Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YOPHUNZIRA 4

NYIMBO NA. 18 Tikuthokoza Chifukwa cha Dipo

Kodi Dipo Limatiphunzitsa Chiyani?

Kodi Dipo Limatiphunzitsa Chiyani?

“Zimene Mulungu anachita potisonyeza chikondi chake.”​—1 YOH. 4:9.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Munkhaniyi tiona mmene dipo limasonyezera makhalidwe abwino a Yehova Mulungu komanso Yesu Khristu.

1. Kodi kupezeka pa Mwambo Wokumbukira Imfa ya Khristu chaka chilichonse kumatithandiza bwanji?

 MUNGAVOMEREZE kuti dipo ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri. (2 Akor. 9:15) Chifukwa chakuti Yesu anapereka moyo wake, mukhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu. Mungakhalenso ndi chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha. Mpake kuti tiyenera kumayamikira Yehova potipatsa dipo chifukwa chakuti amatikonda. (Aroma 5:8) Pofuna kutithandiza kuti tiziyamikira dipo komanso kuti tisamalione mopepuka, Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake.—Luka 22:19, 20.

2. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?

2 Chaka chino, mwambo wa Chikumbutso udzachitika Loweruka pa 12 April 2025. Mosakayikira, tonsefe tikukonza zoti tidzapezekepo. Pa nyengo ya Chikumbutsoyi, tidzapindula kwambiri tikamaganizira a zimene Yehova ndi Mwana wake anatichitira. Munkhaniyi tikambirana zimene dipo limatiphunzitsa zokhudza Yehova ndi Mwana wake. Nkhani yotsatira idzatithandiza kumvetsa mmene dipo limatithandizira komanso mmene tingasonyezere kuti timaliyamikira.

ZIMENE DIPO LIMATIPHUNZITSA ZOKHUDZA YEHOVA

3. Kodi imfa ya munthu mmodzi ingapulumutse bwanji anthu mamiliyoni ambiri? (Onaninso chithunzi.)

3 Dipo limatiphunzitsa kuti Yehova ndi wachilungamo. (Deut. 32:4) Kodi limatiphunzitsa bwanji zimenezi? Taganizirani izi: Chifukwa cha kusamvera kwa Adamu, tinatengera uchimo womwe umachititsa kuti tizifa. (Aroma 5:12) Kuti atipulumutse ku uchimo ndi imfa, Yehova anakonza zoti Yesu apereke dipo. Koma kodi nsembe ya munthu mmodzi wangwiro ikanapulumutsa bwanji anthu mamiliyoni ambiri? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Popeza kusamvera kwa munthu mmodziyo [Adamu] kunachititsa kuti ambiri akhale ochimwa, kumvera kwa munthu mmodziyu [Yesu] kudzachititsanso kuti ambiri akhale olungama.” (Aroma 5:19; 1 Tim. 2:6) Tingati kusamvera kwa munthu mmodzi yemwe anali wangwiro, kunachititsa kuti tikhale akapolo a uchimo ndi imfa. Choncho panafunikanso munthu mmodzi womvera yemwe ndi wangwiro kuti tipulumutsidwe.

Munthu mmodzi anachititsa kuti tikhale akapolo a uchimo ndi imfa, choncho munthu mmodzinso anachititsa kuti timasulidwe (Onani ndime 3)


4. N’chifukwa chiyani Yehova sanangolola kuti ana omvera a Adamu akhale ndi moyo mpaka kalekale?

4 Kodi Yesu anafunikadi kufa kuti atipulumutse? Kodi Yehova sakanatha kungolola ana omvera a Adamu kuti akhale ndi moyo wosatha? Mwina anthufe tingaganize kuti imeneyi ikanakhala njira yabwino yothetsera vutoli. Koma zimenezi si zogwirizana ndi chilungamo cha Yehova. Popeza Yehova ndi wachilungamo, sakanangolekerera kusamvera mwadala kwa Adamu.

5. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti nthawi zonse Yehova azichita zoyenera?

5 Kodi chikanachitika n’chiyani ngati Yehova akanapanda kupereka dipo, n’kunyalanyaza chilungamo chake polola kuti ana a Adamu akhalebe ndi moyo mpaka kalekale? Anthu akanakayikira kuti Mulungu adzachita chilungamo pa nkhani zinanso. Mwachitsanzo, mwina akanamadzifunsa kuti, ‘Kodi iye adzakwaniritsadi zimene analonjeza?’ Koma sitiyenera kudera nkhawa kuti zimenezo zingachitike. Zimene Yehova anachita polola kuti Mwana wake wokondedwa aphedwe, zimatitsimikizira kuti iye nthawi zonse adzachita zoyenera.

