Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malowolo ankaphatikizapo zinthu monga ziweto

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankapereka malowolo?

KALERO, malowolo ankaperekedwa kubanja la mkwatibwi ngati mwamuna ndi mkazi agwirizana kuti akwatirane. Zinthu zimene zinkaperekedwa monga malowolo zinali ziweto, ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Nthawi zinanso munthu ankangogwira ntchito, ngati mmene zinakhalira ndi Yakobo yemwe anavomera kugwirira ntchito bambo ake a Rakele kwa zaka 7 kuti akwatire Rakeleyo. (Gen. 29:17, 18, 20) N’chifukwa chiyani anthu ankachita mwambo umenewu?

Katswiri wina wa maphunziro a Baibulo dzina lake Carol Meyers ananena kuti: “Malowolo ankaperekedwa ku banja la mkwatibwi pofuna kupepesa banjalo chifukwa cha kuchoka kwa mwana wawo yemwe ankawathandiza pantchito zosiyanasiyana monga zaulimi.” Malowolo ankathandizanso kuti mabanja awiri omwe akhala pa ubale chifukwa cha ukwatiwo akhale ogwirizana. Zimenezi zinkathandiza kuti mabanja awiriwa azithandizana akakumana ndi mavuto. Kuwonjezera pamenepo malowolo ankathandiza anthu ena kudziwa kuti mkazi wapeza mwamuna ndipo akuyembekezeredwa kuchoka m’manja mwa bambo ake, n’kumakasamalidwa ndi kutetezedwa ndi mwamuna wake.

Kupereka malowolo sikunkatanthauza kuti mkazi anali m’gulu la zinthu zimene zikanatha kugulidwa kapena kugulitsidwa. Buku lina linanena kuti: “Kupereka ndalama kapena zinthu zina kubanja la mkazi kumachititsa anthu kuona ngati Aisiraeli ankachita malonda pankhani ya ukwati. Koma zikuoneka kuti malowolo sanali malipiro ogulira mkazi, m’malo mwake ankaoneka kuti ndi chipepeso kubanja la mkaziyo.”​—Ancient Israel​—Its Life and Institutions.

Masiku ano m’mayiko ena anthu amachitabe mwambo wopereka malowolo. Makolo a Chikhristu omwe amafuna kulandira malowolo ayenera kuyesetsa kuti ‘anthu onse adziwe kuti ndi ololera,’ popewa kunena kuti apatsidwe ndalama zambiri. (Afil. 4:5; 1 Akor. 10:32, 33) Akatero iwo amasonyeza kuti si “okonda ndalama” kapena kuti adyera. (2 Tim. 3:2) Kuwonjezera pamenepo ngati makolo a Chikhristu sanapemphe anzawo kuti apereke malowolo okwera, mwamuna sangakakamizike kuimitsa kaye ukwati mpaka atapeza ndalama yokwanira yolipilira malowolowo. Zingathandizenso kuti mwamuna asasiye utumiki wake monga mpainiya, n’kukayamba ntchito n’cholinga choti apeze ndalama zokalipira malowolo omwe ndi okwera.

M’mayiko ena muli malamulo okhudza kupereka malowolo. M’mayiko amenewo makolo a Chikhristu amachita zinthu mogwirizana ndi malamulowo. Chifukwa chiyani? Chifukwa Mawu a Mulungu amafuna kuti Akhristu “azimvera olamulira akuluakulu” komanso malamulo omwe sasemphana ndi malamulo a Mulungu.​—Aroma 13:1; Mac. 5:29.