Kusangalala mwa Mulungu wa Chipulumutso Chathu
Kusangalala mwa Mulungu wa Chipulumutso Chathu
“Ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.”—HABAKUKU 3:18.
1. Kodi Danieli anaona masomphenya okhudza chiyani Babulo asanagwe m’chaka cha 539 B.C.E.?
ZAKA zoposa khumi Babulo asanagwe m’chaka cha 539 B.C.E., mneneri wokalambayo Danieli anaona masomphenya ochititsa mantha. Analosera za zochitika padziko lapansi zimene zinapitirizabe mpaka kufika pachimake pa nkhondo ya pakati pa adani a Yehova ndi Mfumu Yake yoikidwa, Yesu Kristu. Kodi Danieli anachita chiyani? Iye anati: “Ndinakomoka . . . ndipo ndinadabwa nawo masomphenyawo.”—Danieli 8:27.
2. Kodi Danieli anaona nkhondo yotani m’masomphenya, ndipo kodi mukumva bwanji chifukwa cha kuyandikira kwakeko?
2 Nanga bwanji ifeyo? Tili kufupi kwambiri ndi kumapeto kwa nthaŵiyo! Kodi timachitanji pamene tizindikira kuti kulimbana kumene Danieli anaona m’masomphenya, nkhondo ya Mulungu ya Armagedo, kuli pafupi kwambiri? Kodi timachita motani pamene tizindikira kuti kuipa kovumbulidwa mu ulosi wa Habakuku kwafalikira kwambiri kotero kuti chiwonongeko cha adani a Mulungu chili chosapeŵeka? Mwachionekere, malingaliro athu amafanana ndi a Habakuku iye mwiniyo, monga momwe alongosoledwera mu chaputala chachitatu cha buku lake laulosi.
Habakuku Apempherera Chifundo cha Mulungu
3. Kodi Habakuku akupemphera m’malo mwa yani, ndipo kodi mawu akewo ayenera kutikhudza motani?
3 Habakuku chaputala 3 ndi pemphero. Malinga ndi vesi 1, pempherolo likuimbidwa monga Sigionoto, nyimbo yachisoni kapena yamaliro. Pemphero la mneneriyu likuperekedwa mokhala ngati akunena za iye mwini. Koma kwenikweni, Habakuku akulankhula m’malo mwa mtundu wosankhidwa wa Mulungu. Lerolino, pemphero lakelo lili ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu a Mulungu, omwe atanganidwa ndi ntchito yolalikira Ufumu. Pamene tiŵerenga Habakuku chaputala 3 tikulingalira zimenezi, mawu ake amatichititsa mantha komanso amatipatsa chimwemwe. Pemphero la Habakuku, kapena kuti nyimbo ya maliro, limatipatsa chifukwa champhamvu chokhalira achimwemwe mwa Yehova, Mulungu wa chipulumutso chathu.
4. N’chifukwa chiyani Habakuku anaopa, ndipo kodi tiyenera kukhala otsimikizira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito mphamvu yake motani?
4 Monga momwe taonera m’nkhani ziŵiri zapitazo, mikhalidwe inali yoipa kwambiri m’dziko la Yuda m’nthaŵi ya Habakuku. Koma Mulungu sanakalola mkhalidwewu kupitirizabe. Yehova anali kudzachitapo kanthu kena monga momwe anachitira m’mbuyomo. N’chifukwa chaketu mneneriyu anafuula kuti: “Yehova, ndinamva mbiri yanu. Ndichita mantha, Yehova, ndi ntchito yanu”! (NW) Kodi iye anatanthauzanji? ‘Mbiri ya Yehova’ inali mbiri yolembedwa ya zochita zamphamvu za Mulungu, monga za pa Nyanja Yofiira, m’chipululu, ndi pa Yeriko. Zochitika zimenezi Habakuku anali kuzidziŵa bwino, ndipo zinali kumuchititsa mantha chifukwa anadziŵa kuti Yehova adzagwiritsanso ntchito mphamvu yake yaikuluyo polimbana ndi adani ake. Pamene tiona kuipa kwa mtundu wa anthu lerolino, ifenso timadziŵa kuti Yehova adzachitapo kanthu monga momwe anachitira m’masiku akale. Kodi zimenezi zimatipangitsa kukhala amantha? Inde! Komabe, timapemphera monga momwe Habakuku anachitira pamene anati: “Tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziŵitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.” (Habakuku 3:2) M’nthaŵi yoikika ya Mulungu, “pakati pa zaka,” agwiritsetu ntchito mphamvu yake yodabwitsa. Ndipo panthaŵiyo, akumbuketu kusonyeza chifundo kwa awo amene amamukonda!