6. Kodi dipo limasonyeza bwanji kuti Yehova amatikonda? (1 Yoh. 4:9, 10)

6 N’zoona kuti dipo limatithandiza kumvetsa kuti Yehova ndi wachilungamo, koma kwenikweni limatithandizanso kudziwa kuti iye amatikonda kwambiri. (Yoh. 3:16; werengani 1 Yohane 4:9, 10.) Zimene timaphunzira zokhudza dipo, zimasonyeza kuti Yehova samangofuna kuti tikhale ndi moyo wosatha, koma amafunanso kuti tikhale m’banja lake. Taganizirani izi: Adamu atachimwa, Yehova sanamulolenso kuti akhale m’banja lake. Choncho tonsefe tinabadwira kunja kwa banja la Mulungu. Koma chifukwa cha dipo, Yehova amatikhululukira machimo athu ndipo pa nthawi yake adzabwezeretsa m’banja lake onse omwe amamukhulupirira komanso kumumvera. Ngakhale panopa, tikhoza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso Akhristu anzathu. Kunena zoona, Yehova amatikonda kwambiri.—Aroma 5:10, 11.

7. Kodi kuvutika kwa Yesu kumatithandiza bwanji kumvetsa kuti Yehova amatikonda kwambiri?

7 Tingamvetse bwino kuti Yehova amatikonda, tikaganizira mmene zinamupwetekera kuti apereke dipo. Satana amanena kuti palibe mtumiki wa Yehova yemwe angakhalebe wokhulupirika ngati atakumana ndi mavuto aakulu. Pofuna kutsutsa bodza limeneli, Yehova analola kuti Yesu avutike asanafe. (Yobu 2:1-5; 1 Pet. 2:21) Yehova ankaona pamene Yesu ankanyozedwa ndi adani ake, kukwapulidwa ndi asilikali komanso kukhomereredwa pamtengo. Kenako Yehova anaona Mwana wake wokondedwayo akuvutika ndi ululu mpaka kufa. (Mat. 27:28-31, 39) Yehova anali ndi mphamvu yoletsa zonsezi kuti zisachitike. Mwachitsanzo, pamene anthu otsutsawo ananena kuti: “Mulunguyo amupulumutse ngati akumufunadi,” iye akanatha kuchita zimenezi. (Mat. 27:42, 43) Koma ngati Mulungu akanachita zimenezi, dipo silikanaperekedwa ndipo tikanakhalabe opanda chiyembekezo. Choncho Yehova analola kuti Mwana wake avutike mpaka kufa.

8. Kodi Yehova anamva kupweteka poona Mwana wake akuvutika? Fotokozani. (Onaninso chithunzi.)

8 Tisamaganize kuti popeza Mulungu ndi wamphamvuyonse ndiye kuti samamva kupweteka. Anthufe tinalengedwa m’chifaniziro chake, choncho ngati ifeyo timamva kupweteka, nayenso amamva kupweteka mumtima. Baibulo limafotokoza kuti iye ‘amakhumudwa’ komanso ‘kumva chisoni.’ (Sal. 78:40, 41) Taganiziraninso nkhani ya Abulahamu ndi Isaki. Mwina mungakumbukire kuti Abulahamu analamulidwa kuti apereke nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. (Gen. 22:9-12; Aheb. 11:17-19) Taganizirani mmene zinamupwetekera Abulahamu pamene ankakonzekera kupha Isaki ndi mpeni. Nayenso Yehova ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri kuona Mwana wake akuzunzidwa ndi anthu oipa mpaka kufa.—Onani pa jw.org vidiyo yakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo—Abulahamu, Mbali Yachiwiri.

Zinamupweteka Yehova poona Mwana wake akuvutika (Onani ndime 8)


9. Kodi lemba la Aroma 8:32, 38, 39 limakuthandizani bwanji kumvetsa kuti Yehova amakukondani kwambiri inuyo komanso Akhristu anzanu?

