Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kukhalabe Maso’?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera ‘Kukhalabe Maso’?

“Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.”—MAT. 24:42.

NYIMBO: 136, 129

1. Perekani chitsanzo chosonyeza zimene zingachitike ngati munthu sakukhala maso ndi zimene zikuchitika. (Onani chithunzi pamwambapa.)

TIYEREKEZE kuti muli pamsonkhano ndipo pulogalamu yatsala pang’ono kuyamba. Tcheyamani akupita kupulatifomu n’kunena mawu amalonje. Kenako nyimbo zikuyamba ndipo anthu akukhala m’malo awo n’kumamvetsera nyimbozo. Izi zikuwathandiza kuti akonzekere kumvetsera nkhani za pamsonkhanowu. Koma pali ena amene sanazindikire n’komwe kuti tcheyamani wapita kupulatifomu ndipo nyimbo zayamba. Choncho akungopitirizabe kucheza kapena kuyendayenda. Chitsanzochi chikusonyeza kuti munthu akapanda kukhala maso, sazindikira zimene zikuchitika. Tingaphunzire zambiri pamenepa chifukwa posachedwapa pachitika zinthu zoopsa ndipo tiyenera kukonzekera. Kodi chichitike ndi chiyani?

2. N’chifukwa chiyani Yesu anauza ophunzira ake kuti ‘akhale maso’?

2 Pamene Yesu Khristu ankauza ophunzira ake za “mapeto a nthawi ino,” anawapatsa malangizo akuti: “Khalani maso, khalani tcheru, pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.” Kenako anawauzanso mobwerezabwereza kuti: “Khalani maso.” (Mat. 24:3; werengani Maliko 13:32-37.) Zimene Mateyu analemba pa nkhani yomweyi zimasonyezanso kuti Yesu anachenjeza ophunzira akewo kuti akhale tcheru. Anawauza kuti: “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere. . . . Pa chifukwa chimenechi, nanunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzabwera.” Ndiyeno ananenanso kuti: “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—Mateyu 24:42-44; 25:13.

3. N’chifukwa chiyani timamvera malangizo a Yesu oti tikhale maso?

3 A Mboni za Yehovafe timaona kuti malangizo a Yesuwa ndi ofunika kwambiri. Tikudziwa kuti tili “nthawi yamapeto” yeniyeni ndipo “chisautso chachikulu” chikhoza kuyamba nthawi iliyonse. (Dan. 12:4; Mat. 24:21) Panopa uthenga wa Ufumu ukulalikidwa padziko lonse. Komanso zinthu monga nkhondo, makhalidwe oipa, njala, miliri ndi zivomerezi zili ponseponse. Nazonso zipembedzo zikusokoneza kwambiri anthu. (Mat. 24:7, 11, 12, 14; Luka 21:11) Tikuyembekezera nthawi imene Yesu adzabwere kudzatipulumutsa komanso kudzakwaniritsa chifuniro cha Mulungu.—Maliko 13:26, 27.

TSIKULO LIKUYANDIKIRA KWAMBIRI

4. (a) Tikudziwa bwanji kuti Yesu panopa akudziwa nthawi imene Aramagedo idzayambe? (b) Ngakhale kuti sitidziwa nthawi imene chisautso chachikulu chidzayambe, kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

4 Tikakhala pamsonkhano, timadziwa nthawi yeniyeni imene chigawo chilichonse chiyambe. Koma ngakhale titayesetsa bwanji sitingadziwe chaka, tsiku kapena ola limene chisautso chachikulu chidzayambe. Yesu ali padzikoli ananena kuti: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mat. 24:36) Koma Yesu Khristu wapatsidwa mphamvu kuti awononge dziko la Satanali. (Chiv. 19:11-16) Choncho tikhoza kunena kuti panopa akudziwa nthawi imene Aramagedo idzayambe. Koma ifeyo sitikudziwa nthawi yake. Ndiyetu mpake kuti tiyenera kukhala maso mpaka pamene chisautso chidzayambe. Yehova akudziwa nthawi yeniyeni pamene chisautso chidzayambe. Nthawiyo ikuyandikirayandikirabe ndipo Baibulo limanena kuti ‘siidzachedwa.’ (Werengani Habakuku 2:1-3.) Kodi tingatsimikize bwanji zimenezi?

5. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amakwaniritsa malonjezo ake pa nthawi yake.

5 Yehova amakwaniritsa chilichonse chimene walonjeza pa nthawi yake yeniyeni. Taganizirani zimene anachita populumutsa Aisiraeli ku Iguputo. Iye anawapulumutsa pa Nisani 14, 1513 B.C.E. Ndiyeno ponena za tsiku limeneli, Mose analemba kuti: “Zaka 430 zimenezi zitatha, pa tsiku lomwe zinatha, makamu onse a Yehova anatuluka m’dziko la Iguputo.” (Eks. 12:40-42) Zaka 430 zimenezi zinayamba pamene pangano lomwe Yehova anachita ndi Abulahamu linayamba kugwira ntchito mu 1943 B.C.E. (Agal. 3:17, 18) Patapita nthawi, Yehova anauza Abulahamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni, ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.” (Gen. 15:13; Mac. 7:6) Zikuoneka kuti zaka 400 zimenezi zinayamba mu 1913 B.C.E. pamene Isimaeli ankanyoza Isaki ndipo zinatha pamene Aisiraeli anachoka ku Iguputo mu 1513 B.C.E. (Gen. 21:8-10; Agal. 4:22-29) Kodi si zochititsa chidwi kuti Yehova ananeneratu nthawi imene adzapulumutse Aisiraeli kutatsala zaka mahandiredi angapo?

6. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira zoti Yehova adzapulumutsa anthu ake?

6 Yoswa anali m’gulu la anthu amene anachoka ku Iguputo. Iye anakumbutsa Aisiraeli kuti: “Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.” (Yos. 23:2, 14) Nafenso tisamakayikire zoti Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzatipulumutsa pa chisautso chachikulu. Koma kuti tidzapulumuke tiyenera kukhalabe maso.

KUTI TIDZAPULUMUKE TIYENERA KUKHALABE MASO

7, 8. (a) Kodi alonda a mizinda yakale ankafunika kuchita chiyani, nanga tikuphunzirapo chiyani? (b) Perekani chitsanzo cha mavuto amene angachitike ngati alonda agona.

7 Tikhoza kuphunzira zambiri pa nkhani yokhudza kukhala maso tikaganizira zimene alonda a m’mizinda yakale ankachita. Kalelo mizinda yaikulu monga Yerusalemu inkakhala ndi mipanda italiitali. Mipandayi inkawateteza ndipo inkathandiza kuti alonda aziona ngati adani akubwera. Alondawo ankakhala pampanda kapena pageti usana ndi usiku. Kukamabwera choopsa chilichonse, iwo ankayenera kudziwitsa anthu a mumzindawo. (Yes. 62:6) Alondawa ankadziwa kuti ayenera kukhala maso nthawi zonse kuti adziwe zimene zikuchitika chifukwa kupanda kutero akanaphetsa anthu ambirimbiri.—Ezek. 33:6.

8 Wolemba mbiri wina dzina lake Josephus ananena kuti, Aroma analowa mumzinda wa Yerusalemu mu 70 C.E. chifukwa chakuti alonda a pageti anagona. Aromawo anapita kukayatsa kachisi kenako n’kuwononga mzinda wonsewo. Ichi chinali chimake cha mavuto oopsa amene anachitika ku Yerusalemu.

9. Kodi anthu ambiri sadziwa za chiyani?

9 Masiku ano, mayiko ambiri ali ndi asilikali olondera m’malire komanso zipangizo zamakono zachitetezo. Amachita izi kuti aziona zigawenga kapena adani ofuna kulowa m’dziko lawo. Koma mabomawa sadziwa zoti pali boma lamphamvu kumwamba lolamulidwa ndi Yesu. Bomali lidzawononga maboma onse padzikoli. (Yes. 9:6, 7; 56:10; Dan. 2:44) Koma ifeyo timayesetsa kukhala maso kuti tsiku la Yehova lidzatipeze tili okonzeka.—Sal. 130:6.

ZINTHU ZIMENE ZINGATISOKONEZE

10, 11. (a) Kodi tiyenera kukhala osamala ndi chiyani? Perekani chifukwa. (b) N’chiyani chikukutsimikizirani kuti Mdyerekezi akupangitsa anthu kuti azinyalanyaza ulosi wa m’Baibulo?

10 Taganizirani mmene mlonda amamvera kukamacha, ngati wakhala maso usiku wonse. Amatopa kwambiri moti zimakhala zovuta kuti akhalebe maso. Ndi mmene zililinso masiku ano. Pamene mapeto akuyandikira zizikhala zovuta kwambiri kuti tikhalebe maso. Koma zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri ngati tingayambe kugona. Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene zingatilepheretse kukhala maso tikapanda kusamala.

11 Satana akusocheretsa anthu. Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anachenjeza ophunzira ake katatu za “wolamulira wa dzikoli.” (Yoh. 12:31; 14:30; 16:11) Iye ankadziwa kuti Mdyerekezi adzachititsa anthu kuti akhale mumdima n’cholinga choti asakhale maso komanso asadziwe zimene zichitike posachedwapa. (Zef. 1:14) Satana amasocheretsa anthu pogwiritsira ntchito zipembedzo zonyenga. Kodi inuyo simuona umboni wakuti iye wachititsa “khungu maganizo a anthu osakhulupirira”? Ambiri sadziwa zoti Yesu akulamulira ndiponso zoti posachedwapa mapeto afika. (2 Akor. 4:3-6) Nthawi zambiri tikamalalikira timapeza anthu osafuna kumva uthenga wathu. Iwo amakayikira tikamawauza kuti mapeto ali pafupi.

12. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala kuti tisapusitsidwe ndi Mdyerekezi?

