NKHANI YA PACHIKUTO | KODI ZINTHU PADZIKOLI ZAFIKA POIPA KWAMBIRI
Kufufuza Mayankho
NGATI mumachita mantha mukawerenga kapena kumva nkhani inayake yoopsa, dziwani kuti si inu nokha. Mu 2014, a Barack Obama omwe anali mtsogoleri wa dziko la United States ananena kuti nkhani zochititsa mantha zomwe zikumalembedwa m’manyuzi, zikuchititsa anthu kuona kuti dzikoli lafika poipa kwambiri moti palibenso zomwe anthu angachite.
Komabe patangopita nthawi yochepa atalankhula mawuwa, mtsogoleriyu anafotokoza njira zatsopano zofuna kuthana ndi mavuto omwe akuchitika padzikoli. Mtsogoleriyu anayamikira zimene mayiko ena akuyesetsa kuchita pothana ndi mavutowa. Ananenanso kuti akutsimikiza kuti zinthu ziyambanso kuyenda bwino. Choncho tingati mtsogoleriyu anasonyeza kuti zinthu zomwe anthu akuyesetsa kuchita, zingateteze dzikoli n’kulipangitsa kukhala malo abwino kwambiri.
Ambiri amagwirizana ndi zomwe a Obama ananena. Mwachitsanzo pali anthu ambiri omwe amakhulupirira kuti njira za sayansi komanso kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga, kungathandize kuthetsa mavuto omwe akuchitika padzikoli. Katswiri wina wa luso la zopangapanga ananena motsimikiza kuti podzafika chaka cha 2030, “luso la zopangapanga lidzakhala litafika patali ndipo pofika mu 2045 zinthu zidzakhala bwino kwambiri.” Katswiriyu ananenanso kuti: “Panopa tikuchita bwino ndithu. Ngakhale kuti pali mavuto ena ndi ena koma sikuti n’zochita kudetsa nkhawa. Njira zolimbana ndi mavutowa zikuyenda bwino kwambiri.”
Kodi zinthu zaipa kufika pati? Kodi ndi zoona kuti dzikoli litha posachedwa? Ngakhale kuti asayansi ndi andale ena akunena kuti zinthu zikhala bwino, palinso anthu ambiri omwe akukayikira ngati zinthu zingakhaledi bwino kutsogoloku. N’chifukwa chiyani zili choncho?
ZIDA ZA NKHONDO ZOMWE ZINGAPHE ANTHU AMBIRI. Bungwe la United Nations komanso mabungwe ena akhala akuyesetsa kuthetsa zida za nyukiliya, koma izi sizikuthandiza. Pali atsogoleri a mayiko ena omwe akukana kutsatira malamulo othetsa zidazi. Mayiko omwe kuchokera kalekale ankadziwika kuti ali ndi zida za nyukiliya, panopo akuziwonjezera mphamvu ndipo akupanganso zina zoopsa kwambiri kuposa zakalezo. Mayiko ena omwe poyamba analibe zida zoopsa, panopa ayamba kusunga zida zoopsa zomwe zingaphe anthu ambiri nthawi imodzi.
Mayiko akusunga zida zoopsa kwambiri pokonzekera kuti nthawi ina kutha kudzabuka nkhondo ya nyukiliya. Zimenezi zikuchititsa kuti anthu padzikoli azikhala mwamantha kwambiri ngakhale pamene zikuoneka ngati zinthu ziliko bwino. Magazini ina inachenjezanso kuti: “Chodetsanso nkhawa kwambiri ndi zida za nkhondo zoopsa kwambiri zomwe zinapangidwa kuti zizigwira ntchito pazokha popanda kuwongoleredwa ndi anthu.”—Bulletin of the Atomic Scientists.
MATENDA. Asayansi sangatilonjeze zoti tingakhale ndi moyo wathanzi nthawi zonse. Zinthu zodetsa nkhawa monga kuthamanga kwa magazi, kunenepa kwambiri, kuwonongeka kwa mpweya komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, zikuwonjezeka kwambiri. Anthu ambiri akumwalira ndi matenda a khansa, a mtima komanso a shuga. Anthu enanso ambiri akulumala chifukwa cha matenda ena kuphatizapo matenda a maganizo. Zaka zaposachedwa kwabukanso matenda oopsa ngati a Ebola komanso a Zika. Koma zoona zake n’zakuti, anthu sangathe kuthetsa matenda ndipo palibe chiyembekezo choti adzawathetsa.
KUWONONGA CHILENGEDWE. Mafakitale akupitirizabe kuwononga mpweya. Anthu ambirimbiri akumwalira chaka chilichonse chifukwa chopuma mpweya woipa.
Anthu komanso mabungwe a boma akupitirizabe kutaya zonyansa za kuchipatala, zinthu zapulasitiki ndi zinyalala zina m’nyanja. Buku lina linanena kuti: “Zinthu zomwe amatayazi zimakhala ndi poizoni ndipo zimawononga zomera ndi zamoyo zina zam’madzi. Komanso anthu omwe amadya zomera komanso zamoyo zam’madzizi amaika moyo wawo pangozi.”—Encyclopedia of Marine Science.
Madzi abwino ayamba kutha. Katswiri wina wa ku Britain amene amalemba mabuku asayansi dzina lake Robin McKie, anachenjeza kuti: “Madzi abwino ayamba kusowa ndipo kutsogoloku vutoli lidzakhala la padziko lonse.” Akatswiri andale amavomereza kuti vuto la kusowa kwa madzi, linayambitsidwa ndi anthu ndipo likuika moyo wa anthu ambiri pangozi.
NGOZI ZADZIDZIDZI. Mphepo zamkuntho ndi zivomerezi zikuchititsa kugumuka kwa nthaka, kusefukira kwa madzi komanso ngozi zina zadzidzidzi. Panopo anthu akufa kapena kuvutika kwambiri ndi ngozi zamtunduwu. Kafukufuku amene bungwe lina la ku United States loona za maulendo a pandege ndi sayansi ya mlengalenga linachita, anapeza kuti kutsogoloku kukhala kukuchitika mphepo zamkuntho, chilala komanso kusefukira kwa madzi. Ndipo ananena kuti zikhala zoopsa kwambiri kuposa panopa. Kodi ndiye kuti anthu adzatha onse padzikoli chifukwa cha ngozi zadzidzidzi zimenezi?
N’kutheka kuti mukudziwa zinthu zinanso zomwe zikuika moyo wathu pangozi. Komabe kungoona zinthu zoopsa zomwe zikuchitika panopo si kungakuthandizeni kudziwa zamtsogolo. Ndipo ena anganene kuti zimenezi n’zofanana ndi kumvetsera zolankhula za akatswiri asayansi ndi a ndale. Koma monga mmene tanenera m’nkhani yoyamba ija, anthu ambiri apeza mayankho okhutiritsa a mafunso ofuna kudziwa za tsogolo la dzikoli komanso chifukwa chake padzikoli pakuchitika zinthu zoopsa chonchi. Kodi mayankho a mafunsowa amapezeka kuti?