Yehova Aguba!
5. Kodi m’motani momwe ‘Mulungu anafumira ku Temani,’ ndipo kodi zimenezi zikusonyeza chiyani polingalira za Armagedo?
5 Kodi n’chiyani chomwe chidzachitika pamene Yehova amva kupempha kwathu chifundo? Timapeza yankho lake pa Habakuku 3:3, 4. Choyamba, mneneriyu akuti: “Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo ku phiri la Parana.” Kumbuyoko m’nthaŵi ya mneneri Mose, Temani ndi Parana anali panjira ya m’chipululu imene Aisrayeli anadzera popita ku Kanani. Pamene mtundu waukuluwo wa Israyeli unali kuyendabe, Yehova iye mwini anali kuoneka kuti anali kuyenda, ndipo panalibe chimene chikanamuimitsa. Mose atatsala pang’ono kumwalira, anati: “Yehova anafuma ku Sinai, nawatulukira ku Seiri; anaoneka wowala pa phiri la Parana, anafumira kwa [angelo] opatulika zikwizikwi.” (Deuteronomo 33:2) Pamene Yehova adzayang’anizana ndi adani ake pa Armagedo, kudzakhala kusonyeza kofananako kwa mphamvu zake zosagonjetseka.
6. Kuwonjezera pa ulemerero wa Mulungu, kodi Akristu ozindikira amaonanso chiyani?
6 Habakuku ananenanso kuti: “Ulemerero wa [Yehova] unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumulemekeza. Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika.” Ndi maonekedwe ochititsatu kaso kwambiri! Inde, anthu sangamuyang’ane Yehova Mulungu ndi kukhala ndi moyo. (Eksodo 33:20) Komabe, atumiki okhulupirika a Mulungu, maso a mitima yawo amathobwedwa pamene asinkhasinkha za ukulu wake. (Aefeso 1:18) Ndipo Akristu ozindikira amaonanso chinachake kuwonjezera pa ulemerero wa Yehova. Habakuku 3:4 likumaliza ndi kuti: “Anali nayo mitsitsi ya dzuŵa yotuluka m’dzanja lake. Ndi komweko kunabisika mphamvu yake.” Inde, timaona kuti Yehova ndi wokonzeka kuchitapo kanthu, kugwiritsa ntchito dzanja lake lamanja lamphamvu ndi lanyonga.
7. Kodi kuguba kwa chipambano kwa Mulungu kukutanthauzanji kwa awo amene akumupandukira?
7 Kuguba kwa chipambano kwa Mulungu kukutanthauza tsoka kwa omupandukira. Habakuku 3:5 akuti: “Patsogolo pake panapita mliri, ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.” Pamene Aisrayeli anali pafupi ndi malire a Dziko Lolonjezedwa m’chaka cha 1473 B.C.E., ambiri a iwo anapanduka ndipo ankachita chisembwere ndi kulambira mafano. Chotsatira chake chinali chakuti anthu oposa 20,000 anafa ndi mliri umene Mulungu anatumiza. (Numeri 25:1-9) Posachedwapa, pamene Yehova adzaguba kumka ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” amene akumupandukira adzalangidwanso mofananamo chifukwa cha machimo awo. Ena angadzafenso ndi mliri weniweni.—Chivumbulutso 16:14, 16.
