Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzifunafuna Ufumu Osati Zinthu Zina

Muzifunafuna Ufumu Osati Zinthu Zina

“Pitirizani kufunafuna Ufumu [wa Mulungu], ndipo zinthu zimenezi zidzawonjezedwa kwa inu.”​—LUKA 12:31.

NYIMBO: 40, 98

1. Kodi zinthu zofunika pa moyo zimasiyana bwanji ndi zosafunika kwenikweni?

ZINTHU zofunika pa moyo wathu n’zochepa koma zimene timalakalaka titakhala nazo ndi zambirimbiri. Vuto ndi lakuti anthu ambiri satha kusiyanitsa zinthu zofunika pa moyo ndi zosafunika kwenikweni. Kodi kusiyana kwake kuli pati? “Zofunika pa moyo” ndi zinthu zimene titapanda kukhala nazo sitingakhale ndi moyo. Apa tikunena chakudya, zovala ndi malo ogona. Koma “zinthu zosafunika kwenikweni” ndi zimene tikhoza kukhala ndi moyo ngakhale tilibe.

2. Tchulani zinthu zina zimene anthu amafuna atakhala nazo.

2 Zinthu zosafunika kwenikweni zimene anthu amazilakalaka zimasiyana malinga ndi kumene anthuwo akukhala. M’mayiko osauka, ambiri amafuna atakhala ndi foni, njinga yamoto kapena malo. Koma m’mayiko olemera anthu amafuna atakhala ndi zovala zapamwamba, nyumba yaikulu komanso galimoto yodula. Koma msampha wokonda chuma umakhudza anthu m’dziko lililonse. Anthu amachita chilichonse chimene angathe kuti apeze zomwe akufuna ngakhale zitakhala zosafunika kwenikweni komanso zodula kwambiri.

PEWANI MSAMPHA WOKONDA CHUMA

3. Kodi Munthu wokonda chuma amatani?

3 Kodi munthu wokonda chuma amatani? Amakhala ndi mtima wongofuna kukhala ndi zinthu zambiri osati kutumikira Mulungu. Munthu wotereyu amalakalaka kwambiri zinthu zimene akufunazo ndipo amaona kuti n’zofunika kuposa chilichonse pa moyo wake. Ngakhale munthu amene alibe ndalama zambiri komanso sagula zinthu zodula kwambiri, akhoza kukhala wokonda chuma. Choncho nawonso anthu osauka akhoza kukhala okonda chuma n’kumalephera kufunafuna Ufumu choyamba.—Aheb. 13:5.

4. Kodi Satana amagwiritsa ntchito bwanji “chilakolako cha maso”?

4 Satana amagwiritsa ntchito anthu otsatsa malonda pofuna kutikopa. Amafuna tiziganiza kuti tingakhale osangalala tikakhala ndi zinthu zambirimbiri. Iye amagwiritsa ntchito “chilakolako cha maso.” (1 Yoh. 2:15-17; Gen. 3:6; Miy. 27:20) Dzikoli lili ndi zinthu zosiyanasiyana, zina zabwino koma zina zachabechabe, ndipo zina zimaoneka zokopa kwambiri. Kodi inuyo munagulapo chinthu chosafunika kwenikweni chifukwa choti anachitsatsa kapena munangochiona musitolo? Kodi munazindikira kuti mukanatha kukhala bwinobwino popanda chinthucho? Zinthu zosafunika kwenikweni ngati zimenezo zimangochititsa kuti tizikhala ndi nkhawa. Zikhoza kutilepheretsa kuchita zinthu zofunika monga kuphunzira Baibulo, kukonzekera komanso kupezeka pamisonkhano ndiponso kulalikira. Tisaiwale chenjezo la mtumwi Yohane lakuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.”

5. N’chiyani chimachitikira anthu amene amatanganidwa ndi kusakasaka chuma?

5 Satana amafuna kuti tikhale akapolo a chuma osati a Yehova. (Mat. 6:24) Anthu amene amatanganidwa ndi kusakasaka chuma, zinthu siziwayendera bwino. Iwo sakhutira ndi zimene apeza, amakhala ndi nkhawa, amagwiritsidwa mwala komanso ubwenzi wawo ndi Yehova umasokonekera. (1 Tim. 6:9, 10; Chiv. 3:17) Mfundo imeneyi ikugwirizana ndi zimene Yesu ananena mu fanizo la wofesa mbewu. Iye anati uthenga wa Ufumu ukafesedwa paminga, “zilakolako za zinthu zina, zimalowa ndi kulepheretsa mawuwo kukula, ndipo sabala zipatso.”—Maliko 4:14, 18, 19.

6. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Baruki?

6 Tiyeni tikambirane nkhani ya mlembi wa Yeremiya dzina lake Baruki. Mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa, iye anayamba kufunafuna “zinthu zazikulu” zomwe sizikanakhalitsa. Komatu Baruki ankangofunika kuyembekezera zimene Yehova anamulonjeza. Paja anamuuza kuti: “Iwe ndidzakupatsa moyo wako monga chofunkha chako.” (Yer. 45:1-5) Yehova sakanapulumutsa chuma cha munthu aliyense mumzinda umene ankafuna kuuwononga. (Yer. 20:5) Panopa mapeto ali pafupi choncho si nthawi yodziunjikira chuma. Tisaganize kuti tidzapulumuka chisautso chachikulu limodzi ndi zinthu zimene tili nazo, ngakhale zitakhala zamtengo wapatali kwambiri.—Miy. 11:4; Mat. 24:21, 22; Luka 12:15.

7. Kodi tikambirana chiyani, nanga zitithandiza bwanji?

7 Ndiye kodi tingatani kuti tizitha kudzisamalira komanso kusamalira mabanja athu popanda kunyalanyaza zinthu zokhudza kulambira? Nanga tingatani kuti tisamakonde chuma komanso tisamadere nkhawa kwambiri zofunika pa moyo? Yesu anapereka malangizo othandiza kwambiri pa ulaliki wake wapaphiri. (Mat. 6:19-21) Tiyeni tiwerenge malangizo amene ali pa Mateyu 6:25-34 n’kukambirana zimene tikuphunzirapo. Izi zitithandiza kuti ‘tizifunafuna ufumu’ osati zinthu zina.Luka 12:31.

YEHOVA AMATIPATSA ZOFUNIKA PA MOYO

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kudera nkhawa kwambiri zinthu zofunika pa moyo? (b) Kodi Yesu ankadziwa bwino zinthu ziti?

8 Werengani Mateyu 6:25. Pamene Yesu anauza anthu amene ankawaphunzitsa kuti, “lekani kudera nkhawa moyo wanu,” ankatanthauza kuti ayenera kusiya kudandaula kwambiri. Anthuwo ankadera nkhawa zinthu zosafunika kuzidera nkhawa. Ndiyeno anawauza kuti asiye ndipo anapereka chifukwa chomveka. Munthu akamadera nkhawa kwambiri zinthu zina akhoza kusokonezeka n’kuyamba kuiwala zinthu zokhudza ubwenzi wake ndi Yehova. Yesu ankaona kuti nkhaniyi ndi yaikulu ndipo anachenjeza ophunzira ake za msampha umenewu maulendo 4 pa ulaliki wake wapaphiri.—Mat. 6:27, 28, 31, 34.

9 N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti tisamadere nkhawa kuti tidya chiyani, timwa chiyani kapena tivala chiyani? Tikufunsa choncho chifukwa zinthu zimenezi ndi zofunika pa moyo. Ndipo ngati palibe njira yopezera zinthuzi, munthu akhoza kudadi nkhawa. Tiyenera kukumbukira kuti Yesu ankadziwa zonsezi. Iye ankadziwanso zinthu zimene anthu amafunikira tsiku lililonse. Komanso ankadziwa mavuto amene anthu adzakumane nawo m’masiku otsiriza ano, omwe Baibulo linawatchula kuti ndi “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Tim. 3:1) Ena mwa mavutowa ndi monga njala, umphawi, kusowa kwa ntchito komanso kukwera mitengo kwa zinthu. Koma Yesu ankadziwa kuti ‘moyo ndi wofunika kuposa chakudya ndipo thupi ndi lofunika kuposa chovala.’

10. Pamene Yesu ankaphunzitsa zokhudza kupemphera, kodi anati chofunika kwambiri ndi chiyani?

10 Chakumayambiriro kwa ulaliki wake, Yesu anaphunzitsa anthu kuti azipempha Atate wakumwamba kuti: “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” (Mat. 6:11) Polemba mawu omwewa, Luka analemba kuti: “Mutipatse chakudya chathu chalero malinga ndi chakudya chofunika pa tsikuli.” (Luka 11:3) Koma malangizo amenewa sakutanthauza kuti tizingokhalira kuganizira zinthu zofunika pa moyo wathu. Tikutero chifukwa chakuti mu pemphero lomweli, Yesu anasonyeza kuti chofunika kwambiri n’kupempha kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. (Mat. 6:10; Luka 11:2) Ndiyeno pofuna kukhazika mtima pansi anthu amene ankawaphunzitsawo, iye anafotokoza umboni wakuti Yehova amasamalira zinthu zimene analenga.

