Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Ndiye Pothaŵirapo Panga ndi Mphamvu Yanga

Yehova Ndiye Pothaŵirapo Panga ndi Mphamvu Yanga

Mbiri ya Moyo Wake

Yehova Ndiye Pothaŵirapo Panga ndi Mphamvu Yanga

YOSIMBIDWA NDI MARCEL FILTEAU

“Ngati ukwatiwa ndi amene uja, ndithudi udzaikidwa m’ndende.” Zimenezo ndi zimene anthu amauza mkazi amene ndimakonzekera kumukwatira. Ndiloleni ndifotokoze chifukwa chake anali kunena zinthu zotero.

PAMENE ndinabadwa mu 1927, chigawo cha Quebec, mu Canada chinali chimake cha Chikatolika. Pafupifupi zaka zinayi pambuyo pake, Cécile Dufour, mtumiki wanthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, anayamba kudzatichezera panyumba yathu mu mzinda wa Montreal. Pachifukwa chimenechi, anansi athu amamuopseza kaŵirikaŵiri. Ndiponso, anamangidwapo maulendo ambiri ndi kuchitidwa nkhanza chifukwa cholalikira uthenga wa Baibulo. Choncho tinaphunzira mwamsanga choonadi cha mawu a Yesu akuti: “Anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.”​—Mateyu 24:9.

Panthaŵiyi, ambiri ankaona ngati kuti n’kupanda nzeru kuti banja lachifalansa lokhala mu Canada lisiye chipembedzo cha Chikatolika. Ngakhale kuti makolo anga sanakhale Mboni zobatizidwa, anazindikira mwamsanga kuti ziphunzitso za Tchalitchi cha Katolika zinali zosagwirizana ndi Baibulo. Choncho analimbikitsa ana awo asanu ndi atatu kuti aziŵerenga mabuku ofalitsidwa ndi Mboni, ndipo anathandiza ana amene anaima kumbali ya choonadi cha Baibulo.

Kuimira Choonadi M’nthaŵi Zovuta

Mu 1942, ndikanali pasukulu, ndinayamba kukhala ndi chidwi chenicheni paphunziro la Baibulo. Panthawiyo ntchito za Mboni za Yehova zinali zoletsedwa mu Canada chifukwa chakuti iwo anali kutsatira chitsanzo cha Akristu oyambirira ndipo sanakhudzidwe nawo m’nkhondo za amitundu. (Yesaya 2:4; Mateyu 26:52) Mbale wanga wamkulu kwambiri, Roland anaikidwa mumsasa wachibalo chifukwa chokana kunyamula zida panthaŵi yomwe nkhondoyo imamenyedwa.

M’nthaŵi yomweyi, Abambo anandipatsa buku lachifalansa lomwe linafotokoza za kuzunzika kwa Mboni za ku Germany chifukwa chokana kuchirikiza magulu ankhondo a Adolph Hitler. * Zitsanzo zolimbikitsa chikhulupiriro zoterozo zinandisonkhezera kudzidziŵikitsa monga mmodzi wa iwo, ndipo ndinayamba kufika pamisonkhano ya Mboni za Yehova imene imachitika m’nyumba ya munthu wina. Posapita nthaŵi ndinapemphedwa kumatenga nawo mbali m’ntchito yolalikira. Ndinavomera pempholo ndikudziŵa bwino lomwe kuti ndingamangidwe ndiponso kuikidwa m’ndende.

Pambuyo popempherera mphamvu, ndinagogoda khomo langa loyamba. Mayi waulemu anayankha, ndipo nditadzidziŵikitsa, ndinamuŵerengera mawu a pa 2 Timoteo 3:16 akuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.”

“Kodi mungakonde kuphunzira zambiri ponena za Baibulo?” ndinam’funsa motero.

“Inde,” anayankha motero.

Choncho ndinamuuza kuti ndidzabwera ndi mnzanga amene amadziŵa bwino kwambiri Baibulo kusiyana ndi ine, zomwe ndinachitadi m’mlungu wotsatira. Pambuyo pa chochitika chimenecho ndinalimba mtima kwambiri, ndipo ndinazindikira kuti sitikutumikira m’mphamvu yathu. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, timatero ndi thandizo la Yehova. Ndithudi, m’pofunika kumazindikira kuti “ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife.”​—2 Akorinto 4:7.

