Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatsatira ndi Mtima Wonse Zimene Zinalembedwa?

Kodi Mumatsatira ndi Mtima Wonse Zimene Zinalembedwa?

“Zinthu zimenezi . . . zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo amene mapeto a nthawi zino atifikira.”1 AKOR. 10:11.

NYIMBO: 11, 61

1, 2. Kodi kukambirana zitsanzo za mafumu 4 a ku Yuda kutithandiza bwanji?

TIYEREKEZE kuti mukuyenda ndipo mwaona munthu amene ali patsogolo panu atapunthwa n’kugwa. Kodi inuyo podutsa pamalopo simungayende mosamala? Mofanana ndi zimenezi, kuganizira zolakwa zimene ena anachita kungatithandize kuti nafenso tisachite zomwezo. Choncho tingaphunzire zambiri pa zolakwa zimene ena anachita kuphatikizapo za anthu otchulidwa m’Baibulo.

2 Mafumu 4 a ku Yuda omwe tinakambirana m’nkhani yapita ija, ankatumikira Yehova ndi mtima wathunthu. Komabe iwo anachita zinthu zina zolakwika kwambiri. Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinawachitikira, nanga tingazipewe bwanji? Popeza nkhani zawo zinalembedwa m’Baibulo kuti zitichenjeze, kukambirana nkhanizi kungatithandize kwambiri.Werengani Aroma 15:4.

KUDALIRA NZERU ZA ANTHU N’KOOPSA

3-5. (a) Ngakhale kuti Asa anatumikira Yehova ndi mtima wathunthu, kodi anakumana ndi mavuto ati chifukwa cha zolakwika zimene anachita? (b) Kodi mwina n’chifukwa chiyani Asa sanadalire Yehova pamene Basa anaukira Yuda?

3 Tiyeni tiyambe ndi kukambirana za Asa. Pamene Aitiyopiya okwana 1 miliyoni anabwera kudzaukira Yuda, Asa anadalira Yehova. Koma iye analephera kudaliranso Yehova pamene Basa mfumu ya Isiraeli, anayamba kumanga mpanda wolimba kwambiri kuzungulira mzinda wa Rama womwe unali m’malire a Yuda. (2 Mbiri 16:1-3) Asa anadalira nzeru zake ndipo anapereka ziphuphu kwa mfumu ya Siriya dzina lake Beni-hadadi n’cholinga choti ikaukire Basa. Kodi mapulani a Asa amenewa anathandiza? Zingaoneke ngati anathandiza chifukwa Baibulo limati: “Basa atangomva zimenezi, nthawi yomweyo anasiya kumanga Rama n’kuimitsa ntchito yake.”—2 Mbiri 16:5.

4 Koma kodi Yehova anasangalala ndi zimene Asa anachitazi? Ayi. Tikutero chifukwa iye anatumiza Haneni kuti akadzudzule Asa chifukwa choti sanamudalire. (Werengani 2 Mbiri 16:7-9.) Haneni anauza Asa kuti: “Kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.” Choncho ngakhale kuti Basa anachoka ndipo Asa anatenga mzinda wa Rama, Asayo ndi anthu ake ankangokhalira kumenya nkhondo pa nthawi yonse ya ulamuliro wake.

5 Komabe monga tinaonera m’nkhani yapita ija, Yehova atafufuza mtima wa Asa anaona kuti ankamutumikira ndi mtima wathunthu. (1 Maf. 15:14) Koma Asa anayenera kukumana ndi zotsatira za zinthu zolakwika zimene anachita. Kodi n’chifukwa chiyani Asa anadalira nzeru zake komanso za —Beni-hadadi —m’malo modalira Yehova? Mwina iye anachita zimenezi chifukwa choti ankaganiza kuti asilikali aluso ndi amene angamuthandize. Kapenanso n’chifukwa choti anatsatira malangizo a anthu olakwika.

6. Kodi tingaphunzire chiyani pa zinthu zolakwika zimene Asa anachita? Perekani chitsanzo.

6 Kodi tingaphunzire chiyani pa zinthu zolakwika zimene Asa anachita? Nthawi zambiri tikakumana ndi mavuto amene tikuona kuti sitingathane nawo patokha, zimakhala zosavuta kudalira Yehova. Koma kodi timadaliranso Yehova pa zinthu zing’onozing’ono zimene timakumana nazo tsiku ndi tsiku kapena timangodalira nzeru zathu? Nanga kodi timafufuza mfundo za m’Baibulo posonyeza kuti tikudalira Yehova? Mwachitsanzo, tiyerekezere kuti mukutsutsidwa ndi achibale anu kuti musamapite kumisonkhano yampingo kapena ikuluikulu. Mwina mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita. Ndiyeno tiyerekezenso kuti mwachotsedwa ntchito ndipo mukuvutika kupeza ina. Kenako mukulankhula ndi bwana wina amene akufuna kuti akulembeni ntchito. Kodi mungamufotokozere zoti adzafunika kumakupatsani nthawi yosonkhana m’kati mwa mlungu? Kapena simunganene poopa kuti sakulembani? Pa vuto lililonse limene tingakumane nalo, tingachite bwino kutsatira malangizo a wamasalimo akuti: “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako, umudalire ndipo iye adzachitapo kanthu.”Sal. 37:5.

