ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Mtanda
Anthu ambiri amaona kuti mtanda ndi chizindikiro cha Akhristu. Komabe si onse amene amaona kuti ndi bwino kuti mtanda uzivalidwa, kuikidwa m’nyumba kapenanso m’matchalitchi.
Kodi Yesu anafera pamtanda?
ZIMENE ANTHU ENA AMANENA
Aroma anapha Yesu pomupachika pamtanda womwe unapangidwa ndi mitengo iwiri.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Anthu anapha Yesu mwa “kumupachika pamtengo.” (Machitidwe 5:30, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Mawu awiri Achigiriki omwe anagwiritsidwa ntchito ndi olemba Baibulo pofotokoza malo omwe Yesu anapachikidwapo, amanena za mtengo umodzi osati iwiri. Buku lina la mbiri yakale limafotokoza kuti mawu Achigiriki akuti stau·rosʹ, amatanthauza “polo kapena mtengo umodzi wowongoka wopanda nthambi iliyonse. Ndipo mawu Achigirikiwa satanthauza ‘mtanda.’” (Crucifixion in Antiquity) Komanso mawu akuti xyʹlon, omwe anagwiritsidwa ntchito pa Machitidwe 5:30 “amangonena za mtengo umodzi wautali womwe Aroma ankagwiritsa ntchito pokhomerapo anthu amene agamulidwa kuti aphedwe.” *
Baibulo limasonyeza kuti Yesu anaphedwa mogwirizana ndi zimene chilamulo cha Aisiraeli chinkanena. Chilamulocho chinkanena kuti: “Pakakhala munthu amene wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe, ndiyeno munthuyo waphedwa, ndipo wam’pachika pamtengo, . . . aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.” (Deuteronomo 21:22, 23) Ponena za chilamulocho, mtumwi Paulo analemba za Yesu kuti “anakhala temberero m’malo mwa ife, chifukwa Malemba amati: ‘Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pamtengo [xyʹlon].’” (Agalatiya 3:13) Pamenepatu, Paulo anasonyeza kuti Yesu anapachikidwa pamtengo umodzi wokha.
“Anamupha nampachika pamtengo.”
—Machitidwe 10:39, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Kodi ophunzira a Yesu ankagwiritsa ntchito mtanda polambira Mulungu kapena ngati chizindikiro choti iwowo ndi Akhristu?
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Palibe paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti Akhristu oyambirira ankagwiritsa ntchito mtanda monga chizindikiro cha chipembedzo chawo. Koma pa nthawiyo Aroma ndi amene ankagwiritsira ntchito chinthu chooneka ngati mtanda monga chizindikiro choimira milungu yawo. Patadutsa zaka 300 Yesu ataphedwa, Constantine yemwe anali Mfumu ya Aroma, anayamba kugwiritsa ntchito mtanda ngati chizindikiro choimira asilikali ake ndipo kenako mtandawo unayamba kugwiritsidwanso ntchito ngati chizindikiro cha matchalitchi Achikhristu.
Popeza kuti anthu achikunja ankagwiritsira ntchito mtanda polambira milungu yawo, kodi zikanakhala zomveka kuti ophunzira a Yesu azigwiritsanso ntchito mtanda polambira Mulungu woona? Akhristuwa sakanachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti kuchokera kalekale, Mulungu sankalola kuti anthu ake azimulambira pogwiritsa ntchito “chifaniziro cha chinthu chilichonse.” Ndipo Akhristuwo ankafunika ‘kuthawa kupembedza mafano.’ (Deuteronomo 4:15-19; 1 Akorinto 10:14) ‘Mulungu ndi Mzimu,’ ndipo anthufe sitingathe kumuona. N’chifukwa chake Akhristu oyambirira sanagwiritse ntchito chinthu chilichonse ngati chizindikiro chowathandiza kumva kuti Mulungu ali nawo pafupi. Koma ankalambira Mulungu ‘motsogoleredwa ndi mzimu woyera’ ndipo mzimuwo nawonso ndi mphamvu ya Mulungu yosaoneka. Komanso ankafunika kumulambira mu “choonadi,” kapena kuti mogwirizana ndi mfundo za m’Malemba.
“Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”
—Yohane 4:23.
Kodi Akhristu angasonyeze bwanji kuti amalemekeza Yesu Khristu?
ZIMENE ANTHU AMANENA
“N’zomveka kuti chilichonse chomwe chingathandize kuti munthu apulumuke chizipatsidwa ulemu komanso chizioneka kuti ndi chinthu chapadera. . . . Aliyense amene amalambira chifaniziro chinachake, amakhala akulambira munthu amene chifanizirocho chikuimira.”
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Akhristu amayamikira kwambiri zimene Yesu anachita powafera chifukwa imfa yake imathandiza kuti machimo awo akhululukidwe, akhale pa ubwenzi ndi Mulungu komanso kuti adzapeze moyo wosatha. (Yohane 3:16; Aheberi 10:19-22) Akhristu sanauzidwe kuti azilemekeza Yesu pogwiritsa ntchito chizindikiro choimira Yesuyo kapena kumangonena zoti amamukhulupirira. Ndipotu “chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.” (Yakobo 2:17) Choncho Akhristu ayenera kukhulupirira Yesu. Koma kodi angachite bwanji zimenezi?
Baibulo limati: “Chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza, chifukwa tatsimikiza kuti munthu mmodzi anafera anthu onse . . . Amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.” (2 Akorinto 5:14, 15) Chikondi chimene Yesu anasonyeza chimakakamiza Akhristu kusintha moyo wawo kuti azitsatira zimene anachita. Akhristuwa akamachita zimenezi amasonyeza kuti amalemekeza Yesu ndipo imeneyi ndi njira yofunika kwambiri kuposa kukhala ndi chifaniziro chake.
“Pakuti chifuniro cha Atate wanga ndi chakuti, aliyense woona Mwana ndi kukhulupirira mwa iye akhale nawo moyo wosatha.”
—Yohane 6:40.
^ ndime 8 Buku lakuti, Critical Lexicon and Concordance to the English and Greek New Testament, 11th Edition, lolembedwa ndi Ethelbert W. Bullinger, tsamba 818-819.