Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Choonadi Chonena za Mulungu Komanso Khristu

Choonadi Chonena za Mulungu Komanso Khristu

Ngakhale kuti anthu amalambira milungu yambiri, pali Mulungu woona mmodzi yekha. (Yohane 17:3) Iye ndi “Wamkulukulu” komanso ndi Mlengi wa zamoyo zonse ndiponso zinthu zina zonse. Iye yekha ndi amene tiyenera kumulambira.​—Danieli 7:18; Chivumbulutso 4:11.

Kodi Mulungu Ndi Ndani?

Dzina la Mulungu limapeza m’mipukutu yoyambirira PAFUPIFUPI KA 7,000

YEHOVA Ndi dzina la Mulungu

AMBUYE, MULUNGU, ATATE​—Mayina ena udindo a Yehova

Kodi Dzina la Mulungu Ndi Ndani? Mwiniwakeyo amatiuza kuti: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) Dzina la Mulungu limapezeka pafupifupi ka 7,000 m’Baibulo. Komabe m’Mabaibulo ena anachotsamo dzinali n’kuikamo mayina audindo monga lakuti, “Ambuye.” Mulungu amafuna kuti mukhale mnzake, choncho akukulimbikitsani kuti ‘muziitana pa dzina lake.’​—Salimo 105:1.

Mayina Audindo a Yehova. Baibulo limamutchula Yehova ndi mayina audindo monga “Mulungu,” “Mlengi,” “Atate,” “Ambuye,” komanso “Wamkulu Koposa.” M’Baibulo muli mapemphero a anthu ambiri omwe popemphera ankatchula Mulungu pogwiritsa ntchito dzina lake lenileni komanso mayina ake audindo kapena aulemu.​—Danieli 9:4.

Mmene Mulungu Alili. Mulungu ndi mzimu choncho sitingathe kumuona. (Yohane 4:24) Baibulo limanena kuti “palibe munthu anaonapo Mulungu.” (Yohane 1:18) Limatiuzanso kuti zochita za anthu zikhoza kumukhumudwitsa kapena ‘kumusangalatsa.’​—Miyambo 11:20; Salimo 78:40, 41.

Makhalidwe Ake Abwino Kwambiri. Mulungu alibe tsankho ndipo amakonda anthu onse mosatengera mtundu wawo kapena mbiri yawo. (Machitidwe 10:34, 35) Komanso iye ndi “wachifundo ndi wachisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.” (Ekisodo 34:6, 7) Komabe ali ndi makhalidwe 4 omwe ndi apadera kwambiri.

Mphamvu. Popeza ndi “Mulungu Wamphamvuyonse,” ali ndi mphamvu zopanda malire moti angathe kukwaniritsa chilichonse chomwe walonjeza.​—Genesis 17:1.

Nzeru. Mulungu ali ndi nzeru kuposa wina aliyense. N’chifukwa chake Baibulo limamutchula kuti “wanzeru yekhayo.”​—Aroma 16:27.

Chilungamo. Nthawi zonse Mulungu amachita zoyenera. Zochita zake ndi ‘zangwiro’ ndipo “sachita chosalungama.”​—Deuteronomo 32:4.

Chikondi. Baibulo limati “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Sikuti Mulungu amangosonyeza chikondi, koma iyeyo ndi chikondi. Chilichonse chimene amachita, amachichita chifukwa cha chikondi chake chachikulu ndipo ifeyo timapindula kwambiri ndi zimene amachitazo.

Ubwenzi wa Mulungu ndi Anthu. Mulungu ndi Atate wathu wakumwamba wachikondi. (Mateyu 6:9) Ngati titamamukhulupirira tikhoza kukhala mabwenzi ake. (Salimo 25:14) Ndipotu Mulungu amakuuzani kuti muzimuyandikira m’pemphero komanso ‘muzimutulira nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7; Yakobo 4:8.

Kodi Mulungu Ndi Yesu Ndi Osiyana Bwanji?

Yesu Si Mulungu. Yesu ndi wapadera chifukwa ndi iye yekha amene Mulungu anamulenga mwachindunji. N’chifukwa chake Baibulo limati iye ndi Mwana wa Mulungu. (Yohane 1:14) Yehova atalenga Yesu, anamugwiritsa ntchito ngati “mmisiri waluso” polenga zinthu zina zonse.​—Miyambo 8:30, 31; Akolose 1:15, 16.

Yesu Khristu sananenepo kuti ndi Mulungu. M’malomwake iye ananena kuti: “Ndine nthumwi. Iyeyu [Mulungu] anandituma ine.” (Yohane 7:29) Pamene ankalankhula ndi wophunzira wake wina, Yesu anatchula Yehova kuti “Atate wanga ndi Atate wanu” komanso “Mulungu wanga ndi Mulungu wanu.” (Yohane 20:17) Yesu atamwalira Yehova anamuukitsa kuti apite kumwamba ndipo anam’patsa ulamuliro kudzanja lake lamanja.​—Mateyu 28:18; Machitidwe 2:32, 33.

Yesu Khristu Angakuthandizeni Kuti Mukhale pa Ubwenzi Ndi Mulungu

Yesu anabwera padziko lapansi kudzatiphunzitsa zokhudza Atate wake. Ponena za Yesu, Yehova anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, muzimumvera.” (Maliko 9:7) Yesu amadziwa bwino kwambiri Mulungu kuposa aliyense. Iye anati: “Atatewo palibe amene akuwadziwa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululira za Atatewo.”​—Luka 10:22.

Yesu amasonyeza bwino makhalidwe a Mulungu. Yesu amatsanzira kwambiri makhalidwe a Atate wake moti ananena kuti: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yohane 14:9) Yesu ankachita komanso kulankhula zinthu zosonyeza kuti Atate wake ndi wachikondi ndipo zimenezi zinathandiza anthu kuti ayandikire Mulungu. Iye anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Ananenanso kuti: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri. Yehova akufufuza anthu ngati inuyo amene akufuna kudziwa zoona zokhudza iyeyo.