Ntchito Yofufuza Anthu Amene Ankawaganizira kuti ndi Mfiti ku Ulaya
ZAKA mahandiredi angapo zapitazo, anthu a ku Ulaya anayamba kuchita mantha ndi nkhani zokhudza ufiti. Izi zinachititsa kuti ayambe kufufuza ndi kupha anthu onse amene ankawaganizira kuti ndi mfiti. Zimenezi zinkachitika kwambiri m’mayiko monga France, Germany, kumpoto kwa Italy, Switzerland, Belgium, Luxembourg ndi Netherlands. Buku lina linanena kuti: “Anthu ambirimbiri a ku Ulaya komanso a m’mayiko amene ankalamulidwa ndi mayiko a ku Ulaya ankafunsidwa mafunso, kudedwa, kuzunzidwa, kutsekeredwa m’ndende, komanso kuphedwa. Anthu amene ankaganiziridwa kuti ndi mfitiwa, ankadziimba mlandu komanso ankakhala mwamantha.” * (Witch Hunts in the Western World) Kodi zimenezi zinayamba bwanji, nanga chinachititsa n’chiyani?
Khoti Komanso Buku Lolimbikitsa Kulanga Anthu Amene Ankawaganizira Kuti Ndi Mfiti
Chida chimene ankachigwiritsira ntchito kwambiri pozunza anthu amene ankawaganizira kuti ndi mfiti, linali khoti la Akatolika. Khotili linakhazikitsidwa ndi tchalitchi cha Akatolika m’zaka za m’ma 1200. Buku lina linanena kuti cholinga cha khotili chinali “kuthandiza ampatuko kuti abwerere komanso kuti anthu asachoke m’tchalitchichi.” (Der Hexenwahn) Khotili linkagwiritsidwa ntchito ngati polisi ya tchalitchi cha Katolika.
Pa December 5, 1484, Papa Innocent wa 8 anatulutsa chikalata chodana ndi khalidwe la ufiti. Anapatsanso mphamvu Jakob Sprenger ndi Heinrich Kramer (yemwe pa Chigiriki ankatchedwa Henricus Institoris) kuti athane ndi khalidweli. Anthu amenewa anatulutsa buku lakuti Malleus Maleficarum (Hamala ya Mfiti). Akatolika ndi Apulotesitanti omwe, anasangalala ndi bukuli chifukwa ankaona kuti lithandiza kuthana ndi vuto la ufiti. M’bukuli munali nkhani zabodza zofotokoza zimene mfiti zimachita ndipo nkhanizi anazipeka pongotengera chikhalidwe cha anthu a kuderalo. Anafotokozamonso zinthu zosiyanasiyana zokhudza ufiti, mmene angadziwire mfiti komanso mmene angachotsere mfitizo pakati pawo. Anthu amati “pa mabuku onse, bukuli ndiye linali loipa kwambiri . . . , komanso ndi limene linachititsa kuti anthu ambiri azunzidwe.”
Anthu amati ‘pa mabuku onse, buku lakuti The Hammer of Witches ndiye loipa kwambiri . . . , komanso ndi limene linachititsa kuti anthu ambiri azunzidwe’
Anthu amene ankaganizira anzawo kuti ndi mfiti, sankapereka umboni weniweni wa zimenezo. Buku lina limanena kuti anthu oganizira anzawowo “ankafuna kuti munthuyo avomere zoti ndi mfiti, ndipo ngati sanavomere ankamukakamiza kuti avomere.” Anthu amene ankawaganizira kuti ndi mfitiwa ankazunzidwa kwambiri.
Buku lija komanso chikalata chimene papa anatulutsa, zinapangitsa kuti ku Ulaya kuyambike ntchito yosaka anthu owaganizira kuti ndi mfiti. Komanso anthu odana ndi ufitiwa ankagwiritsa ntchito makina osindikizira ndipo izi zinachititsa kuti nkhaniyi ifalikirenso ku America konse.
Ndani Ankaimbidwa Mlandu wa Ufiti?
Anthu ambiri amene ankaganiziridwa kuti ndi mfiti anali azimayi, makamaka amasiye, omwe analibe aliyense wowateteza. Enanso amene ankawaganizira anali anthu achikulire, anthu osauka komanso azimayi amene ankadziwa mankhwala achikuda, makamaka ngati mankhwala awowo sanathandize. Choncho, aliyense ankakhudzidwa ndi nkhaniyi, kaya akhale wolemera, wosauka, mwamuna, mkazi, munthu wamba ngakhalenso wotchuka.
