisonkhano kunkamuvuta chifukwa cha maseŵeraŵa. Kodi akanatani? Ngakhale kuti oseŵera anzake, mphunzitsi wa timuyo, ndiponso anzake ena, ankam’limbikitsa kwambiri, Cleveland anaganiza zosiya kuseŵera mpira m’timuyo. Inde, Mawu a Mulungu anali atayamba kugwira ntchito, kumulimbikitsa kuti apindule.

Mphamvu ya Mawu a Mulungu inayamba kuonekeranso pamene Cleveland anayamba kuuza ena zomwe ankaphunzira m’Baibulo. (Machitidwe 1:8) Mapeto ake, anzake aŵiri omwe ankaseŵera nawo mpira anayamba kufika pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Cleveland atayenerera kukhala wofalitsa wa uthenga wabwino, anali kusangalala kwambiri ndi utumiki, kuthandiza anthu ena pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu.

Mphamvu ya Mawu a Mulungu inapitiriza kumulimbikitsa Cleveland ndipo m’kupita kwanthaŵi anasonyeza kudzipatulira kwake kwa Yehova mwa kubatizidwa. Tsopano ali ndi mwayi wapadera wochita utumiki wanthaŵi zonse ndiponso ndi mtumiki wotumikira mumpingo.

Ku Jamaica ndiponso padziko lonse, anthu miyandamiyanda azindikira kuti, Mawu a Mulungu ‘alidi amoyo ndiponso amphamvu.’

[Mapu/​Chithunzi patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

JAMAICA

[Mawu a Chithunzi]

Mapu ndi dziko: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.