Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?
ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake ngati nyama kapena chinthu chinachake. Pamene ena amakhulupirira kuti munthu akafa, ndiye kuti zake zathera pomwepo. Nanga inuyo mumakhulupirira zotani?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Akufa sadziwa chilichonse.” (Mlaliki 9:5) Choncho munthu akamwalira, ndiye kuti kulibenso.
MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO
Adamu atamwalira anabwereranso kufumbi. (Genesis 2:7; 3:19) Masiku anonso anthu onse amene amamwalira, amabwerera kufumbi.—Mlaliki 3:19, 20.
Anthu amene amwalira amakhala kuti amasuka ku machimo awo. (Aroma 6:7) Umenewu ndi umboni wakuti munthu akamwalira, sapita kwinakwake kukalangidwa chifukwa cha machimo amene anachita.
Kodi anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo?
KODI MUNGAYANKHE KUTI . . .
Inde
Ayi
Mwina
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Kudzakhala kuuka.”—Machitidwe 24:15.
MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO
Nthawi zambiri Baibulo limayerekezera imfa ndi tulo. (Yohane 11:11-14) Mulungu adzaukitsa akufa ngati mmene timadzutsira munthu akagona.—Yobu 14:13-15.
M’Baibulo muli nkhani za anthu ambiri amene anaukitsidwa. Zimenezi zimatitsimikizira kuti Mulungu adzaukitsadi akufa.—1 Mafumu 17:17-24; Luka 7:11-17; Yohane 11:39-44.