Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndiye Pothaŵirapo Pathu

Yehova Ndiye Pothaŵirapo Pathu

Yehova Ndiye Pothaŵirapo Pathu

“Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothaŵirapo panga! . . . Palibe choipa chidzakugwera.”​—SALMO 91:9, 10.

1. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndiye pothaŵirapo pathu?

YEHOVA alidi pothaŵirapo anthu ake. Ngati tadzipereka kotheratu kwa iye, tingakhale “osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osawonongeka.” Chifukwa chiyani? Chifukwa Yehova amatipatsa “ukulu woposa wa mphamvu [“mphamvu yoposa yachibadwa,” NW].” (2 Akorinto 4:7-9) Inde, Atate wathu wakumwamba amatithandiza kuti tichite zimene iye amafuna, ndipo timaonadi zimenezi mwa zimene wamasalmo ananena. Anati: “Popeza unati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Unaika Wam’mwambamwamba chokhalamo chako; palibe choipa chidzakugwera.”​—Salmo 91:9, 10.

2. Kodi tinganene chiyani za Salmo 91 ndipo likulonjeza chiyani?

2 Mawu ameneŵa mu Salmo 91 akuoneka kuti analembedwa ndi Mose. Pamwamba pa Salmo 90 pali mawu onena kuti analilemba ndi Mose, ndipo Salmo 91 likutsatira Salmoli popanda mawu osonyeza kuti analemba ndi wina. Mwinamwake Salmo 91 analiimba molandizana, ndiko kuti, mwina mmodzi anaimba koyamba (91:1, 2), gulu la anthu n’kudzayankha (91:3-8). Mwina woimba mmodzi yemweyo anaimbanso (91:9a), ndipo anthu anamuyankha (91:9b-13). Ndiyeno woimba mmodzi ayenera kuti anaimba mawu omaliza (91:14-16). Kaya anaimba motere kapena ayi, Salmo 91 limalonjeza kuti gulu la Akristu odzozedwa lidzatetezedwa mwauzimu ndipo limatsimikizanso chimodzimodzi kwa gulu la anzawo amene adzipatulira kwa Mulungu. * Tiyeni tipende Salmo limeneli ndi kuona mmene likukhudzira atumiki a Yehova onseŵa.

Tetezekani ‘M’ngaka ya Mulungu’

3. (a) Kodi “ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” n’chiyani? (b) Kodi n’chiyani chimachitika ‘tikagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse’?

3 Wamasalmo anaimba kuti: “Iye amene akhala pansi m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. Ndidzati kwa Yehova, Pothaŵirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndim’khulupirira.” (Salmo 91:1, 2) “Ngaka yake ya Wam’mwambamwamba” ndiwo malo ophiphiritsa achitetezo chathu, makamaka kwa odzozedwa, amene Mdyerekezi akulimbana nawo kwambiri. (Chivumbulutso 12:15-17) Bwenzi tonse atatiwononga tikanakhala kuti tilibe chitetezo chimene tapeza monga anthu amene tikugona mwa Mulungu monga alendo auzimu. Mwa ‘kugonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse,’ Mulungu amatiteteza mu mthunzi wake. (Salmo 15:1, 2; 121:5) Palibenso pothaŵirapo pena kapena linga lotetezeka kwambiri kuposa Ambuye Mfumu, Yehova.​—Miyambo 18:10.

4. Kodi Satana yemwe ndi “wosaka mbalame” amagwiritsa ntchito misampha yotani, ndipo timawonjoka bwanji ku misampha imeneyo?

4 Wamasalmoyu anawonjezera kuti: [Yehova] adzakuwonjola ku msampha wa msodzi [“wosaka mbalame,” NW], ku mliri wosakaza.” (Salmo 91:3) Wosaka mbalame mu Israyeli wakale nthaŵi zambiri anali kupha mbalame pogwiritsa ntchito msampha kapena diŵa. Ina mwa misampha ya Satana yemwe ndi “wosaka mbalame,” ndiyo gulu lake loipa ndiponso “machenjerero” ake. (Aefeso 6:11) Amatitchera misampha mobisalira kuti tichite zoipa ndi kugwa mwauzimu. (Salmo 142:3) Komabe, popeza tinasiya kuchita zosalungama, “moyo wathu unawonjoka ngati mbalame mu msampha.” (Salmo 124:7, 8) Tikuyamikiratu kwambiri kuti Yehova amatipulumutsa kwa “wosaka mbalame” woipa ameneyu.​—Mateyu 6:13.

