Muzipemphera Kuti Mulungu Akudalitseni
Pemphero ndi mphatso yapadera imene Mulungu anapatsa anthu kuti azitha kulankhula naye ndi kufotokoza mmene akumvera. Mneneri Davide anapempha kuti: “Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.” (Salimo 65:2) Koma kodi tizipemphera bwanji kuti Mulungu azimva mapemphero athu komanso kutidalitsa?
MUZIPEMPHERA MODZICHEPETSA KOMANSO MOCHOKERA PANSI PA MTIMA
Mukamapemphera kwa Mulungu ‘mumamukhuthulira za mumtima mwanu’ ndi kumuuza mmene mukumvera. (Salimo 62:8) Mulungu Wamphamvuyonse amakonda mapemphero ochokera pansi pa mtima.
MUZITCHULA DZINA LA MULUNGU POPEMPHERA
Ngakhale kuti Mulungu ali ndi mayina audindo ambiri, dzina lake lenileni ndi limodzi lokha. Paja iye anati: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.” (Yesaya 42:8) M’Malemba Opatulika, dzina lakuti Yehova limapezeka nthawi zosachepera 7,000. Aneneri ambiri ankatchula dzina lenileni la Mulungu popemphera. Abulahamu anati: “Chonde Yehova, . . . ndiloleni ndilankhulebe [ndi inu].” (Genesis 18:30) Nafenso tizitchula dzina la Mulungu lakuti Yehova tikamapemphera.
MUZIPEMPHERA M’CHINENERO CHANU
Mulungu amamvetsa maganizo athu komanso mmene tikumvera posatengera chinenero chathu. Mawu ake amatitsimikizira kuti: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Komabe, kuti Mulungu atidalitse tiyenera kuchita zambiri kuwonjezera pa kupemphera. M’nkhani zotsatirazi tiona zimene tiyenera kuchita.