Nzeru Zothandiza Kukhala Ndi Banja Losangalala
Kukhala pabanja komanso kukhala ndi ana ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mlengi wathu. Iye amafuna kuti tikhale ndi banja losangalala. Choncho pogwiritsa ntchito buku lakale lopatulika iye amatipatsa malangizo amene angathandize banja lathu kukhala labwino komanso losangalala. Taganizirani malangizo anzeru otsatirawa:
Amuna, Muzikonda Akazi Anu
“Amuna akonde akazi awo monga matupi awo. Amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, pakuti palibe munthu anadapo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda.”—AEFESO 5:28, 29.
Mwamuna ndiye mutu wa banja. (Aefeso 5:23) Koma mwamuna wabwino sakhala waukali kapena wongolamula zilizonse. Iye amalemekeza mkazi wake ndipo amamupezera zinthu zofunika pa moyo komanso amamukonda. Amayesetsanso kuchita zinthu zosangalatsa mkazi wake, m’malo mongokakamira zofuna zake. (Afilipi 2:4) Amafotokoza zamumtima mwake momasuka ndiponso mkaziyo akamalankhula amamumvetsera. Iye ‘sapsera mtima kwambiri’ mkazi wake, kumuchitira nkhanza ngakhalenso kumulankhula mwachipongwe.—Akolose 3:19.
Akazi, Muzilemekeza Amuna Anu
“Mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.”—AEFESO 5:33.
Mkazi akamalemekeza mwamuna wake komanso kugwirizana ndi zimene mwamunayo wasankha, zimathandiza kuti m’banjamo mukhale mtendere. Ngati mwamunayo walakwitsa zinazake mkaziyo sachita zinthu momupeputsa koma amakhalabe wodekha komanso waulemu. (1 Petulo 3:4) Pakakhala nkhani yoti akambirane ndi mwamuna wake amasankha nthawi yabwino komanso amalankhula naye mwaulemu.—Mlaliki 3:7.
Muzikhala Okhulupirika Kwa Mwamuna Kapena Mkazi Wanu
‘Mwamuna adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.’—GENESIS 2:24.
Mwamuna ndi mkazi akakwatirana amapanga ubwenzi wolimba kwambiri. Choncho anthu okwatirana ayenera kumayesetsa kuti banja lawo likhale lolimba. Iwo angamachite zimenezi pouzana zakukhosi komanso kusonyezana kukoma mtima mu zinthu zing’onozing’ono. Ayenera kukhala okhulupirika m’banja mwawo ndipo sayenera kugona ndi mkazi kapena mwamuna wina. Kuchita zimenezi ndi nkhanza ndipo anthu amasiya kukhulupirirana komanso banja likhoza kutha.—Aheberi 13:4.
Makolo, Muziphunzitsa Ana Anu
“Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”—MIYAMBO 22:6.
Mulungu anapatsa makolo udindo wophunzitsa ana awo. Zimenezi zikuphatikizapo kuwaphunzitsa makhalidwe abwino komanso kuwapatsa chitsanzo chabwino. (Deuteronomo 6:6, 7) Mwana akamapanda kumvera, kholo lanzeru limachita zinthu modekha. Khololo ‘limakhala lofulumira kumva, lodekha polankhula, losafulumira kukwiya.’ (Yakobo 1:19) Ngati laona kuti mwanayo akufunika kulandira chilango limachita zimenezo mwachikondi, osati mwaukali.
Ananu, Muzimvera Makolo Anu
“Ananu, muzimvera makolo anu . . . ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.’”—AEFESO 6:1, 2.
Ana ayenera kumvera makolo awo komanso kuwalemekeza kwambiri. Ana akamalemekeza makolo awo amathandiza kuti banja likhale losangalala, lamtendere komanso logwirizana. Ana akuluakulu amalemekeza makolo awo akamaonetsetsa kuti makolowo akusamaliridwa bwino. Zimenezi zingaphatikizepo kuonetsetsa kuti akusamalira pakhomo pawo kapena kuwapatsa thandizo la ndalama.—1 Timoteyo 5:3, 4.