5, 6. Kodi ndi “mliri” wanji umene ‘wasakaza’ anthu, koma n’chifukwa chiyani anthu a Yehova sakugonja?

5 Wamasalmo anatchula za “mliri wosakaza.” Monga mliri wa matenda opatsirana, pali chinachake chimene ‘chimasakaza’ anthu onse ndiponso amene ali kumbali ya ulamuliro wa Yehova. Pamfundo imeneyi, wolemba mbiri wina, Arnold Toynbee analemba kuti: “Kuyambira pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inatha, kufuna kudzilamulira kwachititsa kuti mayiko odziimira paokha achuluke kuŵirikiza kaŵiri . . . Maganizo a anthu masiku ano akupitirizabe kugaŵikana.”

6 Kwa zaka zambirimbiri, olamulira ena asonkhezera nkhondo zogaŵanitsa mitundu. Aumirizanso anthu kuti aziwalambira kapena kulambira mafano kapena zizindikiro zosiyanasiyana. Koma Yehova sanalole kuti “mliri” umenewu ugonjetse atumiki ake. (Danieli 3:1, 2, 20-27; 6:7-10, 16-22) Monga abale okondana padziko lonse, timalambira Yehova yekha ndipo mogwirizana ndi Malemba sitiloŵerera mu ndale. Ndiponso timazindikira mopanda tsankhu kuti “m’mitundu yonse, wakumuopa [Mulungu] ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35; Eksodo 20:4-6; Yohane 13:34, 35; 17:16; 1 Petro 5:8, 9) Ngakhale kuti ‘amatisakaza’ mwa kutizunza monga Akristu, ndife achimwemwe ndiponso otetezeka mwauzimu “m’ngaka yake ya Wam’mwambamwamba.”

7. Kodi Yehova amatiteteza bwanji “ndi nthenga zake”?

7 Popeza Yehova ndiye pothaŵirapo pathu, timalimbikitsidwa ndi mawu akuti: “Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathaŵira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza [ndi linga, NW].” (Salmo 91:4) Mulungu amatiteteza monga mmene mbalame imachitira kuuluka motchingira ana ake kuwateteza. (Yesaya 31:5) ‘Amatifungatira ndi nthenga zake.’ Nthaŵi zambiri, “nthenga” za mbalame zimaimira mapiko ake. Imazigwiritsa ntchito kufungatira ana ake, kuwateteza ku zinthu zimene zingawawononge. Mofanana ndi ana a mbalame, ndife otetezeka kunsi kwa nthenga zophiphiritsa za Yehova chifukwa tathaŵira ku gulu lake loona lachikristu.​—Rute 2:12; Salmo 5:1, 11.

8. Kodi ndi motani mmene “choonadi” cha Yehova chilili chikopa chotchinjirizira chachikulu ndiponso linga?

8 Timadalira “choonadi” chake kapena kukhulupirika kwake. Chili ngati chikopa chotchinjirizira cha m’nthaŵi zakale chimene chinali chachikulu kwambiri moti n’kuphimba thupi lonse. (Salmo 5:12) Kukhulupirira chitetezo chimenecho kumatithandiza kukhala opanda mantha. (Genesis 15:1; Salmo 84:11) Mofanana ndi chikhulupiriro chathu, choonadi cha Mulungu ndicho chikopa chotchinjirizira chachikulu kwambiri chimene chimaimitsa mivi yoyaka moto ya Satana ndi kutiteteza kwa adani. (Aefeso 6:16) Choonadi chake chili ngatinso linga, thanthwe lotetezera lolimba kwambiri lomwe tabisalako ndi kuima amphumphu.

‘Sitidzaopa’

9. Kodi n’chifukwa chiyani usiku ungakhale nthaŵi yoopsa kwambiri, koma n’chifukwa chiyani ife sitiopa?

9 Poganizira za chitetezo cha Mulungu, wamasalmo anati: “Sudzaopa choopsa cha usiku, kapena muvi wopita usana; kapena mliri woyenda mumdima, kapena chiwonongeko chakuthera usana.” (Salmo 91:5, 6) Popeza anthu amachita zoipa zambiri kukakhala mdima, usiku ungakhale nthaŵi yoopsa kwambiri. Kuwonjezera pa mdima wauzimu umene wakuta dziko lonse lerolino, adani athu amayesa kutinyenga kuti tisiye kukonda zinthu zauzimu ndi kuletsa ntchito yathu yolalikira. Koma ‘sitiopa choopsa cha usiku’ chifukwa Yehova amatiteteza.​—Salmo 64:1, 2; 121:4; Yesaya 60:2.