KUGWIRIZANA NDI ANTHU OLAKWIKA KUNGATIIKE M’MAVUTO

7, 8. Kodi Yehosafati anachita zinthu ziti zolakwika, ndipo zotsatira zake zinali zotani? (Onani chithunzi patsamba 23.)

7 Tiyeni tsopano tikambirane chitsanzo cha mwana wa Asa dzina lake Yehosafati. Iye anali ndi makhalidwe abwino ambiri. Pa nthawi imene ankadalira Yehova zinthu zinkayenda bwino kwambiri. Koma iye analakwitsanso zinthu zina. Mwachitsanzo, anakonza zoti mwana wake wamwamuna akwatire mwana wamkazi wa Mfumu Ahabu ya Isiraeli, yomwe inali yoipa kwambiri. Kenako anagwirizana ndi Ahabu kuti akamenyane ndi Asiriya ngakhale kuti anachenjezedwa ndi mneneri Mikaya kuti asapite. Kunkhondoko, Yehosafati anapulumukira m’kamwa mwa mbuzi ndipo anabwerera ku Yerusalemu. (2 Mbiri 18:1-32) Ndiyeno mneneri Yehu anamufunsa kuti: “Kodi chithandizo chiyenera kuperekedwa kwa oipa, ndipo kodi muyenera kukonda anthu odana ndi Yehova?”Werengani 2 Mbiri 19:1-3.

8 Kodi Yehosafati anaphunzirapo kanthu? Ayi ndithu. N’zoona kuti ankayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Yehova koma anapitiriza kugwirizana ndi anthu osalambira Yehova. Iye anachitanso mgwirizano ndi Mfumu Ahaziya yemwe anali mwana wa Ahabu. Yehosafati ndi Ahaziya anapanga zombo koma zinasweka asanazigwiritse ntchito imene ankafuna.—2 Mbiri 20:35-37.

9. Kodi kugwirizana ndi anthu oipa kungatibweretsere mavuto ati?

9 Nkhani ya Yehosafatiyi ingatithandize kuti tionenso zimene timachita pa moyo wathu. Yehosafati anachita zabwino ndipo “anafunafuna Yehova ndi mtima wake wonse.” (2 Mbiri 22:9) Koma ankagwirizana ndi anthu oipa ndipo izi zinamubweretsera mavuto. Paja Baibulo limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miy. 13:20) Ifenso timayesetsa kuthandiza anthu kuti ayambe kulambira Yehova. Koma tisamaiwale kuti Yehosafati anangotsala pang’ono kuphedwa chifukwa chogwirizana ndi anthu olakwika. Choncho tizidziwa kuti si bwino kugwirizana kwambiri ndi anthu osalambira Yehova chifukwa tingapeze mavuto mwinanso kuika moyo wathu pachiswe.

10. (a) Ngati tikufuna kupeza munthu wokwatirana naye, kodi tingaphunzire chiyani kwa Yehosafati? (b) Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati tayamba kukondana ndi munthu wosalambira Yehova?

10 Kodi tingaphunzirenso chiyani pa nkhani ya Yehosafati? Mwina Mkhristu angayambe kukondana ndi munthu wosalambira Yehova poganiza kuti sangapeze munthu woyenera kukwatirana naye m’gulu la Yehova. Kapenanso Mkhristu angamakakamizidwe ndi achibale omwe si Mboni kuti alowe m’banja. Angamamuuze kuti ngati salowa m’banja panopa ndiye kuti akalamba. N’zoona kuti Yehova anatilenga m’njira yoti tizifuna kukonda ena komanso kukondedwa. Komabe kodi Mkhristu ayenera kuchita chiyani ngati sakupeza munthu woyenera kukhala naye pa banja? Kuganizira zimene zinachitikira Yehosafati kungathandize kwambiri. Iye ankadalira Yehova kuti amutsogolere. (2 Mbiri 18:4-6) Musaiwale zimene zinachitikira Yehosafati pamene anayamba kugwirizana ndi Ahabu, yemwe sankakonda Yehova. Iye ankayenera kukumbukira kuti maso a Yehova amakhala pa anthu amene amamutumikira ndi mtima wathunthu. Masiku anonso “maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi” ndipo iye ndi wokonzeka ‘kuti ationetse mphamvu zake.’ (2 Mbiri 16:9) Yehova amatikonda ndipo amadziwa bwino mavuto athu. Paja iye ndi amene anatilenga m’njira yoti tizifuna kukonda ena komanso kukondedwa. Ndiye kodi inuyo mumakhulupirira kuti iye angakuthandizeni kupeza munthu woyenera kukwatirana naye? Musamakayikire, chifukwa pangapite nthawi adzakuthandizani ndithu.