12 Tonsefe tikudziwa ubwino wokhala maso choncho tisalole kuti zochita za anthu ena zitifooketse kapena kutisokoneza. Paja Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku.” (Werengani 1 Atesalonika 5:1-6.) Nayenso Yesu anapereka chenjezo loti: “Inunso khalani okonzeka, chifukwa pa ola limene simukuliganizira, Mwana wa munthu adzafika.” (Luka 12:39, 40) Posachedwapa, Satana adzapusitsa anthu n’kumaganiza kuti padzikoli pali “bata ndi mtendere” ndipo zinthu zikuyenda bwino. Koma ife tikapitirizabe kukhala maso, tsiku lachiweruzoli silidzatidzidzimutsa “ngati mmene lingachitire kwa mbala.” Choncho tiyenera kuwerenga Mawu a Mulungu tsiku lililonse n’kumaganizira kwambiri zimene Yehova akutiphunzitsa.

13. Kodi mzimu wa dziko ukusokoneza bwanji anthu, nanga ifeyo tingaupewe bwanji?

13 Mzimu wa dzikoli umagonetsa anthu mwauzimu. Masiku ano anthu akutanganidwa kwambiri ndi zinthu zina moti sazindikira “zosowa zawo zauzimu.” (Mat. 5:3) Iwo amakopeka ndi zinthu za m’dzikoli zimene zimalimbikitsa ‘chilakolako cha thupi ndi cha maso.’ (1 Yoh. 2:16) Nazonso zosangalatsa zili mbwee moti anthu ambiri ndi “okonda zosangalatsa.” (2 Tim. 3:4) Akakhala mayesero ndiye akuwonjezeka chaka ndi chaka. N’chifukwa chake Paulo anauza Akhristu kuti: “Musamakonzekere kuchita zilakolako za thupi.”—Aroma 13:11-14.

14. Kodi palemba la Luka 21:34, 35 pali malangizo otani?

14 Timayesetsa kupewa mzimu wa dziko ndipo timafuna kuti mzimu wa Mulungu uzititsogolera. Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wakewu potithandiza kumvetsa zinthu zimene zichitike posachedwapa. [1] (1 Akor. 2:12) Komabe timadziwa kuti kupanda kusamala, ngakhale zinthu zabwinobwino zingatilepheretse kukhala maso. (Werengani Luka 21:34, 35.) Anthu ena angamatinyoze akaona kuti tikuyesetsa kukhala maso, koma tisalole kuti zimenezi zitifooketse. (2 Pet. 3:3-7) M’malomwake tiyenera kusonkhana ndi Akhristu anzathu chifukwa mzimu wa Mulungu umapezeka kumisonkhanoko.

Kodi mukuchita zonse zimene mungathe kuti mukhalebe maso? (Onani ndime 11-16)

15. Kodi n’chiyani chinachitikira Petulo, Yakobo ndi Yohane, nanga zoterezi zingatichitikerenso bwanji ifeyo?

15 Tingamavutike kukhala maso chifukwa si ife angwiro. Yesu ankadziwa kuti n’zosavuta kwa anthu omwe si angwiro kugonja akakumana ndi mayesero. Taganizirani zimene zinachitika usiku woti aphedwa mawa lake. Iye ankadziwa kuti ayenera kudalira Atate wake kuti athe kukhalabe wokhulupirika. Choncho anapita kukapemphera ndipo anauza Petulo, Yakobo ndi Yohane kuti nawonso ‘akhalebe maso.’ Koma iwo sanazindikire kuti nthawiyi inali yofunikadi kukhala maso kwambiri, choncho anagona. Ngakhale kuti Yesu nayenso anali atatopa, anakhalabe maso ndipo ankapemphera kwambiri kwa Atate wake. N’zimenenso ophunzira akewo ankayenera kuchita.—Maliko 14:32-41.

16. Mogwirizana ndi lemba la Luka 21:36, kodi Yesu anati tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tikhalebe maso’?

16 Kuti ‘tikhale maso’ pamafunika zambiri osati kungokhala ndi maganizo abwino. Masiku angapo zisanachitike zimene tatchula m’ndime yapitayi, Yesu anauza atumwiwo kuti azipemphera kwa Yehova mopembedzera. (Werengani Luka 21:36.) Choncho kuti tikhale maso, nafenso tiyenera kumapemphera nthawi zonse.—1 Pet. 4:7.

TISASIYE KUKHALA MASO

17. Kodi tingatani kuti tikhale okonzeka?

17 Paja Yesu ananena kuti mapeto adzafika ‘pa ola limene sitikuliganizira.’ (Mat. 24:44) Choncho ino si nthawi yoti tizifunafuna moyo umene dzikoli limaona kuti ungachititse munthu kukhala wosangalala. Zimenezo zingapangitse kuti tiyambe kusinza mwauzimu. M’Baibulo timapeza malangizo ochokera kwa Yehova ndi Yesu amene angatithandize kuti tikhalebe maso. Choncho tiyeni tiziganizira maulosi a m’Baibulo amene akukwaniritsidwa panopa komanso kukwaniritsidwa kwake. Tizionetsetsanso kuti tili pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso tikuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba. Tikatero mapeto adzatipeza tili okonzeka ndipo tidzapulumuka.—Chiv. 22:20.

^ [1] (ndime 14) Onani mutu 21 m’buku lakuti, Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.