Pambuyo pake, ntchito yolalikira inakhala mbali yokhazikika m’moyo wanga monganso momwe zinakhalira ndi kumangidwa ndi kuponyendwa m’ndende. M’posadabwitsa kuti msungwana amene ndimayembekezera kudzakwatirana nayeyo anauzidwa kuti, “Ngati ukwatiwa ndi amene uja, ndithudi udzaikidwa m’ndende”! Komabe zokumana nazo ngati zimenezo sizinali zovuta kwenikweni motero. Kaŵirikaŵiri titakhala usiku umodzi m’ndende timatulutsidwa pachikole ndi Mboni inzathu.

Zosankha Zofunika

Mu April 1943, ndinadzipatulira kwa Yehova ndipo ndinakusonyeza mwa ubatizo wa m’madzi. Kenako, mu August 1944, ndinakhala nawo koyamba pamsonkhano waukulu, mu Buffalo, New York, U.S.A., pafupi kwambiri ndi malire a dziko la Canada. Panali anthu 25,000, ndipo pologalamuyo inalimbikitsa chikhumbo changa cha kukhala mpainiya, malinga ndi momwe amadziŵikira atumiki anthaŵi zonse a Mboni za Yehova. Chiletso cha ntchito ya Mboni za Yehova m’Canada chinachotsedwa m’May 1945, ndipo m’mwezi wotsatira ndinayamba upainiya.

Komabe, pamene ndinali kupita patsogolo muutumiki, kutengeredwa kundende nakonso kunapita patsogolo. Ndinaikidwapo m’selo imodzi ndi Mike Miller, mtumiki wokhulupirika wa Yehova yemwe anatumikira kwa nthaŵi yaitali. Tinakhala pansi pasimenti n’kumacheza. Makambitsirano athu auzimuwo anandilimbikitsa kwabasi. Komabe, pambuyo pake, ndinadzifunsa m’mtima kuti, ‘Bwanji ngati pakanakhala kusamvana pakati pa ine ndi iye ndipo sitimayankhulana?’ Nthaŵi imene ndinakhala kundendeko ndi mbale wokondedwayo inandipatsa maphunziro abwino kwambiri m’moyo wanga​—timafunikira abale athu ndipo tiyenera kumakhululukirana ndi kukomerana mitima. Koma ngati sititero, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati mulumana ndi kudyana, chenjerani mungawonongane.”​—Agalatiya 5:15.

Mu September 1945, ndinaitanidwa kukatumikira pa ofesi yanthambi ya Watch Tower Society mu Toronto, Canada, yomwe timaitcha kuti Beteli. Pulogalamu yauzimu ya kumeneko inalidi yomangirira ndi yolimbitsa chikhulupiriro. Chaka chotsatira, ndinatumizidwa kukagwira ntchito ku munda wa Beteli, makilomita 40 kumpoto kwa ofesi ya nthambi. Pamene ndimatchola zipatso zamtundu wa mabulosi [malubeni] ndi msungwana wina wodziŵika ndi dzina lakuti Anne Wolynec, ndinazindikira osati kokha kukongola kwa maonekedwe komanso chikondi ndi changu chake pa Yehova. Tinayamba chibwenzi, ndipo tinakwatirana mu January 1947.

Kwa zaka ziŵiri ndi theka zotsatira, timachita upainiya mu London, Ontario, ndipo pambuyo pake pachisumbu cha Cape Breton, komwe tinathandiza kuyambitsa mpingo. Kenako, mu 1949, tinaitanidwa ku kalasi la 14 la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, komwe tinakaphunzitsidwa kukhala amishonale.

Ntchito Yaumishonale mu Quebec

Ophunzira ochokera ku Canada a makalasi a m’mbuyomo a Gileadi anali atatumizidwa kukatsegulira ntchito yolalikira mu Quebec. Mu 1950, ineyo ndi mkazi wanga pamodzi ndi ena 25 a kalasi lathu la 14 tinapita kukathandizana nawo. Kuwonjezeka kwa ntchito yaumishonale kunadzetsa chizunzo choopsa ndiponso kuchitidwa ziwawa ndi magulu a anthu, zosonkhezeredwa ndi atsogoleri a Tchalitchi cha Roma Katolika.