10. (a) Kodi “muvi wopita usana” uyenera kuti ukutanthauzanji, ndipo timachita bwanji ndi muvi umenewu? (b) Kodi “mliri woyenda mumdima” n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani sitiopa?

10 “Muvi wopita usana” ukuoneka kuti ukutanthauza kutsutsa. (Salmo 64:3-5; 94:20) Kutsutsa poyera utumiki wathu wopatulika kumeneku kumakhala kopanda phindu pamene tikulimbikira kuuza anthu choonadi. Ndiponso, sitiopa “mliri woyenda mumdima.” Umenewu ndi mliri wophiphiritsa umene uli mu mdima wa dziko lodzala ndi makhalidwe oipa ndi chipembedzo chonyenga limene likugona mwa Satana. (1 Yohane 5:19) Mliri umenewu umawononga maganizo ndi mitima ya anthu, ndi kuwachititsa kusadziŵa za Yehova, zolinga zake, ndi zinthu zimene iye wagaŵira mwachikondi. (1 Timoteo 6:4) Ife sitiopa mu mdima umenewu, popeza tili nako kuŵala kwauzimu kwakukulu.​—Salmo 43:3.

11. Kodi n’chiyani chimachitikira anthu amene ‘akuthera masana’?

11 Sitiopanso “chiwonongeko chakuthera usana.” “Usana” ungatanthauze zimene amati kuwala kwa dziko lapansi. Amene amakondetsa zinthu zakuthupi, amawonongeka mwauzimu. (1 Timoteo 6:20, 21) Pamene tikulengeza uthenga wa Ufumu molimba mtima, sitiopa adani athu, chifukwa Yehova ndiye Mtetezi wathu.​—Salmo 64:1; Miyambo 3:25, 26.

12. Kodi anthu zikwizikwi ‘akugwa’ pambali pa ndani, ndipo motani?

12 Wamasalmo anapitiriza kuti: “Pambali pako padzagwa chikwi, ndi zikwi khumi pa dzanja lamanja lako; sichidzakuyandikiza iwe. Koma udzapenya ndi maso ako, nudzaona kubwezera chilango oipa.” (Salmo 91:7, 8) Ambiri ‘akugwa’ mu imfa yauzimu “pambali” pathu chifukwa cholephera kuthaŵira kwa Yehova. Inde, “zikwi khumi” zagwa pa “dzanja lamanja” la Israyeli wauzimu lerolino. (Agalatiya 6:16) Koma kaya ndife Akristu odzozedwa kapena anzawo odzipatulira, ndife otetezeka “m’ngaka” ya Mulungu. ‘Tikungopenya ndi kuona kubwezera chilango oipa,’ amene akututa mavuto m’nkhani ya zamalonda, zachipembedzo, ndi m’nkhani zina.​—Agalatiya 6:7.

‘Palibe Choipa Chidzatigwera’

13. Kodi ndi zoipa ziti zimene sizimatigwera, ndipo chifukwa chiyani?

13 Ngakhale kuti chitetezo cha dziko lapansi lino chikuchepa, timaika Mulungu patsogolo ndi kudalira mawu a wamasalmo akuti: “Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothaŵirapo panga! Udaika Wam’mwambamwamba chokhalamo chako; palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.” (Salmo 91:9, 10) Inde, Yehova ndiye pothaŵirapo pathu. Komabe, Mulungu Wam’mwambamwamba ndiyenso ‘mokhalamo mwathu,’ mmene timasungika. Timatamanda Yehova monga Mfumu ya Chilengedwe chonse, ‘timakhala’ mwa iye monga Mtetezi, ndiponso timalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wake. (Mateyu 24:14) Motero, ‘palibe choipa chidzatigwera.’ Zoipa zonse zimene anazifotokoza kuchiyambi kwa Salmo limeneli sizidzatigwera. Ngakhale timavutika mofanana ndi anthu ena chifukwa cha zivomezi, mikuntho, madzi osefukira, njala, ndi nkhondo, zimenezi sizimawononga chikhulupiriro chathu kapena chitetezo chathu chauzimu.

14. N’chifukwa chiyani zolanga zakupha sizimatikhudza monga atumiki a Yehova?

14 Akristu odzozedwa ali ngati alendo ogonera m’mahema kutali ndi dongosolo la zinthu lino. (1 Petro 2:11) ‘Cholanga sichiyandikiza hema wawo.’ Kaya tikuyembekeza kudzapita kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi, sitili mbali ya dziko. Ndiponso zolanga zakupha mwauzimu za m’dzikoli monga chiwerewere, kukondetsa chuma, chipembedzo chonyenga, ndi kulambira “chilombo” ndi “fano” lake limene lili United Nations, sizimatikhudza.​—Chivumbulutso 9:20, 21; 13:1-18; Yohane 17:16.

