GALAMUKANI! Na. 6 2017 | Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri?
N’chifukwa chiyani zinthu padzikoli zikuoneka ngati sizingayendenso bwino?
Baibulo limati: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.
“Galamukani!” iyi ikufotokoza chifukwa chake anthu ena amaona kuti zinthu padzikoli zidzakhala bwino kwambiri mtsogolo.
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Zinthu Padzikoli Zafika Poipa Kwambiri Kapena Ayi?
Akatswiri atakokera “Wotchi Yosonyeza Nthawi ya Kutha kwa Dziko,” wotchiyi inayamba kusonyeza kuti kwatsala nthawi yochepa kuti 12 koloko ya usiku ikwane ndipo izi ndi zosiyana ndi mmene nthawi inalili chikhazikitsireni wotchiyi zaka 60 zapitazo. Kodi dzikoli latsaladi pang’ono kutha?
NKHANI YAPACHIKUTO
Kufufuza Mayankho
Ofalitsa nkhani akuchititsa anthu ambiri kukhulupirira kuti zinthu padzikoli zafika poipa kwambiri moti palibenso zomwe anthufe tingachite. Kodi zinthu zaipa kufika pati?
NKHANI YAPACHIKUTO
Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Zaka zambirimbiri m’mbuyomo, Baibulo linaneneratu za zinthu zoipa zomwe zikuchitika masiku ano.
MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA
Mungaphunzitse Bwanji Ana Anu Kukhala Odzichepetsa?
Muziphunzitsa mwana kukhala wodzichepetsa popanda kum’pangitsa kudziona ngati wachabechabe.
ANTHU NDI MAYIKO
Dziko la New Zealand
Ngakhale kuti dziko New Zealand lili kutali kwambiri, alendo pafupifupi 3 miliyoni amalowa m’dzikoli. Kodi n’chiyani chimawachititsa chidwi alendowa?
TIONE ZAKALE
Alhazen
Mwina simunamvepo za Alhazen koma zomwe anapanga zimakukhudzani ndithu mwa njira inayake.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Dzina la Mulungu
Anthu amatchula Mulungu Wamphamvuyonse ndi mayina osiyanasiyana. Koma Mulunguyo ali ndi dzina lake lenileni.
Mlozera Nkhani wa Magazini a Galamukani! a 2017
Mndandanda wa nkhani zomwe zinafalitsidwa mu 2017.
Zina zimene zili pawebusaiti
Uzinena Zoona
N’chifukwa chiyani nthawi zonse uyenera kunena zoona?
Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?
Kodi ineyo ndikuona kuti chimenechi ndi chipembedzodi cholondola?