Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Wathanzi

Moyo Wathanzi

Baibulo si buku la zachipatala. Komabe lili ndi mfundo zimene zingatithandize kukhala ndi moyo wathanzi. Tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize kusamalira thanzi lathu.

MUZISAMALIRA THANZI LANU

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”​—Aefeso 5:29.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Mfundo ya m’Baibulo imeneyi imatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kusamalira thanzi lathu. Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu ambiri amadwala chifukwa choti sadziwa kusamalira thanzi lawo. Choncho mukamachita zinthu zoyenera mukhoza kukhala ndi moyo wathanzi.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzidya Zakudya Zopatsa Thanzi. Muzionetsetsa kuti mukudya zakudya zopatsa thanzi komanso kumwa madzi ambiri.

  • Muzichita Masewera Olimbitsa Thupi. Masewera olimbitsa thupi akhoza kukuthandizani kuti mukhale athanzi. Masewera olimbitsa thupi ndi abwino kwa anthu amisinkhu yonse. Akhoza kukuthandizaninso ngakhale zitakhala kuti ndinu wolumala kapena mukudwala matenda enaake. N’zoona kuti achibale anu kapena anzanu angamakulimbikitseni kuti muzichita masewera olimbitsa thupi. Komabe, palibe amene angakuchitireni zimenezi.!

  • Muzigona Mokwanira. Anthu amene akhala nthawi yaitali asakugona mokwanira, akhoza kudwala kwambiri. Ena amalephera kugona mokwanira chifukwa chochita zinthu zina pa nthawi imene amayenera kumagona. Munthu akamagona mokwanira amakhala wathanzi..

MUZIPEWA ZIZOLOWEZI ZOIPA

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.”​—2 Akorinto 7:1.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Tingakhale ndi moyo wathanzi ngati timapewa kuwononga thupi lathu ndi zinthu ngati fodya. Akatswiri amanena kuti fodya amayambitsa matenda oopsa omwe amapha anthu ambiri.

ZIMENE MUNGACHITE: Sankhani tsiku limene mukufuna kusiya kusuta fodya ndipo mulilembe pakalendala yanu. Tsikulo lisanafike, muyenera kutaya zinthu zonse zokhudzana ndi kusuta fodya monga ndudu, zoyatsira fodya, timbale toikamo phulusa ndi zina. Muzipewa kupezeka pamalo amene anthu amakonda kusuta. Mungachitenso bwino kufotokozera achibale anu komanso anzanu kuti mukufuna kusiya kusuta fodya kuti akuthandizeni.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO

Ngati mukufuna Baibulo funsani wa Mboni za Yehova aliyense m’dera lanu

MUZIPEWA NGOZI.

“Ukamanga nyumba yatsopano uzimanganso kampanda padenga la nyumbayo kuopera kuti ungaike mlandu wa magazi panyumba yako ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.”​—DEUTERONOMO 22:8.

MUZIUGWIRA MTIMA.

“Wosafulumira kukwiya n’ngozindikira zinthu kwambiri, koma wokwiya msanga amalimbikitsa uchitsiru.”​—MIYAMBO 14:29

MUZIPEWA KUDYA KWAMBIRI.

‘Usakhale pakati pa anthu . . . osusuka.’​—MIYAMBO 23:20.