Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Nkhani Zokhudza Chilengedwe

Nkhani Zokhudza Chilengedwe

Mulungu analenga dzikoli kuti lizitipatsa mpweya, chakudya komanso madzi abwino. Koma anthu akuwononga kwambiri zinthu zachilengedwe. Choncho, asayansi akuyesetsa kufufuza njira zothetsera vutoli koma akulephera

Australia

Zikuoneka kuti pansi pa nyanja zikuluzikulu pali madzi ambiri opanda mchere abwino kumwa. Pulofesa wina wa pa yunivesite ya Flinders mumzinda wa Adelaide, dzina lake Vincent Post anati: “Poyamba madzi a m’nyanja sanali ambiri ngati mmene zilili panopa moti malo aakulu omwe ali m’mbali mwa nyanja anali pamtunda. Mvula ikagwa, madzi a mvulawo ankalowa munthaka m’malo amenewa. Koma panopa madzi a m’nyanja anakwera ndipo anafika pamalo amene poyamba anali pamtundawa. Izi zapangitsa kuti madzi abwino kumwa, omwe ankalowa pansi aja, akhale pansi pa madzi a m’nyanja.” Asayansi akuganiza kuti m’tsogolomu adzapeza njira yomwe ingathandize kuti ena mwa anthu oposa 700 miliyoni, omwe amasowa madzi abwino, azidzamwa madzi amenewa.

Chipululu cha Sahara

Hafu ya nyama zomwe zinkapezeka m’chipululu cha Sahara zinatha kapena zangotsala pang’ono kutheratu. Zimene zikuchititsa zimenezi ndi zinthu monga nkhondo, zipolowe komanso kupha nyama mwachisawawa. Ngakhale kuti m’zipululu mumapezekanso nyama zambiri ngati m’nkhalango, kafukufuku akusonyeza kuti “akatswiri oona za nyama sasamalira nyama za m’chipululu chifukwa chosowa ndalama.” Zimenezi zikuchititsa kuti akatswiri oteteza zachilengedwe azilephera kudziwa kuti ndi nyama ziti za m’chipululu zomwe zangotsala pang’ono kutheratu.

Dziko Lonse

Kafukufuku wina anasonyeza kuti munthu mmodzi pa anthu 8 alionse omwe anamwalira mu 2012, anafa chifukwa chopuma mpweya woipa. Malinga ndi lipoti lomwe bungwe loona za umoyo padziko lonse linalemba, “mpweya woipa ndi umene ukuyambitsa matenda ambiri kuposa chilichonse.”