Pamene Kuthaŵa Kumakhala Kwanzeru
Pamene Kuthaŵa Kumakhala Kwanzeru
ANTHU kaŵirikaŵiri m’dziko lamakonoli amasonyeza mzimu wa n’kafa ndikhale ndiponso udani. Ndipotu dzikoli ladzala ndi mayesero. Munthu amene amathaŵa pa zochitika zinazake amati ndi wopepera kapena wamantha. Munthu woteroyo mwina mpaka amamuseka kwambiri.
Komabe, Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti nthaŵi zina kuthaŵa kumakhala kwanzeru ndiponso kumasonyeza kulimba mtima. Yesu Kristu potsimikiza mfundo imeneyi, anauza ophunzira ake asanawatumize kokalalikira kuti: “Pamene angakuzunzeni inu m’mudzi uwu, thaŵirani mwina.” (Mateyu 10:23) Inde, ophunzira a Yesu anafunikira kuthaŵa ozunzawo. Sanafunikire kuchita chilichonse ngati kuti akumenya nkhondo yachipembedzo yofuna kutembenuza anthu mowaumiriza. Iwo anali kulalikira uthenga wamtendere. (Mateyu 10:11-14; Machitidwe 10:34-37) M’malo mokwiya ndi zochitikazo, Akristu anafunika kuthaŵa kuti atalikirane ndi anthu ozunzawo. Mwa kuchita zimenezi, iwo anasungabe chikumbumtima chabwino ndiponso unansi wawo wamtengo wapatali ndi Yehova.—2 Akorinto 4:1, 2.
Nkhani yosiyana ndi imeneyi imapezeka m’buku la m’Baibulo la Miyambo. Imasimba za mnyamata wina yemwe m’malo mothaŵa atakumana ndi chiyeso, anatsatira mkazi wachiwerewere “monga ng’ombe ipita kukaphedwa.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? Anaona mbwadza chifukwa chogonja ku chiyeso chomwe chinam’phetsa.—Miyambo 7:5-8, 21-23.
Nanga inu mungatani ngati mwakumana ndi chiyeso choti muchite chiwerewere kapena zinthu zomwe zingakuvulazeni? Mawu a Mulungu amanena kuti choyenera kuchita ndicho kuthaŵa, kutalikirana ndi zochitikazo mwamsanga.—Miyambo 4:14, 15; 1 Akorinto 6:18; 2 Timoteo 2:22.