15. Kodi angelo amatithandiza m’njira ziti?

15 Posimba za chitetezo chimene tili nacho, wamasalmo anawonjezera kuti: [Yehova] adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m’njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja awo, ungagunde phazi lako pamwala.” (Salmo 91:11, 12) Angelo apatsidwa mphamvu kuti atiteteze. (2 Mafumu 6:17; Salmo 34:7-9; 104:4; Mateyu 26:53; Luka 1:19) Amatisunga ‘m’njira zathu zonse.’ (Mateyu 18:10) Angelo amatitsogolera ndi kutisunga pamene tikulengeza za Ufumu ndipo sitikhumudwa mwauzimu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Ngakhale ‘miyala’ monga kuletsedwa kwa ntchito yathu sizinatichititse kukhumudwa ndi kutaya chiyanjo cha Mulungu.

16. Kodi kugwira kwa “msona wa mkango” kumasiyana bwanji ndi kuluma kwa “mphiri,” ndipo ife timachita bwanji akatiukira?

16 Wamasalmo anapitiriza kuti: “Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka.” (Salmo 91:13) Monga mmene msona wa mkango umagwira poyera, adani athu ena amatsutsa poyera mwa kupanga malamulo oletsa ntchito yathu yolalikira. Koma kuphatikiza pa kutsutsa kumeneku, amatilumanso modzidzimutsa monga mmene mphiri imalumira itabisala. Nthaŵi zina atsogoleri a zipembedzo amatiukira mwamseri kudzera mwa opanga malamulo, oweruza, ndi anthu ena. Koma mothandizidwa ndi Yehova, timathetsa mwamtendere zimenezi kudzera m’makhoti, motero ‘timateteza ndi kukhazikitsa mwalamulo uthenga wabwino.’​—Afilipi 1:7, NW; Salmo 94:14, 20-22.

17. Kodi timapondereza bwanji “msona wa mkango”?

17 Wamasalmo akufotokozanso za kupondereza “msona wa mkango ndi chinjoka.” Msona wa mkango ungakhale woopsa kwambiri, ndipo chinjoka chingakhale chilombo chokwaŵa chachikulu kwambiri. (Yesaya 31:4) Komabe, kaya msona wa mkangowo ndi woopsa motani pamene ukuukira poyera, mophiphiritsa timaupondereza mwa kumvera Mulungu m’malo momvera anthu ndi magulu onga mkango. (Machitidwe 5:29) Motero “mkango” woopsa sumativulaza mwauzimu.

18. Kodi “chinjoka” chikutikumbutsa za ndani, ndipo kodi tifunika kuchita chiyani chikamayesa kutikola?

18 “Chinjoka” chimene wamasalmoyo anatchula chikutikumbutsa za “chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana.” (Chivumbulutso 12:7-9; Genesis 3:15) Iye ali ngati chilombo chokwaŵa chachikulu kwambiri chomwe chingaphwanye ndi kumeza nyama imene chagwira. (Yeremiya 51:34) Satana amayesa kutikola, kutiphwanya ndi zovuta za m’dziko lapansi lino, ndi kutimeza. Koma tiyeni tichikanize ndi kuchipondereza “chinjoka” chimenechi. (1 Petro 5:8) Otsalira odzozedwa ayenera kuchita zimenezi kuti athe kukwaniritsa nawo Aroma 16:20.

Yehova Ndiye Gwero Lathu la Chipulumutso

19. N’chifukwa chiyani timathaŵira kwa Yehova?

19 Pofotokoza za wolambira woona, wamasalmo akuimira Mulungu pamene akuti: “Popeza andikondadi ndidzam’pulumutsa; ndidzam’kweza m’mwamba, popeza adziŵa dzina langa.” (Salmo 91:14) Mawuwo akuti “ndidzam’kweza m’mwamba” kwenikweni amatanthauza kuti “ndidzam’teteza,” kumuika pamalo osafikika. Timathaŵira kwa Yehova monga olambira ake makamaka chifukwa chakuti ‘timam’kondadi.’ (Marko 12:29, 30; 1 Yohane 4:19) Ndiyeno, Mulungu ‘amatipulumutsa’ kwa adani athu. Iwo sadzatiwononga. M’malo mwake, Mulungu adzatipulumutsa chifukwa timadziŵa dzina lake ndipo timaitanira pa dzinalo. (Aroma 10:11-13) Ndipotu tatsimikiza ‘kuyenda m’dzina la Yehova kunthaŵi yomka muyaya.’​—Mika 4:5; Yesaya 43:10-12.

