Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Ukhondo Komanso Makhalidwe Abwino

Ukhondo Komanso Makhalidwe Abwino

Mulungu amafuna kuti tizikhala aukhondo

“Tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu, kwinaku tikukwaniritsa kukhala oyera poopa Mulungu.”2 Akorinto 7:1.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mlengi wathu amatikonda ndipo amafuna kuti tikhale ndi moyo wathanzi, wautali komanso wosangalala. Iye amatiuza kuti: “Mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, udzakhala ndi masiku ochuluka, moyo wazaka zambiri, ndi mtendere.” (Miyambo 3:1, 2) Chilamulo chimene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli chimasonyezanso kuti iye amakonda anthu. Chilamulochi chinali ndi malangizo osapita m’mbali onena za ukhondo. (Deuteronomo 23:12-14) Aisiraeli akamatsatira malangizowa, ankakhala ndi thanzi labwino. Iwo sankadwala matenda omwe Aiguputo komanso anthu a mitundu ina ankadwala. Pa nthawiyi n’kuti anthu asanazindikire mfundo zokhudza ukhondo zofanana ndi zimene Mulungu anapereka kwa Aisiraelizi.—Deuteronomo 7:12, 15.

Masiku anonso, anthu amene amatsatira malangizo a Mulungu akuti, “tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi,” amakhala ndi thanzi labwino, amapewa matenda osiyanasiyana komanso safa msanga. Zina mwa zinthu zodetsazi ndi kusuta fodya, kumwa mwauchidakwa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza ubongo. Tikamatsatira malangizo a Mulungu okhudza ukhondo, timasonyezanso kuti timaganizira ena.—Maliko 12:30, 31.

Mulungu amafunanso kuti tizipewa makhalidwe oipa

“Chititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano. Chifukwa cha zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera.”Akolose 3:5, 6.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Monga taonera kale, Baibulo limatilimbikitsa kuti, “tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi kapena mzimu.” Pa nthawi imene Yesu anali padziko lapansi, anthu ambiri kuphatikizapo atsogoleri a chipembedzo, ankatsatira monyanyira malangizo okhudza ukhondo koma n’kumanyalanyaza malangizo okhudza kukhala ndi makhalidwe abwino. (Maliko 7:1-5) Apa tingati iwo ankayesetsa kukhala aukhondo koma ankanyalanyaza kufunika kokhala oyera mwauzimu. Pofuna kuwathandiza, Yesu anati: “Palibe chochokera kunja kwa thupi n’kudutsa m’thupi mwa munthu chimene chingamuipitse, popeza sichidutsa mumtima mwake, koma m’matumbo mwake, ndipo chimakatuluka kuchimbudzi.” Anatinso: “Chotuluka mwa munthu n’chimene chimaipitsa munthu. Pakuti mkatimo, mumtima mwa munthu, mumatuluka maganizo oipa. Mumatuluka zadama, zakuba, zaumbanda, zachigololo, kusirira kwa nsanje, kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lotayirira, diso la kaduka, . . . ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena. Zoipa zonsezi . . . zimaipitsa munthu.”—Maliko 7:18-23.

Zimene Yesu ananenazi zikusonyeza kuti anthu amene amatsatira malangizo okhudza ukhondo monyanyira koma n’kumanyalanyaza malangizo oti tizipewa makhalidwe oipa, amakhala ngati makapu oyera kunja koma m’kati mwake muli mwakuda.—Mateyu 23:25, 26.

Kodi n’zotheka kutsatira zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ukhondo komanso makhalidwe abwino?

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”1 Yohane 5:3.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Lemba la Mika 6:8 limati: “Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” Malangizo amenewa si ovuta, ndipo aliyense angathe kuwatsatira. Ndipotu Mlengi wathu amafuna kuti tizimumvera chifukwa chomukonda. Tikamachita zimenezi, timakhala osangalala. (Salimo 40:8) Tikalakwa, timakhulupirira kuti Mulungu atikhululukira chifukwa ndi wachifundo. Baibulo limati: “Monga mmene bambo amasonyezera chifundo kwa ana ake, Yehova wasonyezanso chifundo kwa onse omuopa. Pakuti iye akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi.” (Salimo 103:13, 14) Izi zikusonyeza kuti Mulungu amadziwa kuti si ife angwiro ndipo timalakwitsa zinthu zina.

M’nkhaniyi taona kuti malangizo a Mulungu okhudza ukhondo komanso makhalidwe abwino, amasonyeza kuti Mulungu ndi wabwino ndipo amatikonda. Tikamatsatira malangizo amenewa, timasonyeza kuti ndife anzeru ndiponso kuti timakonda Yehova.