Tizisamala ndi zinthu zimene zingachititse kuti timangidwe m’goli ndi anthu osakhulupirira (Onanindime 10)

TISALOLE KUTI MTIMA WATHU UYAMBE KUDZIKUZA

11, 12. (a) Kodi Hezekiya anachita chiyani posonyeza zimene zinali mu mtima mwake? (b) N’chifukwa chiyani Mulungu anakhululukira Hezekiya?

11 Kodi tingaphunzire chiyani kwa Hezekiya? Pa nthawi ina, Mulungu amene amafufuza mitima anathandiza Hezekiya kudziwa zimene zinali mu mtima mwake. (Werengani 2 Mbiri 32:31.) Hezekiya atadwala kwambiri, Mulungu anamupatsa chizindikiro choti achira. Chizindikiro chake chinali mthunzi umene unabwerera m’mbuyo masitepe 10. Mwana wa mfumu ya ku Babulo anafuna kudziwa zambiri za chizindikirocho, choncho anatumiza anthu kuti akamufunse Hezekiya. (2 Maf. 20:8-13; 2 Mbiri 32:24) Mulungu ‘atamusiya’ kuti asonyeze zimene zinali mumtima mwake, Hezekiya anaonetsa anthu a ku Babulowo “zonse za m’nyumba yake yosungiramo chuma.” Apa Hezekiya sanachite zinthu mwanzeru ndipo anasonyeza kuti anali ndi mtima wonyada.

12 Baibulo silinena chimene chinayambitsa kuti Hezekiya akhale ndi mtima wonyada. Kodi chinali chifukwa choti anapambana pa nkhondo yolimbana ndi Asuri kapena chifukwa choti Mulungu anamuchiritsa mozizwitsa? Kodi mwina n’chifukwa choti anali “ndi chuma chambiri ndi ulemerero wochuluka zedi?” Sitikudziwa, koma n’zomvetsa chisoni kuti Hezekiya anadzikuza ndipo “sanabwezere zabwino” zimene Mulungu anamuchitira. Choncho ngakhale kuti Hezekiya anatumikira Mulungu ndi mtima wathunthu, nthawi ina anachita zinthu zosasangalatsa Yehova. Komabe kenako “anadzichepetsa” limodzi ndi anthu ake ndipo mkwiyo wa Yehova sunawagwere.—2 Mbiri 32:25-27; Sal. 138:6.

13, 14. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingasonyeze zomwe zili mu mtima mwathu? (b) Kodi tizitani anthu ena akatiyamikira pa zabwino zimene tachita?

13 Kodi kuwerenga nkhani ya Hezekiya komanso kuiganizira kwambiri kungatithandize bwanji? Kumbukirani kuti Hezekiya anayamba kusonyeza mtima wodzikuza Yehova atangomuthandiza kugonjetsa Senakeribu komanso atamuchiritsa matenda ake oopsa. Ndiye kodi ifeyo timatani ngati tachita zinazake zabwino ndipo anthu ena akutiyamikira? Zimene tingachite, zingasonyeze zomwe zili mu mtima mwathu. Mwachitsanzo, m’bale wina angakambe bwino nkhani yake pamsonkhano ndipo anthu ambiri angamuyamikire. Kodi pamenepa angatani?

14 Anthu akatiyamikira pa zabwino zomwe tachita, tiyenera kukumbukira mawu a Yesu akuti: “Mukachita zonse zimene munapatsidwa ngati ntchito yanu, muzinena kuti, ‘Ife ndife akapolo opanda pake. Tangochita zimene tinayenera kuchita.’” (Luka 17:10) Ndiye kodi tingatani kuti tisachite zinthu ngati Hezekiya? Paja Hezekiya atadzikuza, anasonyeza kuti sanayamikire zimene Yehova anamuchitira. Tikamaganizira kwambiri zimene Mulungu watichitira, tingapewe mtima wonyada umene iye amadana nawo. M’malomwake tingamalankhule zinthu zosonyeza kuti timayamikira Yehova. Tizikumbukiranso kuti iye ndi amene anatipatsa Baibulo komanso mzimu woyera kuti uzitithandiza kuchita bwino zinthu.