9 Dipo limatiphunzitsa kuti Yehova amatikonda kwambiri, moti palibe wachibale kapena mnzathu amene angatikonde choncho. (Werengani Aroma 8:​32, 38, 39.) Sitikayikira kuti Yehova amatikonda kwambiri kuposa mmene timadzikondera tokha. Kodi inuyo mukufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale? Dziwani kuti Yehova ndi amene amafuna kwambiri zimenezo. Kodi mumafuna kuti mukhululukidwe machimo anu? Yehova ndi amene amafuna kwambiri kukukhululukirani. Chomwe amangofuna n’chakuti tiziyamikira mphatso ya dipo, tizimukhulupirira komanso tizimumvera. Kunena zoona, dipo limasonyeza kuti Mulungu amatikonda kwambiri. Ndipotu m’dziko latsopano, tidzaphunzira zambiri zokhudza chikondi cha Yehova.—Mlal. 3:11.

ZIMENE DIPO LIMATIPHUNZITSA ZOKHUDZA YESU

10. (a) Kodi ndi chiyani chinkamudetsa nkhawa kwambiri Yesu akaganizira za imfa yake? (b) Kodi Yesu anayeretsa bwanji dzina la Yehova? (Onaninso bokosi lakuti “ Kukhulupirika kwa Yesu Kunayeretsa Dzina la Yehova.”)

10 Yesu ankadera nkhawa kwambiri zimene anthu aziganiza zokhudza Atate wake. (Yoh. 14:31) Yesu ankadera nkhawa kuti kuimbidwa mlandu kuti ndi wonyoza Mulungu komanso woukira, kunyozetsa dzina la Atate wake. N’chifukwa chake iye anapemphera kuti: “Atate wanga, ngati n’kotheka lolani kuti kapu iyi indipitirire.” (Mat. 26:39) Pokhalabe wokhulupirika kwa Yehova mpaka imfa, Yesu anasonyeza kuti zimene Satana ananena zokhudza Atate wake ndi zabodza.

11. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda kwambiri anthu? (Yoh. 13:1)

11 Dipo limatiphunzitsanso kuti Yesu amakonda kwambiri anthu, makamaka otsatira ake. (Miy. 8:31; werengani Yohane 13:1.) Mwachitsanzo, Yesu ankadziwa kuti zina zomwe adzakumane nazo pa utumiki wake zidzakhala zovuta kwambiri, makamaka imfa yake. Komabe, Yesu anachita zonsezi, osati chifukwa chakuti ndi zimene Yehova anamutuma kudzachita, koma chifukwa chakuti ankakonda anthu. Choncho iye ankaika mtima wake wonse pa ntchito yolalikira, kuphunzitsa ndi kutumikira ena. Ngakhale pa tsiku limene anaphedwa, Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake, kuwapatsa malangizo komanso kuwauza mawu olimbikitsa. (Yoh. 13:12-15) Kenako Yesu ali pamtengo wozunzikirapo, anathandiza chigawenga kukhala ndi chiyembekezo komanso anakonza zoti mayi ake azisamaliridwa. (Luka 23:42, 43; Yoh 19:26, 27) Apa Yesu anasonyeza kuti amakonda anthu, osati potifera pokha, koma pa moyo wake wonse.

12. Kodi Yesu akutithandiza bwanji masiku ano?

12 Ngakhale kuti Khristu anatifera “kamodzi kokha basi,” pali zambiri zimene akuchita potithandiza. (Aroma 6:10) Kodi ndi zinthu ziti zimene akuchita? Iye akugwirabe ntchito kuti atipatse zinthu zabwino zimene zimatheka chifukwa cha dipo. Mwachitsanzo, iye amagwira ntchito mwakhama monga Mfumu, Mkulu wa Ansembe komanso mutu wa mpingo. (1 Akor. 15:25; Aef. 5:23; Aheb. 2:17) Iye akuyang’anira ntchito yosonkhanitsa odzozedwa komanso a khamu lalikulu ndipo adzamaliza kuchita zimenezi chisautso chachikulu chisanathe. b (Mat. 25:32; Maliko 13:27) Yesu amaonetsetsanso kuti atumiki ake okhulupirika akulandira chakudya chauzimu chokwanira m’masiku otsiriza ano. (Mat. 24:45) Ndipo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000, iye adzapitiriza kutithandiza. Apatu Yehova anapereka Mwana wake ndi mtima wonse kuti atithandize.

MUSASIYE KUPHUNZIRA

13. Kodi mungatani kuti muphunzire zambiri zokhudza chikondi cha Mulungu ndi Khristu?

13 Mungaphunzire zambiri zokhudza chikondi cha Yehova Mulungu ndi Khristu Yesu mukamapitiriza kuganizira zimene anakuchitirani. Mwina pa nyengo ya Chikumbutso ya chaka chino mungawerenge mosamala buku limodzi kapena angapo a Uthenga Wabwino. Musamawerenge machaputala ambiri pa nthawi imodzi. Koma muziwerenga pang’onopang’ono ndipo muzifufuza zifukwa zina zomwe zingakuchititseni kuti muzikonda Yehova ndi Yesu. Komanso muziyesetsa kuuzako ena zimene mwaphunzira.

