Mawu Oyamba
Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino
Nthawi zambiri timamva nkhani zosiyanasiyana zomwe zimasokoneza mabanja. Magaziniyi ikufotokoza zimene anthu ena achita kuti mabanja awo aziyenda bwino.
Zaka zapakati pa 1990 ndi 2015, ku United States, chiwerengero cha mabanja omwe anatha chinawirikiza kawiri kwa anthu a zaka zoposa 50 ndipo chinawirikiza katatu kwa anthu a zaka zoposa 65.
Makolo ambiri asokonezeka chifukwa akatswiri ena amawauza kuti nthawi zonse aziyamikira ana awo. Pomwe ena amawauza kuti mwana amafunika kumuikira malamulo okhwima.
Achinyamata ambiri akukula asanaphunzire luso lililonse lomwe lingadzawathandize m’tsogolo.
Komabe zoona ndi zakuti . . .
N’zotheka kukhala ndi banja losangalala komanso kwa moyo wonse.
Makolo angakwanitse kulangiza ana awo mwachikondi.
Achinyamata akhoza kuphunzira luso linalake lomwe lingadzawathandize akadzakula.
Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Werengani Galamukani! iyi kuti mupeze mfundo 12 zothandiza kuti banja liziyenda bwino.