8. Malinga ndi Habakuku 3:6, kodi adani a Mulungu akuyembekezera kukumana ndi zotani?
8 Tsopano tamverani mmene mneneriyu akulongosolera mwamphamvu Yehova wamakamu ali pa ntchito. Pa Habakuku 3:6 timaŵerenga kuti: “[Yehova Mulungu] anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinaŵerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.” Choyamba, Yehova ‘akuimirira,’ monga ngati mkulu wa asilikali akuyang’ana bwalo lomenyerapo nkhondo. Adani ake akunjenjemera ndi mantha. Akuona yemwe mdani wawo ali ndipo akuopa, akulumphalumpha posokonezeka maganizo. Yesu ananeneratu za nthaŵi pamene, “mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa.” (Mateyu 24:30) Iwo adzazindikira mochedwa kwambiri kuti palibe amene angaime motsutsana ndi Yehova. Mabungwe a anthu, ngakhale aja amene akuoneka kuti sadzatha monga ngati “mapiri achikhalire” ndi “zitunda zakale lomwe,” adzanyenyeka. Zidzakhala ngati ‘mayendedwe a kale lomwe’ a Mulungu, monga momwe anachitira m’nthaŵi zakale.
9, 10. Kodi Habakuku 3:7-11 akutikumbutsa chiyani?
9 “Mkwiyo” wa Yehova pa adani ake wakula zedi. Koma kodi iye adzagwiritsa ntchito zida ziti m’nkhondo yake yaikuluyo? Mvetserani pamene mneneriyu akuzilongosola, iye akuti: “Munapombosola uta wanu; malumbiro analumbirira mafuko anali mawu oona. Munang’amba dziko lapansi ndi mitsinje. Mapiri anakuonani, namva zoŵaŵa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mawu ake, nakweza manja ake m’mwamba. Dzuŵa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwawo; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung’anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.”—Habakuku 3:7-11.
10 M’masiku a Yoswa, Yehova anachititsa dzuŵa ndi mwezi kuima pa chisonyezero chodabwitsa cha mphamvu. (Yoswa 10:12-14) Ulosi wa Habakuku ukutikumbutsa kuti Yehova adzagwiritsa ntchito mphamvu imodzimodziyi pa Armagedo. M’chaka cha 1513 B.C.E.,Yehova anasonyeza kuti akhoza kulamulira madzi akuya pamene anagwiritsa ntchito Nyanja Yofiira kuwononga ankhondo a Farao. Zaka makumi anayi pambuyo pake, mtsinje wa Yordano wosefukirawo sunathe kuletsa Aisrayeli kuguba mwachipambano kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Yoswa 3:15-17) M’masiku a mneneri wamkazi Debora, mvula yamphamvu inakokolola magareta a Sisera mdani wa Israyeli. (Oweruza 5:21) Yehova adzakhalabe ndi mphamvu zofananazi za madzi osefukira, mvula yamphamvu, ndi madzi akuya pa Armagedo. Mabingu ndi mphezi zilinso m’manja mwake, monga nthungo kapena phodo lodzala ndi mivi.
11. N’chiyani chomwe chidzachitika pamene Yehova adzamasula mphamvu zake zazikulu?
11 Ndithudi, zidzakhala zochititsa mantha pamene Yehova adzamasula mphamvu zake zazikulu. Mawu a Habakuku akusonyeza kuti usiku udzasanduka masana ndipo masana adzakhala owala kwambiri kuposa mmene dzuŵa lingawalitsire. Kaya mafotokozedwe a Armagedo aulosi wouziridwa ameneŵa ndi enieni kapena ophiphiritsa, chinthu chimodzi chili chotsimikizirika, ndicho chakuti Yehova adzapambana, sadzalola mdani aliyense kuthaŵa.
Chipulumutso N’chotsimikizirika kwa Anthu a Mulungu!
12. Kodi Mulungu adzachitanji kwa adani ake, koma ndani omwe adzapulumutsidwe?
12 Mneneriyu akupitiriza kulongosola mmene Yehova akuwonongera adani Ake. Pa Habakuku 3:12, tikuŵerenga kuti: “Munaponda dziko ndi kulunda, munapuntha amitundu ndi mkwiyo.” Komabe, sikuti Yehova adzawononga mwachisawawa. Anthu ena adzapulumutsidwa. Habakuku 3:13 akuti: “Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu.” Inde, Yehova adzapulumutsa atumiki ake odzozedwa okhulupirika. Ndiyeno kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa chipembedzo chonyenga, kudzamalizidwa. Komabe, lerolino mitundu ikuyesa kufafaniza kulambira koyera. Posachedwa, atumiki a Yehova adzaukiridwa ndi magulu a ankhondo a Gogi wa ku Magogi. (Ezekieli 38:1–39:13; Chivumbulutso 17:1-5, 16-18) Kodi adzapambana pa kuukira kwa usatana kumeneko? Iyayi! Ndiyeno Yehova mwaukali adzapuntha adani ake, kuwapondaponda ndi mapazi kukhala ngati akupuntha zinthu zakumunda pabwalo lopunthira. Koma adzapulumutsa aja amene amamulambira mumzimu ndi m’choonadi.—Yohane 4:24.
