Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mavuto

Mavuto

Anthu ena amaganiza kuti Mulungu ndi amene amachititsa mavuto, apo ayi ndiye kuti alibe nazo ntchito za mavuto a anthu. Koma kodi zimenezi ndi zomwe Baibulo limaphunzitsa? Mungadabwe ndi yankho la m’Baibulo la funsoli.

Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika?

“Ndithudi, Mulungu sachita zoipa.”Yobu 34:12.

ZIMENE ANTHU AMANENA Anthu ena amanena kuti chilichonse chimene chimachitika padzikoli ndi chifuniro cha Mulungu.

Choncho, amaona kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika. Mwachitsanzo, pakachitika ngozi zamwadzidzidzi amanena kuti Mulungu ndi amene wachititsa zimenezo pofuna kulanga anthu ochimwa.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu si amene amachititsa mavuto padzikoli. Mwachitsanzo limanena kuti tikakumana ndi mavuto, n’kulakwa kuganiza kuti, “Mulungu akundiyesa” chifukwa “Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yakobo 1:13) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu si amene amachititsa mavuto omwe timakumana nawo. Akanakhala kuti amachititsa mavuto ndi iyeyo, bwenzi ali woipa. Komatu Baibulo limati, “Mulungu sachita zoipa.”—Yobu 34:12.

Ngati Mulungu si amene amachititsa kuti tizivutika, ndiye ndi ndani amene amachititsa zimenezi? Choyamba, anthu ena amavutika chifukwa choponderezedwa ndi anthu anzawo. (Mlaliki 8:9) Chachiwiri, anthu amakumana ndi mavuto chifukwa cha “zinthu zosayembekezereka” zimene zimagwera anthu onse. Zoterezi zimangochitika chifukwa choti pa nthawi imene tsoka linalake limachitika, munthuyo anali pamalopo. (Mlaliki 9:11) Komanso Baibulo limaphunzitsa kuti Satana Mdyerekezi, yemwe ndi “wolamulira wa dzikoli” ndi amene amachititsa mavuto ambiri padzikoli. Limati: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) Choncho Satana ndi amene amachititsa kuti anthufe tizivutika, osati Mulungu.

Kodi Mulungu amamva bwanji tikamavutika?

“Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.”Yesaya 63:9.

ZIMENE ANTHU AMANENA

Anthu ena amaona kuti Mulungu alibe nazo ntchito za mavuto athu. Mwachitsanzo, munthu wina analemba kuti ngati Mulungu alipodi ndiye kuti ndi “wouma mtima, wopanda chisoni komanso satidera nkhawa tikamavutika. Akanakhala kuti amatidera nkhawa, bwenzi atathetsa mavuto padzikoli.”

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Baibulo limanena kuti Mulungu ndi wachifundo. Limaphunzitsanso kuti amakhudzidwa anthufe tikamavutika ndipo limasonyeza kuti posachedwapa adzathetsa mavuto onse. Tiyeni tikambirane mfundo zitatu zolimbikitsa zimene tiyenera kudziwa zokhudza Mulungu.

Mulungu amadziwa mavuto athu. Umboni umasonyeza kuti kuyambira kalekale palibe munthu amene anakumanapo ndi vuto linalake, Yehova * osadziwa zimenezo. Izi zili choncho chifukwa “maso ake owala” amaona chilichonse. (Salimo 11:4; 56:8) Mwachitsanzo, pamene atumiki ake akale ankaponderezedwa, Mulungu anati: “Ndaona nsautso ya anthu anga.” Komabe sikuti Mulungu anangoona kuti anthuwo akuvutika. Ankadziwa bwino mavuto awo komanso mmene ankamvera moti ananena kuti: “Ndikudziwa bwino zowawa zawo.” (Ekisodo 3:7) Anthu ambiri amalimbikitsidwa akadziwa kuti Mulungu amadziwa bwino mavuto komanso mayesero awo ngakhale amene anthu ena sangathe kuwadziwa.—Salimo 31:7; Miyambo 14:10.

Mulungu amatimvera chisoni tikamavutika. Sikuti Yehova Mulungu amangodziwa mavuto athu koma amatimveranso chisoni. Mwachitsanzo, pa nthawi inanso, Mulungu anavutika mumtima pamene atumiki ake ankakumana ndi mavuto. Baibulo limati: “Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.” (Yesaya 63:9) Ngakhale kuti Mulungu ndi wapamwamba kwambiri, amatimvera chisoni tikamavutika. Amamva ngati mavutowo akumuchitikira iyeyo. “Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yakobo 5:11) Kuwonjezera pamenepa, Yehova amatithandiza kuti tipirire tikamavutika.—Afilipi 4:12, 13.

Mulungu adzathetsa mavuto onse. Baibulo limanena kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake kuthetsa mavuto onse komanso kusintha zinthu padzikoli. Pa nthawiyo Mulungu ‘adzapukuta misozi yonse m’maso mwa anthu, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.’ (Chivumbulutso 21:4) Baibulo limanenanso kuti Mulungu adzaukitsa anthu amene anamwalira ndipo adzasangalala ndi moyo wopanda mavuto. (Yohane 5:28, 29) Komanso palibe munthu aliyense yemwe azidzakumbukira mavuto amene ankakumana nawo. Baibulo limati: “Zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso ndipo sizidzabweranso mumtima.”—Yesaya 65:17. *

^ ndime 13 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.

^ ndime 15 Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu walola kuti mavuto azichitikabe komanso mmene adzawathetsere, werengani mutu 8 ndi 11 m’buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.