Masiku aŵiri pambuyo pofika m’dera lathu loyamba la ntchito yaumishonale mu mzinda wa Rouyn, Anne anamangidwa ndi kuponyedwa kumbuyo kwa galimoto lapolisi. Chimenechi chinali chokumana nacho chachilendo kwa iye, chifukwa chakuti amachokera m’mudzi waung’ono wa m’chigawo cha Manitoba, mu Canada, kumene wapolisi sanali kuonekeraonekera. Mwachibadwa, anachita mantha kwambiri ndipo anakumbukira mawu aja akuti, “Ngati ukwatiwa ndi amene uja, ndithudi udzaikidwa m’ndende.” Koma, asanachoke, apolisi anandipeza nanenso ndi kundiponya m’galimotomo pamodzi ndi Anne. “Ndakondwa kukuonani!” iye anadzuma motero. Komabe, modabwitsa kwambiri iye anakhazika mtima pansi, akumanena kuti, “Ayi, popeza kuti zinthu zofananazi zinachitikiranso atumwi chifukwa cholalikira za Yesu.” (Machitidwe 4:1-3; 5:17, 18) Pambuyo pake tsiku lomwelo tinamasulidwa pachikole.

Patangopita chaka chimodzi pambuyo pachochitika chimenechi, ndili mu utumiki wa khomo ndi khomo m’dera lathu latsopano ku Montreal, ndinamva phokoso mu msewu ndipo ndinaona kagulu ka anthu okwiya kakugenda. Apolisi anafika pamalopo panthaŵi yomwe ndimapita kuti ndikathandize Anne ndi mnzake. M’malo momanga anthu a m’kagulu kachiwawako, apolisi anamanga Anne ndi mnzakeyo! Ali m’ndende Anne anakumbutsa Mboni yatsopanoyo kuti akukumana ndi zoona zake zenizeni za mawu a Yesu akuti: “Adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa.”​—Mateyu 10:22.

Panthaŵi ina, mu Quebec munali milandu yokwana 1,700 ya Mboni za Yehova imene imayembekezera kuzengedwa. Nthaŵi zambiri, tinali kuimbidwa mlandu wa kugaŵira mabuku ogalukira boma kapena wa kugaŵira mabuku opanda chilolezo. Chotsatirapo chake chinali chakuti, Dipatimenti ya za Malamulo ya Watch Tower Society inachitapo kanthu ku boma la Quebec. Pambuyo pa zaka zambiri zolimbana ndi akhoti, Yehova anatipatsa zipambano ziŵiri mu Bwalo Lapamwamba la Canada. Mu December, mlandu wathu wakuti mabuku athu n’ngogalukira boma unatha, ndipo mu October 1953, ufulu wathu wa kugaŵira mabuku popanda chilolezo unachirikizidwa. Choncho tinaona bwino lomwe mmene Yehova alidi “pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.”​—Salmo 46:1.

Ndithudi, chiŵerengero cha Mboni mu Quebec chawonjezeka kuchoka pa 356 mu 1945, nthaŵi yomwe ndinayamba upainiya, ndi kupitirira 24,000 lerolino! Zachitikadi monga momwe ulosi wa Baibulo unaneneratu kuti: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa.”​—Yesaya 54:17.

Ntchito Yathu mu France

Mu September 1959, ine ndi Anne tinaitanidwa kukatumikira pa Beteli mu Paris ku France, kumene ndinagaŵiridwa ntchito yoyang’anira ntchito yosindikiza. Kufikira pamene tinafika mu January 1960, ntchito yosindika imachitidwa ndi gulu lina lazamalonda. Popeza kuti Nsanja ya Olonda inali yoletsedwa mu France panthaŵiyo, timasindikiza magaziniyi mwezi uliwonse monga kabuku ka masamba 64. Kabukuko kamatchedwa kuti The Interior Bulletin of Jehovah’s Witnesses, (Nkhani za Pakati pa Mboni za Yehova) ndipo kamakhala ndi nkhani zoti ziphunziridwe m’mipingo m’kati mwa mweziwo. Kuchokera mu 1960 ndi kufika mu 1967, chiŵerengero cha ochita nawo ntchito yolalikira mu France chinawonjezeka kuchoka pa 15,439 n’kufika pa 26,250.