13. Kodi Habakuku 3:13 adzakwaniritsidwa motani?
13 Chiwonongeko chotheratu cha oipa chaloseredwa m’mawu aŵa: “Munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m’khosi.” (Habakuku 3:13) “Nyumba” imeneyi ndi dongosolo loipa lobwera mosonkhezeredwa ndi Satana Mdyerekezi. Idzaphwasulidwa. “Mutu,” kapena kuti otsogolera kutsutsa Mulungu, adzaphwanyidwa. Dongosolo lonse lidzawonongedwa, mpaka pa maziko ake. Silidzakhalakonso. Udzakhalatu mpumulo waukulu kwabasi umenewo!
14-16. Malinga ndi Habakuku 3:14, 15, kodi n’chiyani chomwe chidzachitikire anthu a Yehova komanso adani awo?
14 Pa Armagedo, awo amene akuyesa kuwononga “odzozedwa” a Yehova adzasokonezedwa maganizo. Malinga ndi Habakuku 3:14, 15, mneneriyu akulankhula ndi Mulungu kuti: “Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kavumvulu kundimwaza; kukondwerera kwawo kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika. Munaponda panyanja ndi akavalo anu, madzi amphamvu anaunjikana mulu.”
15 Pamene Habakuku akunena kuti “ankhondo . . . anadza ngati kavumvulu kundimwaza,” mneneriyu akunena za atumiki odzozedwa a Yehova. Monga anthu achifwamba odikirira anzawo panjira, mitundu idzadumphira pa olambira a Yehova kuti iwawononge. Adani a Mulungu ndi a anthu ake ameneŵa ‘adzakondwera,’ poyesa
kuti apambana. Akristu okhulupirika adzaoneka ofooka, monga ngati “ozunzika.” Koma pamene magulu otsutsa Mulungu adzaukira, Yehova adzawapangitsa kuti adziponyere zida zawo zomwe. Adzagwiritsa ntchito zida zawo, kapena “maluti,” kumenyera ankhondo awo omwe.16 Komanso pali zambiri zomwe zidzachitika. Yehova adzagwiritsa ntchito magulu auzimu, amphamvu zoposa za anthu kumalizitsa kuwononga adani akewo. Ndi “akavalo” a ankhondo ake a kumwamba otsogozedwa ndi Yesu Kristu, iye adzapitabe patsogolo mwachipambano kudutsa “panyanja” ndi ‘pamadzi amphamvu ounjikana mulu,’ ndiko kuti, chiŵerengero chomawonjezereka cha anthu achidani. (Chivumbulutso 19:11-21) Ndiyeno oipa adzachotsedwa padziko lapansi. Mphamvu za Mulungu ndi chilungamo chake zidzasonyezedwatu mwamphamvu kwambiri!
Tsiku la Yehova Likudza!
17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro pa kukwaniritsidwa kwa mawu a Habakuku? (b) M’motani momwe tingakhalire ngati Habakuku pamene tikudikira tsiku lalikulu la Yehova?
17 Tingakhale otsimikiza kuti mawu a Habakuku adzakwaniritsidwa posachedwa. Sadzachedwa. Kodi inu mumachita motani podziŵiratu zimenezi? Kumbukirani kuti Habakuku anali kulemba mouziridwa ndi Mulungu. Yehova adzachitapo kanthu, ndipo padzakhala chipwirikiti Habakuku 3:16) Habakuku ananjenjemera kwambiri, ndipotu m’pomvekadi. Koma kodi chikhulupiriro chake chinagwedezeka? Kutalitali! Anali wofunitsitsa kuyembekezera mofatsa tsiku lalikulu la Yehova. (2 Petro 3:11, 12) Kodi ifeyo sitilinso ndi maganizo omwewo? Ndithudi tili nawo! Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti ulosi wa Habakuku udzakwaniritsidwa. Komano, tidikirabe mofatsa kufikira utakwaniritsidwa.
padziko lapansi pamene zimenezi zichitika. M’posadabwitsa kuti mneneriyu analemba kuti: “Ndinamva, ndi m’mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamawu, m’mafupa mwanga mudaloŵa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m’malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nawo ndi makamu.” (18. Ngakhale kuli kwakuti Habakuku anayembekezera mavuto, kodi anali ndi malingaliro otani?