20. Pomaliza Salmo 91, kodi Yehova akulonjeza chiyani kwa mtumiki wake wokhulupirika?

20 Pomaliza Salmo 91, Yehova akufotokoza za mtumiki wake wokhulupirika kuti: “Adzandifuulira Ine ndipo ndidzam’yankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzam’landitsa, ndi kum’chitira ulemu. Ndidzam’khutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.” (Salmo 91:15, 16) Tikapemphera kwa Mulungu mogwirizana ndi zimene iye amafuna, amatiyankha. (1 Yohane 5:13-15) Takumana kale ndi nsautso zambirimbiri zobwera chifukwa cha udani umene Satana amauyambitsa. Koma mawu akuti “kunsautso ndidzakhala naye pamodzi” amatikonzekeretsa kulimbana ndi mayesero amene angabwere m’tsogolo ndipo amatitsimikizira kuti Mulungu adzatipulumutsa powononga dziko lapansili.

21. Kodi odzozedwa alandira kale ulemerero motani?

21 Ngakhale kuti Satana akutsutsa mwaukali kwambiri, otsalira odzozedwa amene tili nawo adzakwezedwa kumwamba pa nthaŵi yoikika ya Yehova atakhala “masiku ambiri” padziko. Komabe, chipulumutso chachikulu cha Mulungu chabweretsa kale ulemerero wauzimu kwa odzozedwa. Ndipo ndi mwayi waukulutu kwambiri umene ali nawo wotsogolera monga Mboni za Yehova padziko lapansi masiku otsiriza ano. (Yesaya 43:10-12) Yehova adzapulumutsa anthu ake m’nkhondo yake yaikulu ya Armagedo pamene adzatsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuyeretsa dzina lake loyera.​—Salmo 83:18; Ezekieli 38:23; Chivumbulutso 16:14, 16.

22. Kodi ndani amene ‘adzaona chipulumutso cha Yehova’?

22 Kaya ndife Akristu odzozedwa kapena anzawo odzipatulira, tikuyembekeza Mulungu kuti atipulumutse. Amene akutumikira Mulungu mokhulupirika adzawapulumutsa “tsiku la Yehova lalikulu loopsa.” (Yoweli 2:30-32) Ife amene tidzakhala ena mwa “khamu lalikulu” limene lidzapulumuka kuloŵa m’dziko latsopano ndiponso amene tidzakhulupirikabe pa chiyeso chomaliza ‘adzatikhutitsa ndi masiku ambiri,’ womwe uli moyo wosatha. Adzaukitsanso anthu akufa miyandamiyanda. (Chivumbulutso 7:9; 20:7-15) Yehova adzasangalaladi ‘kutionetsa chipulumutso’ kudzera mwa Yesu Kristu. (Salmo 3:8) Popeza tili ndi chiyembekezo chachikulu chimenechi, tiyeni tipitirizebe kupempha Mulungu kuti atidziŵitse kuŵerenga masiku athu kuti tim’lemekeze. Tiyeni tipitirize kusonyeza kuti Yehova ndiye pothaŵirapo pathu mwa zimene timalankhula ndi zimene timachita.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Amene analemba Malemba Achigiriki Achikristu sanafotokoze kuti Salmo limeneli likunena za ulosi wa Mesiya. N’zoona kuti Yehova anali pothaŵirapo ndi linga kwa Yesu Kristu, monga mmene alili kwa otsatira a Yesu odzozedwa ndi anzawo amene adzipatulira kwa Mulungu monga gulu mu “nthaŵi ya chimaliziro” ino.​—Danieli 12:4.

Kodi Mungayankhe Motani?

• Kodi “ngaka yake ya Wam’mwambamwamba n’chiyani?

• N’chifukwa chiyani sitiopa?

• Kodi ndi motani mmene ‘choipa sichidzatigwera’?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndiye gwero lathu la chipulumutso?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi mukudziŵa mmene choonadi cha Yehova chilili chikopa chachikulu chotitchinjiriza?

[Zithunzi patsamba 18]

Yehova amathandiza atumiki ake kupitirizabe kuchita utumiki wawo ngakhale kuti anthu amatiukira modzidzimutsa kapena kutitsutsa poyera

[Mawu a Chithunzi]

Njoka: A. N. Jagannatha Rao, Trustee, Madras Snake Park Trust