Banja Labwino Komanso Mabwenzi Abwino
Anthu ambiri zimawavuta kuti akhale ndi banja labwino komanso anzawo abwino. M’Baibulo muli mfundo zomwe zingakuthandizeni kuti muzikhala bwino ndi anthu ena. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
MUZIGANIZIRA ZA ENA
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.
ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Tikhoza kukhala ndi anzathu abwino tikamaganizira kwambiri zimene tingawachitire m’malo mwa zimene iwowo angatichitire. Ngati munthu atakhala ndi mtima wodzikonda, sangamagwirizane ndi anzake. Mwachitsanzo, ngati mwamuna kapena mkazi ndi wodzikonda, akhoza kukhala wosakhulupirika m’banja. Komanso palibe angakonde kumacheza ndi munthu amene amangokhalira kudzitama chifukwa cha zimene ali nazo kapena zimene amadziwa. N’chifukwa chake buku lina limanena kuti “mtima wodzikonda umabweretsa mavuto ambiri.”—The Road to Character.
ZIMENE MUNGACHITE:
-
Muzithandiza ena. Mabwenzi abwino amakhulupirirana komanso kuthandizana. Kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene amakonda kuthandiza ena sadwala matenda amaganizo ndipo amakhala osangalala.
-
Muziganizira mmene ena akumvera. Anthu amene amachita zimenezi amatha kudziyerekezera mmene iwowo angamvere ngati atakumana ndi zimene munthu wina wakumana nazo. Mukamaganizira mmene ena akumvera, mungapewe kulankhula mawu opweteka kapena nthabwala zimene zingakhumudwitse ena.
Mukamaganizira mmene ena akumvera, mumagwirizana kwambiri ndi anthu ena.
Choncho khalidwe limeneli lingakuthandizeninso kuti musakhale atsankho ndipo mungakhale ndi anzanu ochokera m’zikhalidwe zosiyanasiyana. -
Muzipeza nthawi yocheza ndi ena. Mukamacheza kwambiri ndi anthu ena, m’pamene mumawadziwa bwino. Ngati mukufuna kupeza anzanu abwino, muzinena zimene anzanuwo angasangalale nazo komanso zimene amakonda. Choncho muyenera kumawamvetsera akamalankhula komanso muzisonyeza kuti mumawaganizira. Kafukufuku wina waposachedwapa anasonyeza kuti “anthu amene amakonda kucheza momasuka amakhala osangalala.”
MUZISANKHA BWINO ANTHU OCHEZA NAWO
MFUNDO YA M’BAIBULO: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”—1 Akorinto 15:33.
ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Anthu amene mumakonda kucheza nawo akhoza kukuchititsani kuti mukhale ndi khalidwe labwino kapena loipa. Akatswiri oona za makhalidwe a anthu amanena kuti anthu ocheza nawo akhoza kuthandiza kapena kusokoneza munthu kwambiri. Mwachitsanzo, amanena kuti munthu akhoza kuyamba kusuta fodya kapena kuthetsa banja lake ngati amacheza ndi anthu omwe amachita zimenezi.
ZIMENE MUNGACHITE: Muzicheza ndi anthu amene ali ndi makhalidwe amene amakusangalatsani kapena amene mumafuna mutakhala nawo. Mwachitsanzo, mungachite bwino kumagwirizana ndi anthu amene amachita zinthu mosamala, aulemu, ochereza komanso owolowa manja.
MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO
MUZIPEWA KULANKHULA MAWU OMWE ANGAKHUMUDWITSE ENA.
“Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga.”—MIYAMBO 12:18.
MUZIKHALA OWOLOWA MANJA.
“Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto.”—MIYAMBO 11:25.
MUZICHITIRA ENA ZINTHU ZOMWE MUNGAFUNE KUTI AKUCHITIRENI.
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.”—MATEYU 7:12.