14. Mogwirizana ndi Salimo 119:97 ndi mawu a m’munsi, kodi kufufuza kungatithandize bwanji kuti tiphunzire zambiri zokhudza dipo komanso zinthu zina? (Onaninso chithunzi.)

14 Ngati mwakhala m’choonadi kwa zaka zambiri mwina mungaone kuti simungapeze mfundo zina zatsopano zokhudza chilungamo cha Mulungu, chikondi chake komanso dipo. Koma zoona n’zakuti sitidzamaliza kuphunzira zokhudza nkhani zimenezi ndi zinanso. Ndiye kodi muyenera kuchita chiyani? Muziwerenga komanso kuphunzira nkhani za m’Baibulo zomwe zimapezeka m’mabuku athu. Mukapeza nkhani yomwe simukuimvetsa, muzifufuza. Ndipo tsiku lonse muziganizira zimene mwaphunzira zokhudza Yehova, Mwana wake komanso mmene amakukonderani.—Werengani Salimo 119:97 ndi mawu a m’munsi.

Ngakhale kuti takhala m’choonadi kwa nthawi yaitali, tingathe kumayamikira kwambiri mphatso ya dipo (Onani ndime 14)


15. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kufufuza mfundo zamtengo wapatali zopezeka m’Mawu a Mulungu?

15 Musamagwe ulesi ngati nthawi zina simukupeza mfundo zatsopano kapena zochititsa chidwi pamene mukuwerenga kapena kufufuza. Pa nthawiyi mumakhala ngati munthu amene akufufuza golide. Anthu omwe akufufuza golide amakhala maola mwinanso masiku asanapeze ngakhale kachidutswa ka golide. Iwo amalezabe mtima chifukwa amadziwa kuti kachidutswa kalikonse ka golide ndi kamtengo wapatali. Mofanana ndi zimenezi, mfundo iliyonse ya m’Baibulo imene mungapeze ndi yamtengo wapatali. (Sal. 119:127;Miy. 8:10) Choncho muzileza mtima ndipo muzipitiriza kuwerenga Baibulo nthawi zonse.—Sal. 1:2.

16. Kodi tingatsanzire bwanji Yehova ndi Yesu?

16 Mukamaphunzira, muziganizira mmene mungagwiritsire ntchito zimene mukuphunzirazo. Mwachitsanzo, muzitsanzira chilungamo cha Yehova pochita zinthu mopanda tsankho ndi anthu ena. Muzitsanzira mmene Yesu ankakondera Atate wake ndi anthu ena pokhala wofunitsitsa kuchita zimene Yehova amafuna komanso kuthandiza anthu ena ngakhale pamene kuchita zimenezo kuli kovuta. Muzitsanziranso Yesu polalikira kwa ena n’cholinga choti nawonso akhale ndi mwayi wolandira mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova.

17. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

17 Tikamayesetsa kumvetsa komanso kuyamikira dipo, m’pamenenso timakonda kwambiri Yehova ndi Mwana wake. Zotsatira zake n’zakuti iwonso adzayamba kutikonda kwambiri. (Yoh. 14:21; Yak. 4:8) Choncho tiyeni tipitirize kugwiritsa ntchito zonse zimene Yehova watipatsa kuti tiphunzire zokhudza dipo. Munkhani yotsatira tidzakambirana madalitso ena omwe timapeza chifukwa cha dipo komanso mmene tingasonyezere kuti timayamikira chikondi cha Yehova.

NYIMBO NA. 107 Tizitsanzira Chikondi Cha Mulungu

a TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kuganizira mozama kumatanthauza kuika maganizo onse pa nkhani inayake.

b Kusonkhanitsa “zinthu zakumwamba” komwe Paulo anatchula pa Aefeso 1:10, n’kosiyana ndi kusonkhanitsa “osankhidwa” ake komwe Yesu anatchula pa Mateyu 24:31 ndi Maliko 13:27. Paulo ankanena za nthawi imene Yehova amasankha anthu oti akalamulire limodzi ndi Yesu powadzoza ndi mzimu wake woyera. Pomwe Yesu ankanena za nthawi imene odzozedwa omwe adzakhale adakali padzikoli adzasonkhanitsidwe kupita kumwamba pa nthawi ya chisautso chachikulu.