11, 12. Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova amasamalirira mbalame? (Onani chithunzi patsamba 7.)

11 Werengani Mateyu 6:26. Yesu anati ‘tizionetsetsa mbalame zam’mlengalenga.’ Mbalame zimakonda kudya zipatso, nthanga, tizilombo touluka komanso nyongolotsi. Ndipotu tikaganizira kulemera kwa mbalame, tingati zimadya kwambiri kuposa anthu. Koma sizilima kuti zipeze chakudya chimenechi. Yehova amazipatsa chakudya chokwanira. (Sal. 147:9) Komabe sikuti amachita kuika chakudya pakamwa pa mbalamezi. Amangoonetsetsa kuti chakudyacho chilipo. Mbalame iliyonse imafunika kukasaka chakudya choti idye.

12 Yesu ankaona kuti Atate wake wakumwamba sangapatse chakudya mbalame koma n’kulephera kupatsa anthu zofunika pa moyo. [1] (1 Pet. 5:6, 7) Koma nafenso sitingayembekezere kuti aika chakudya pakamwa pathu. M’malomwake amatithandiza kuti tithe kulima chakudya kapena tipeze ndalama zoti tigulire chakudya cha tsiku ndi tsiku. Pa nthawi ya mavuto, angapangitse kuti anthu ena atithandize. Ngakhale kuti Yesu sanatchule zoti Yehova amapatsa mbalame malo okhala, iye amazipatsa nzeru, luso komanso zinthu zoti zithe kumangira zisa n’kumakhalamo. Ifenso Yehova angatithandize kuti tipeze malo okhala.

13. N’chiyani chimasonyeza kuti ndife amtengo wapatali kuposa mbalame?

13 Yesu anafunsa anthu amene ankawaphunzitsa kuti: “Nanga inu sindinu amtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” Pamene Yesu ankafunsa funsoli ankadziwanso kuti pakapita nthawi apereka moyo wake kuwombola anthuwo. (Yerekezerani ndi Luka 12:6, 7.) Dipo la Yesu silinaperekedwe pofuna kuwombola nyama kapena mbalame. Yesu anafera anthu n’cholinga choti adzapeze moyo wosatha.—Mat. 20:28.

14. N’chifukwa chiyani kuda nkhawa kwambiri n’kosathandiza?

14 Werengani Mateyu 6:27. Nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti munthu sangatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha mwa kuda nkhawa? N’chifukwa chakuti kudera nkhawa zinthu zosafunika sikungathandize kuti munthu akhale ndi moyo wautali. Ndipotu kuda nkhawa kwambiri n’kumene kungapangitse kuti munthu afe msanga.

15, 16. (a) Kodi tikuphunzira chiyani tikaganizira mmene Yehova amasamalirira maluwa akutchire? (Onani chithunzi patsamba 7.) (b) Kodi tiyenera kudzifunsa funso liti, ndipo n’chifukwa chiyani?

15 Werengani Mateyu 6:28-30. Tonsefe timafuna kutchena, makamaka tikamapita mu utumiki komanso kumisonkhano yampingo kapena ikuluikulu. Koma kodi tiyenera kuda nkhawa kwambiri “pa nkhani ya zovala”? Ayi. Tikutero chifukwa pa nkhani imeneyinso Yesu anatchula zimene Yehova amachita. Tingaphunzire zambiri tikaona mmene “maluwa akutchire” amaonekera. Mwina Yesu ankaganizira za maluwa osiyanasiyana amene amaoneka okongola kwambiri. Komatu palibe chilichonse chimene maluwa amenewa amachita kuti azioneka okongola chonchi. Koma Yesu ananena kuti “ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.”

16 Kenako Yesu anafunsa anthuwo kuti: “Ngati Mulungu amaveka chotero zomera zakutchire, . . . kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo, achikhulupiriro chochepa inu?” Yankho la funsoli linali lodziwikiratu. Koma ophunzira a Yesuwo anali ndi chikhulupiriro chochepa. (Mat. 8:26; 14:31; 16:8; 17:20) Choncho ankafunika kulimbitsa chikhulupiriro kuti azidalira kwambiri Yehova. Nanga bwanji ifeyo? Kodi timakhulupirira kuti Yehova angathe kutipatsa zonse zomwe timafunikira?

