Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Amene Mumamukonda Akamwalira

Munthu Amene Mumamukonda Akamwalira

Vanessa, yemwe amakhala ku Australia, anati: “Mchimwene wanga atamwalira mwadzidzidzi ndinasowa chochita. Patatha miyezi ingapo, ndinkamuganizirabe ndipo ndinkadwala komanso ndinkamva ululu ngati ndabaidwa ndi mpeni. Nthawi zina ndinkakwiya ndipo ndinkadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani mchimwene wanga anamwalira?’ Komanso ndinkadziimba mlandu ndikaganizira kuti ndinalibe nthawi yokwanira yocheza naye.”

N’KUTHEKA kuti inunso munthu amene munkamukonda atamwalira munamva chisoni kwambiri, munkaona kuti mwatsala nokha komanso munasowa chochita. Mwinanso munkakhala wokwiya, munkadziimba mlandu komanso munali ndi mantha n’kumaona kuti bola kungofa.

Dziwani kuti si kulakwa kumva chisoni. Zimangosonyeza kuti munkamukonda kwambiri munthuyo. Koma kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuchepetsako chisoni pa nthawi yovutayi?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

N’kutheka kuti muli ndi chisoni chachikulu ndipo mukuona kuti chisoni chanu sichidzatha. Koma mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni:

MUSAMADZILETSE KUSONYEZA CHISONI

Anthu amasonyeza chisoni m’njira zosiyanasiyana ndipo ena amatenga nthawi kuti chisoni chawo chithe. Ndipotu kulira kumathandiza kuti munthu ayambe kumvako bwino. Vanessa yemwe tamutchula uja ananena kuti: “Ndinkalira, ndipo ndinkaona kuti zimenezi zinkandithandiza kwambiri.” Sofía yemwenso mng’ono wake anamwalira mwadzidzidzi anati: “Ngakhale kuti kuganizira zomwe zinachitikazo kunali kowawa ngati kutsuka pabala, kunandithandiza kuti ndiyambe kumvako bwino.”

MUZIFOTOKOZERA ENA MMENE MUKUMVERA

N’zoona kuti nthawi zina mungafune kukhala panokha. Koma muzikumbukira kuti chisoni chili ngati katundu wolemera woti simunganyamule nokha. Mnyamata wina wazaka 17 dzina lake Jared, yemwe bambo ake anamwalira, ananena kuti: “Ndinkafotokozera ena mmene ndinkamvera. Ngakhale kuti sindinkatha kufotokoza bwinobwino, ndimaona kuti zinandithandiza.” Janice amene tamutchula munkhani yoyamba uja, ananena kuti: “Kufotokozera ena mmene ndikumvera kunandithandiza kwambiri. Ndinaona kuti ena akumvetsa mavuto anga ndipo sindili ndekha.”

MUZILOLA KUTI ENA AKUTHANDIZENI

Dokotala wina anati: “Anamfedwa amene amalola kuti anzawo kapena achibale awathandize pa nthawi imene wachibale wawo wangomwalira kumene, savutika kwambiri ndi chisoni pa nthawi yonse yovutayo.” Choncho muziuza anzanu zimene mungafune kuti akuthandizeni. Iwo amafuna kukuthandizani koma mwina sangadziwe kuti akuthandizeni bwanji.​—Miyambo 17:17.

MUZILANKHULA NDI MULUNGU M’PEMPHERO

Tina ananena kuti: “Mwamuna wanga atamwalira ndi khansa, ndinkasowa womuuza zakukhosi, choncho ndinkapemphera kwa Mulungu n’kumufotokozera chilichonse. M’mawa wa tsiku lililonse ndinkamupempha kuti andithandize pa tsikulo. Mulungu anandithandiza m’njira zambiri moti sindingathe kutchula zonse.” Tarsha yemwe mayi ake anamwalira iye ali ndi zaka 22 ananena kuti: “Kuwerenga Baibulo n’kumene kunandithandiza. Ndinkapeza mfundo zolimbikitsa zoti ndiziziganizira.”

MUZIYEREKEZERA ACHIBALE ANUWO ATAUKITSIDWA

Tina ananenanso kuti: “Poyamba chiyembekezo chakuti akufa adzauka sichinkandithandiza kwenikweni, chifukwa ndinkalakalaka nditaona mwamuna wanga nthawi yomweyo. Ana anganso ankafuna ataona bambo awo. Koma tsopano patha zaka 4, ndipo ndimaona kuti chiyembekezo chakuti akufa adzauka chimandithandiza kwambiri. Ndimaganizira mmene ndidzasangalalire mwamuna wanga akadzaukitsidwa ndipo zimenezi zimandithandiza kukhala ndi mtendere wamumtima komanso kukhala wosangalala.”

Sikuti chisoni chingathe kamodzinkamodzi. Komabe zimene Vanessa ananena n’zolimbikitsa. Iye anati: “Umaona ngati chisoni chako sichidzatha koma pang’ono ndi pang’ono chimatha ndipo umayambanso kusangalala.”

N’zoona kuti tingamamusowebe wachibale wathu amene wamwalira, koma zimenezi sizikutanthauza kuti palibenso chifukwa chokhalira ndi moyo. Mulungu angakuthandizeni kuti muzikhalabe wosangalala limodzi ndi anzanu ndi achibale anu. Ndipotu posachedwapa adzaukitsa anthu amene anamwalira. Iye akufuna kuti mudzakumbatiranenso ndi achibale anu. Pa nthawi imeneyo chisoni ndi kupweteka konse zidzatheratu.