Anthu owaganizira kuti ndi mfitiwa ankaonedwa kuti ndi amene amachititsa zinthu zonse zoipa. Magazini ina ya ku Germany inanena kuti, “pakagwa mliri wa nkhono komanso tizilombo towononga mbewu ndi zipatso, ankati mfiti ndi zimene zachititsa zimenezo.” (Damals) Kukabwera chimphepo n’kuwononga mbewu, ng’ombe ikamalephera kutulutsa mkaka komanso ngati mwamuna kapena mkazi ndi wosabereka, ankati mfiti ndi zimene zikuchititsa zonsezi.
Kodi ankamudziwa bwanji munthu kuti ndi mfiti? Anthu onse amene akuwakayikira ankawamanga n’kuwaponya m’madzi enaake ozizira amene ankati ndi odalitsidwa. Aliyense amene wamira ankamuona kuti si mfiti ndipo ankamutulutsamo. Koma aliyense amene akuyandama, ankamuona kuti ndi mfiti ndipo ankamupha pomwepo, kapena ankam’pititsa kukhoti kuti akamuimbe mlandu. Ena amene akuwakayikira ankawakweza pasikelo, chifukwa ankakhulupirira kuti munthu wopepuka kwambiri ndi mthakati.
Buku lina linanena kuti njira ina imene ankadziwira kuti munthu ndi mfiti inali kumufufuza ngati ali ndi “chidindo cha Satana, chimene Satanayo anamusiyira posonyeza kuti ali naye pa mgwirizano.” (Witch Hunts in the Western World) Pofuna kupeza chidindochi, akuluakulu “ankameta munthu tsitsi n’kumufufuza paliponse, ndipo ankachita zimenezi pagulu. Akapeza kuti ali ndi njerewere, chiphudu kapena chipsera ankatenga singano n’kubaya pamalopo. Ngati sipanatuluke magazi kapena ngati munthuyo sanamve kuwawa, ankati chinthucho ndi chidindo cha Satana.
Khalidwe lozunza anthu powaganizira kuti ndi mfitili linkachitika m’mayiko a Akatolika ndi a Apulotesitanti omwe. Koma m’madera ena, Apulotesitanti ndi amene ankazunza kwambiri anthuwa kuposa Akatolika. Komabe m’kupita kwa nthawi, anthu anayamba kuona kuti zimene ankanena zokhudza ufiti zinali zabodza. Mwachitsanzo, mu 1631, wansembe wina dzina lake Friedrich Spee, anayendera limodzi ndi anthu amene anawagamula kuti ndi mfiti. Anthuwa ankapita nawo kukawamangirira kumtengo, n’kuwawotcha ali amoyo. Koma wansembeyu ananena kuti mogwirizana ndi zimene iye anapeza, pa anthu onsewo panalibe amene anali mfiti. Iye anachenjeza anthu kuti ngati angapitirizebe kupha anthu powaganizira kuti ndi mfiti, ndiye kuti dziko lonse likhala lopanda anthu. Kenako, madokotala anayamba kuzindikira kuti zinthu zimene zinkachititsa anthu kuganiza kuti ena ndi mfiti, zinkachitika chifukwa cha matenda osati chifukwa choti munthuyo ali ndi ziwanda kapena ndi mfiti. M’zaka za m’ma 1600, milandu yokhudza ufiti inayamba kuchepa ndipo chakumapeto kwa zakazi inatheratu.
Kodi zinthu zoopsa zimene zinachitika pa nthawi imeneyi zikutiphunzitsa chiyani? Mfundo yaikulu imene tikuphunzirapo ndi yakuti: Anthu amene amati ndi Akhristu akayamba kutsatira ziphunzitso ndi zikhulupiriro zabodza m’malo motsatira zimene Yesu Khristu anaphunzitsa, amachititsa kuti pazichitika zinthu zoipa kwambiri. Kusakhulupirika kwawoku kumachititsa kuti anthu azinyoza Chikhristu choona. Ndipotu Baibulo linachenjezeratu kuti zoterezi zimachititsa kuti, ‘anthu azilankhula monyoza njira ya choonadi.’—2 Petulo 2:1, 2.
^ ndime 2 Mayiko amene ankalamulidwa ndi mayiko a ku Ulaya akuphatikizapo mayiko a ku America.