Zochitika Padzikoli
Padziko Lonse
Malinga ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena, vuto lochitira nkhanza akazi “lakula kwambiri padziko lonse.” Bungweli linanena kuti “akazi 35 pa 100 alionse amachitidwa nkhanza ndi amuna awo, chibwenzi chawo, munthu amene anali naye pa chibwenzi, munthu amene anali naye pa banja kapena azibambo ena. Koma pa azimayi ochitidwa nkhanzawa, 5 okha pa 100 alionse ndi amene amachitidwa nkhanza ndi azibambo ena.”
Britain
Pa anthu 64,303, amene anafunsidwa pa nkhani zokhudza chipembedzo, anthu 50,799, ananena kuti “chipembedzo ndi chimene chikuyambitsa mavuto ambiri komanso mikangano masiku ano.” Kuwonjezera pamenepa, kafukufuku wina amene anachitika mu 2011 ku Wales ndi ku England, anasonyeza kuti mu 2001 anthu 72 pa 100 alionse ankati ndi Akhristu, koma mu 2011 anthu 59 okha pa 100 alionse ndi amene ankati ndi Akhristu. Kafukufukuyu anasonyezanso kuti kuchokera mu 2001 kufika mu 2011, chiwerengero cha anthu amene ankanena kuti alibe chipembedzo chinakwera kuchoka pa 15 pa anthu 100 alionse kufika pa 25 pa anthu 100 alionse.
China
Ku China kunali lamulo loti anthu azikaona makolo awo okalamba pafupipafupi. Koma lipoti lina la posachedwapa lanena kuti kuwonjezera pa lamuloli, akhazikitsanso lamulo loti anthuwo azionetsetsa kuti “akupeza nthawi yocheza ndi makolo awo okalambawo kuti amve maganizo awo komanso zimene zikuwadetsa nkhawa.” Komabe lamuloli “silinanene chilango” chimene chiziperekedwa kwa anthu amene alephera kulitsatira.
Europe
Masiku ano zigawenga zayamba kupanga katundu osiyanasiyana wachinyengo monga zodzoladzola, sopo wochapira ngakhalenso zakudya. Popeza popanga katunduyu mafakitale amagwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana zimene zimapangitsa kuti katunduyo akhale wabwino komanso kuti aziyenda malonda, pulezidenti wa kampani ina yoona za zakudya ananena kuti: “Zigawengazi zikumapanga zinthu zachinyengozi pogwiritsa ntchito zinthu zina zimene zimapezeka mu katundu wopangidwa ndi mafakitale ovomerezeka, komano n’kuikamo zinthu zina zachinyengo.” Katswiri wina ananena kuti zakudya zina zimene anthu a m’mayiko osauka amagula zimakhala zachinyengozi.