1 | Pemphero—‘Muzimutulira Nkhawa Zanu Zonse’
BAIBULO LIMATI: ‘Muzimutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’—1 PETULO 5:7.
Tanthauzo Lake
Yehova Mulungu akukupemphani kuti muzimufotokozera mavuto ena aliwonse amene mukukumana nawo komanso zilizonse zomwe zikukudetsani nkhawa. (Salimo 55:22) Muzimufotokozera vuto lililonse lomwe mukukumana nalo kaya ndi lalikulu kapena laling’ono, chifukwa Yehova amationa kuti ndife ofunika. Choncho zilizonse zomwe zikutichitikira zimamukhudza. Ndiye kupemphera kwa iye, ndi njira yofunika kwambiri yokuthandizani kupeza mtendere wa m’maganizo.—Afilipi 4:6, 7.
Mmene Mfundo Zimenezi Zingakuthandizireni
Tikamalimbana ndi matenda ovutika maganizo, tikhoza kumadzimva kuti tili tokhatokha. Si nthawi zonse pamene anthu ena angamvetse zomwe tikukumana nazo. (Miyambo 14:10) Koma tikamapemphera kwa Mulungu moona mtima, n’kumamuuza mmene tikumvera, nthawi zonse iye amatimvetsera mokoma mtima ndiponso amatimvetsa. Yehova amationa, amadziwa mmene zikutipwetekera komanso mmene tikuvutikira ndipo amafuna kuti tizimuuza m’pemphero chilichonse chomwe chikutidetsa nkhawa.—2 Mbiri 6:29, 30.
Tikamapemphera kwa Yehova, timalimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti iye amasamala za ife. Tikhoza kumamva ngati mmene wamasalimo wina anamvera, pamene anapemphera kuti: “Mwaona kusautsika kwanga. Mwadziwa zowawa zimene zandigwera.” (Salimo 31:7) Kungodziwa kokha mfundo yakuti Yehova amadziwa mavuto amene tikulimbana nawo, kungatithandize kuti tipitirizebe kupirira. Komabe sikuti iye amangoona mavuto athu basi, koma amachitapo kanthu. Kuposa wina aliyense, iye amadziwa bwino mavuto amene tikukumana nawo komanso amatitonthoza ndi kutilimbikitsa kudzera m’Baibulo.