TIZIKHALA OSAMALA POSANKHA ZOCHITA

15, 16. N’chiyani chinachititsa kuti Yehova asateteze Yosiya?

15 Pomaliza tiyeni tikambirane zimene tingaphunzire pa zimene zinachitikira Mfumu Yosiya. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iye agonjetsedwe n’kufa? (Werengani 2 Mbiri 35:20-22.) Yosiya “anapita kukamenyana” ndi Mfumu Neko ya ku Iguputo ngakhale kuti mfumuyo inanena kuti sinabwere kudzamenyana ndi iyeyo. Baibulo limanena kuti mawu a Neko anali “ochokera pakamwa pa Mulungu.” Ndiye n’chifukwa chiyani Yosiya anapita kukamenyana ndi Neko? Baibulo silinena chifukwa chake.

16 Koma kodi Yosiya akanadziwa bwanji kuti mawu a Neko analidi ochokera kwa Yehova? Iye akanatha kufunsa Yeremiya, yemwe anali mneneri wokhulupirika. (2 Mbiri 35:23, 25) Koma palibe umboni woti anachita zimenezi. Chinanso chimene akanachiganizira ndi choti Neko ankapita ku Karikemisi kumenyana ndi “mtundu wina” osati Yerusalemu. Ndipotu nkhaniyi sinkakhudza dzina la Yehova chifukwa Neko sananyoze Yehova kapena anthu ake. Choncho Yosiya sanaganize bwino popita kukamenyana ndi Neko ndipo Yehova sanamuteteze. Ndiye kodi tingaphunzirepo chiyani? Tikakumana ndi vuto tizifufuza kaye maganizo a Yehova pa nkhaniyo.

17. Tikakhala ndi vuto, kodi tingatani kuti tisalakwitse zinthu ngati mmene Yosiya anachitira?

17 Tikakumana ndi vuto tiyenera kufufuza mfundo zonse za m’Baibulo zimene zikukhudzana ndi vutolo n’kuona kuti tingazitsatire bwanji. Nthawi zina tingafunike kufunsa nzeru kwa akulu. N’zoona kuti ifeyo tingadziwe zinthu zina zokhudza nkhaniyo ndipo mwina tafufuza kale mfundo zina. Koma n’kutheka kuti pangakhale mfundo zinanso zimene akulu angatithandize kuti tiziganizire. Tiyerekeze kuti pali mlongo wina amene mwamuna wake si Mboni. Mlongoyu akudziwa kuti ayenera kumalalikira uthenga wabwino. (Mac. 4:20) Ndiyeno wakonza zoti tsiku lina adzalowe mu utumiki. Koma mwamuna wake akufuna kuti pa tsikulo adzapitire limodzi kwinakwake. Mwamunayo akuona kuti n’kale pamene anakhalapo ndi nthawi yochita zinthu limodzi. Mkaziyo angaganizire lamulo la Yesu loti tiziphunzitsa anthu komanso mfundo yakuti tiyenera kumvera Mulungu. (Mat. 28:19, 20; Mac. 5:29) Koma angachitenso bwino kuganizira mfundo yakuti akazi ayenera kugonjera amuna awo ndiponso azikhala ololera. (Aef. 5:22-24; Afil. 4:5) Kodi mwamuna wakeyo amamuletsa kupita kolalikira kapena akungofuna kuti pa tsikuli asachoke kuti achitire limodzi zinthu zina? Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti tiyenera kukhala osamala pochita zinthu kuti tizikhala ndi chikumbumtima chabwino potumikira Mulungu.

PITIRIZANI KUTUMIKIRA YEHOVA NDI MTIMA WATHUNTHU

18. Kodi zitsanzo za mafumu 4 amene takambirana m’nkhaniyi zakuthandizani bwanji?

18 Popeza si ife angwiro, kupanda kusamala nafenso tingalakwitse zinthu zina ngati mmene zinaliri ndi mafumu 4 amene takambirana m’nkhaniyi. Mwina tingayambe (1) kudalira nzeru zathu, (2) kugwirizana ndi anthu olakwika, (3) kukhala ndi mtima wodzikuza kapena (4) kusankha zochita tisanafufuze maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Tikuthokoza kwambiri kuti Yehova ndi wabwino ndipo angathe kuona zabwino mwa ife ngati mmene anachitira ndi mafumu 4 aja. Yehova amadziwa kuti timamukonda komanso timafuna kumutumikira ndi mtima wonse. Choncho watipatsa zitsanzo kuti zitithandize kupewa kulakwitsa zinthu kwambiri. Tiyeni tiziganizira kwambiri za nkhani zimenezi ndipo tizithokoza Yehova pochititsa kuti zilembedwe m’Baibulo.