M’kupita kwa nthaŵi, amishonale ambiri anadzawatumiza ku madera ena, ena ku mayiko oyankhula Chifalansa a mu Africa ndi ena kubwerera ku Quebec. Popeza kuti Anne anali kudwala ndipo amafunikira opaleshoni, tinabwerera ku Quebec. Pambuyo polandira thandizo la mankhwala kwa zaka zitatu, thanzi la Anne linabwezeretsedwa. Kenako ndinatumizidwa m’ntchito yadera, kuchezera mpingo umodzi mlungu uliwonse kukaulimbikitsa mwauzimu.

Ntchito Yaumishonale mu Africa

Zaka zingapo pambuyo pake, mu 1981, tinasangalala kulandira ntchito yatsopano yaumishonale ku Zaire, tsopano kotchedwa kuti Democratic Republic of Congo. Anthu kumeneko anali osauka ndipo anali ndi mavuto ambiri. Pamene timafika, kunali Mboni 25,753, koma tsopano chiŵerengero chimenecho chawonjezeka mpaka kupitirira pa 113,000, ndipo anthu 446,362 anachita nawo mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Kristu mu 1999!

Mu 1984 boma linatilola kukhala ndi mahekitala ngati 200 oti timangepo ofesi yatsopano yanthambi. Kenako, mu December 1985 msonkhano wa mayiko unachitika mu Kinshasa, lomwe ndi likulu la dzikoli, ndipo nthumwi 32,000 zinasonkhana kuchokera ku madera ambiri a dziko lapansi. Pambuyo pa msonkhanowo, chitsutso chosonkhezeredwa ndi atsogoleri a chipembedzo chinasokoneza ntchito yathu mu Zaire. Pa March 12, 1986, abale amaudindo analandira kalata yomwe inafotokoza kuti bungwe la Mboni za Yehova la mu Zaire ndi loletsedwa. Chiletso cha ntchito zathu zonse chimenechi chinasainidwa ndi pulezidenti wadzikoli panthaŵiyo, malemu Mobutu Sese Seko.

Chifukwa cha zochitika mwadzidzidzi zimenezo, tinafunikira kutsatira uphungu wa Baibulo wakuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Tinapeza njira zopezera mapepala, inki, filimu, zipangizo zosindikizira, ndi mankhwala kuchokera kunja kwa dzikoli kuti tizisindikiza zofalitsa zathu mu Kinshasa. Tinapezanso njira yathu yogaŵirira zofalitsazo. Titalinganiza zinthu bwinobwino, njira yathu inagwira ntchito bwino kwambiri kusiyana ndi njira zotumizira makalata za a mtengatenga a boma!

Mboni zambiri zinamangidwa, ndipo zambiri zinazunzidwa mwankhanza. Komabe, ambiri anapirira nkhanza zoterozo ndipo anakhalabe okhulupirika. Nanenso ndinamangidwapo ndipo ndinaona mkhalidwe wovuta wa kundende womwe abale analimo. Nthaŵi zambiri timasautsidwa paliponse ndi gulu la apolisi akabisalira komanso akuluakulu aboma, koma Yehova amatipulumutsa nthaŵi zonse.​—2 Akorinto 4:8.

Tinabisa makatoni a mabuku okwana 3,000 m’nyumba yosungira katundu ya mkulu wina wamalonda. Koma, m’kupita kwa nthaŵi, mmodzi wa antchito ake anadziŵitsa gulu la apolisi akabisalira, ndipo apolisiwo anagwira wamalondayo. Pamene amapita kundende, mwamwayi anakumana nane ndili m’galimoto yanga. Wamalondayo anawauza kuti ndiineyo amene ndinapanga naye makonzedwe osunga mabukuwo. Apolisiwo anaima n’kundifunsa za zimenezo, akumandiimba mlandu woika mabuku oletsedwa m’nyumba yosungira katundu ya mkuluyo.

“Kodi muli ndi limodzi la mabukuwo?” ndinafunsa motero.

“Inde,” anayankha motero.

“Ndingalione?” ndinawapempha.

Anandipatsa kope limodzi, ndipo ndinawasonyeza tsamba lam’kati, lomwe limati: “Losindikizidwa ku United States of America ndi Watch Tower Bible & Tract Society.”