18 Nthaŵi zonse nkhondo imabweretsa mavuto, ngakhalenso kwa amene pomalizira pake amapambana. Chakudya chingathe. Katundu angawonongeke. Moyo wa anthu ungakhale wovuta kwambiri. Ngati zimenezi zitatichitikira, kodi tidzatani? Malingaliro a Habakuku anali chitsanzo chabwino, pakuti iye anati: “Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m’minda m’mosapatsa chakudya; ndi zoŵeta zachotsedwa kukhola, palibenso ng’ombe m’makola mwawo; koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.” (Habakuku 3:17, 18) Moyenerera Habakuku anayembekezera mavuto, mwinamwake njala. Koma iye sanaleke kusangalala mwa Yehova, mwa amene anapeza chipulumutso.
19. Ndi mavuto otani amene Akristu ambiri akukumana nawo, koma kodi tingakhale otsimikizira za chiyani ngati tiika Yehova patsogolo m’miyoyo yathu?
19 Lerolino, ngakhale pamene nkhondo ya Yehova yolimbana ndi oipa isanachitike, anthu ambiri akuvutika ndi mavuto adzaoneni. Yesu ananeneratu kuti nkhondo, njala, zivomezi, ndi miliri zidzakhala mbali ya ‘chizindikiro cha kukhalapo kwake’ m’mphamvu ya Ufumu. (Mateyu 24:3-14; Luka 21:10, 11) Abale athu ambirimbiri akukhala m’mayiko amene akuvutika kwambiri ndi kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu, ndipo zimenezi zikuwadzetsera mavuto aakulu kwambiri. Akristu ena mwina angadzavutikenso mofananamo m’tsogolo. Kwa ambiri a ife, ndi zotheka kwambiri kuti ‘mkuyu sudzaphuka’ chimaliziro chisanadze. Komabe, tikudziŵa chifukwa chake zinthu zimenezi zikuchitika, ndipo zimenezi zimatipatsa nyonga. Ndiponso, tikuchirikizidwa. Yesu analonjeza kuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Zimenezi sizitsimikizira moyo wofeŵa, koma zimatitsimikizira kuti ngati tiika Yehova patsogolo, iye adzatiyang’anira.—Salmo 37:25.
20. Mosasamala kanthu za mavuto a kanthaŵi kochepaŵa, kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?
20 Ngakhale tikumane ndi mavuto alionse a kanthaŵi kochepa, sitidzataya chikhulupiriro m’mphamvu yopulumutsa ya Yehova. Abale ndi alongo athu ochuluka mu Afirika, Eastern Europe, ndi malo enanso akukumana ndi mavuto adzaoneni, koma akupitirizabe ‘kukondwera mwa Yehova.’ Mofanana ndi iwowo, tisaleketu kuchita zofananazo. Kumbukirani kuti Ambuye Mfumu Yehova ali Gwero lathu la “mphamvu.” (Habakuku 3:19) Sadzalephera kutithandiza. Armagedo ikubweradi, ndipo tili otsimikizira kuti dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu lidzatsatiradi. (2 Petro 3:13) Ndiyeno, “dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja.” (Habakuku 2:14) Mpaka nthaŵi yosangalatsa imeneyo, tiyeni titsanzire chitsanzo chabwino cha Habakuku. Tiyeni tisekere mwa Mulungu wa chipulumutso chathu’ nthaŵi zonse.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi pemphero la Habakuku lingatikhudze motani?
• N’chifukwa chiyani Yehova akuguba?
• Kodi ulosi wa Habakuku ukunenanji pa za chipulumutso?
• Kodi tiyenera kuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova ndi malingaliro otani?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 23]
Kodi mukudziŵa zinthu zomwe Mulungu adzagwiritsa ntchito powononga oipa pa Armagedo?