17. Kodi n’chiyani chingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?

17 Werengani Mateyu 6:31, 32. Tiyenera kukhala osiyana ndi “anthu a mitundu ina.” Paja iwo sakhulupirira zoti Atate wakumwamba amapereka zofunika pa moyo kwa anthu amene amaika Ufumu pamalo oyamba. Tikamalimbana ndi kufufuza ‘zinthu zimene anthu a mitundu ina amafunafuna mwakhama,’ tikhoza kusokoneza ubwenzi wathu ndi Yehova. Tisamakayikire kuti tikamaika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba, Yehova adzaonetsetsa kuti tikupeza zofunika pa moyo. “Mtima wodzipereka kwa Mulungu” ungatithandize kuti tizikhutira ndi “chakudya, zovala ndi pogona.”—1 Tim. 6:6-8.

KODI MUMAONA KUTI UFUMU WA MULUNGU NDI WOFUNIKA KWAMBIRI?

18. Kodi Yehova amadziwa zinthu ziti zokhudza ifeyo, nanga amachita chiyani?

18 Werengani Mateyu 6:33. Akhristufe tiyenera kuika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba nthawi zonse. Yesu anati tikamachita zimenezi, Mulungu ‘adzatiwonjezera zina zonse.’ Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Yesu anati: “Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.” Ponena kuti “zinthu zonsezi” ankatanthauza zofunika pa moyo. Yehova amatha kudziwiratu zimene munthu akufunikira pa nkhani ya chakudya, zovala komanso pogona, mwinanso munthuyo asanadziwe n’komwe. (Afil. 4:19) Mwachitsanzo, amadziwa kuti ndi chovala chanu chiti chimene chidzayambe kutha. Amadziwanso chakudya choyenera kwa inu komanso malo amene angakhale oyenera kwa inu mogwirizana ndi kukula kwa banja lanu. Ndipotu amaonetsetsa kuti tili ndi zofunika pa moyo.

19. N’chifukwa chiyani sitiyenera kudera nkhawa za mawa?

19 Werengani Mateyu 6:34. Kodi mwaona kuti palembali Yesu ananena kachiwirinso kuti “musamade nkhawa”? Iye ankafuna kuti tizithana ndi mavuto a tsiku limodzi popanda kudera nkhawa za mawa ndipo tizikhulupirira kuti Yehova atithandiza. Munthu akamadera nkhawa kwambiri zimene zidzachitike m’tsogolo, amayamba kudzidalira m’malo modalira Yehova. Izi zingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova.—Miy. 3:5, 6; Afil. 4:6, 7.

MUZIFUNA UFUMU CHOYAMBA NDIPO YEHOVA ADZAKUPATSANI ZINAZO

Kodi mungasinthe zina ndi zina kuti muzikhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu zokhudza kulambira? (Onani ndime 20)

20. (a) Kodi inuyo muli ndi zolinga zotani? (b) Kodi musintha zinthu ziti kuti zolingazo zitheke?

20 Si nzeru kusiya zinthu zokhudza kulambira chifukwa chofuna kukhala ndi moyo wawofuwofu. Nthawi zonse zinthu zokhudza kulambira ziyenera kukhala pamalo oyamba. Mwachitsanzo, kodi mungathe kusamukira kumpingo umene kulibe ofalitsa ambiri? Kapena kodi mungayambe upainiya? Ngati mukuchita kale upainiya, kodi mungapemphe kuti mulowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu? Nanga kodi mungakwanitse kutumikira ku Beteli kapena ku ofesi ya omasulira mabuku, masiku angapo pamlungu? Kodi mwina mungadzipereke kuchita utumiki wa zomangamanga? Ndi bwino kuona zimene mungasinthe pa moyo wanu n’cholinga choti muthe kuchita zambiri potumikira Yehova. Onani bokosi lakuti, “ Zimene Mungachite Kuti Muzikhala Moyo Wosalira Zambiri” ndipo pempherani kwa Yehova n’kuganizira zimene mungachite kuti mukwanitse zolinga zanu.

21. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova?

21 Yesu anali ndi zifukwa zabwino potiuza kuti tizifunafuna Ufumu osati zinthu zina. Tikamatsatira malangizo akewa, sitidera nkhawa kwambiri zinthu zofunika pa moyo. Komanso tikamakhulupirira Yehova ndi mtima wonse, timakhala naye pa ubwenzi wolimba. Zikatero, sitimangotengeka ndi zilizonse ndipo ngakhale titakhala ndi ndalama zokwanira timapewa kumangogula chilichonse chimene taona. Tikamayesetsa kukhala moyo wosalira zambiri, tingathe kugwira “mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:19.

^ [1] (ndime 12) Kuti mudziwe chifukwa chake nthawi zina Yehova amalola kuti Mkhristu akhale wopanda chakudya chokwanira, werengani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2014, patsamba 22.