Ndinawakumbutsa kuti: “Chinthu chimene mwagwira m’manja mwanucho ndi cha ku America ndipo si cha mu Zaire.” “Boma lanu laletsa bungwe lalamulo la gulu la Mboni za Yehova la mu Zaire osati Watch Tower Bible & Tract Society ya ku United States. Choncho muyenera kusamala kwambiri ndi zomwe muti muchite ndi zofalitsa zimenezi.”

Ndinaloledwa kupita chifukwa chakuti analibe chilolezo cha khoti chomwe akanatha kundimangira. Madzulo a tsiku limenelo, tinapita ndi galimoto zikuluzikulu ziŵiri kunyumba yosungira katunduko ndi kuchotsa mabuku onsewo. Pamene akuluakulu aboma anabwera tsiku lotsatira, anadabwa kwambiri kupeza kuti pamalopo palibe kanthu. Nthaŵiyi tsopano anali kundifuna chifukwa anali ndi chilolezo cha khoti choti andimangire. Anandipeza, ndipo pachifukwa chakuti analibe galimoto, ndinayendetsa galimoto yanga kupita ku ndende! Mboni ina inandiperekeza kuti ikatenge galimoto yangayo asanailande.

Pambuyo pa kufunsidwa kwa maola asanu ndi atatu, analingalira zondipitikitsa m’dzikolo. Koma ndinawasonyeza kope la kalata yochokera ku boma yotsimikizira kuti ndaloledwa kugulitsa zinthu za gulu la Mboni za Yehova la mu Zaire lomwe panthaŵiyi linali lotsekedwa. Choncho ndinaloledwa kupitiriza ntchito yanga pa Beteli.

Pambuyo pa zaka zinayi za kutumikira movutika chifukwa cha kuletsedwa kwa ntchitoyi mu Zaire, ndinadwala zilonda za m’mimba zomwe zinaika moyo wanga pangozi. Panakonzedwa zoti ndipite kukapeza thandizo la mankhwala ku South Africa, komwe ndinakasamaliridwa ndi nthambi ya kumeneko ndipo ndinachira. Nditatumikira kwa zaka zisanu ndi zitatu mu Zaire, zomwe ndithudi n’zosaiŵalika ndiponso n’chokumana nacho chosangalatsa, tinasamukira ku nthambi ya South Africa mu 1989. Mu 1998 tinabwerera kwathu ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo takhala tikutumikiranso pa Beteli ya Canada.

Wosangalala Chifukwa Chotumikira

Pamene ndilingalira zaka zanga 54 za muutumiki wanthaŵi zonse, ndimasangalala kwambiri chifukwa ndinagwiritsa ntchito unyamata wanga muutumiki wa mtengo wapatali wa Yehova. Ngakhale kuti Anne wapirira mikhalidwe yovuta, iye sanadandaulepo koma wakhala akuchirikiza kwambiri m’ntchito zathu zonse. Tonse aŵiri, takhala ndi mwayi wothandiza anthu ambiri kudziŵa Yehova, omwe ambiri mwa iwo ali muutumiki wa nthaŵi zonse tsopano. Zimapatsa chimwemwe chachikulu kuona ena mwa ana awo ngakhalenso zidzukulu zawo akutumikira Mulungu wathu wamkulu, Yehova!

Ndatsimikiza kuti palibe chinthu chilichonse cha m’dziko ili chomwe chingafanane ndi mwayi komanso madalitso amene Yehova watipatsa. Zoonadi, tapilira mayesero ambiri, koma mayeserowo atithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso chidaliro chathu pa Yehova. Iye wakhaladi nsanja yamphamvu, pothaŵirapo, ndi thandizo lopezekeratu m’masautso.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Buku limeneli linasindikizidwa poyambirira m’Chijeremani, Kreuzzug gegen das Christentum (Crusade Against Christianity). Linatembenuzidwira m’Chifalansa ndi m’Chipolishi koma osati m’Chingelezi.

[Zithunzi patsamba 26]

Kuchitira limodzi upainiya mu 1947; ndi Anne lerolino

[Chithunzi patsamba 29]

Anthu a ku Zaire amene tinakumana nawo anakonda choonadi cha Baibulo