Zochitika Padzikoli
United States
Mumzinda wa Los Angeles ku California kuli maloboti okwana pafupifupi 4,500. Maloboti onsewa awakonza moti azionetsa mtundu wofanana pa nthawi imodzi. Achita izi n’cholinga choti magalimoto amene adutsa pamaloboti, asamaime chifukwa cha magalimoto omwe aimitsidwa pamaloboti akutsogolo. Malinga ndi zimene nyuzipepala ina inalemba, mzinda wa Los Angeles ndi “mzinda waukulu woyamba kuchita zimenezi.”
Padziko Lonse
Kafukufuku amene anachitika padziko lonse anasonyeza kuti chiwerengero cha anthu okhala ndi vuto la kunenepa kwambiri chawonjezeka pa zaka za pakati pa 1990 ndi 2010. Kunenepa kwambiri kukupha anthu ochuluka katatu kuyerekeza ndi matenda obwera chifukwa cha kusowa zakudya m’thupi. Izi zili choncho ngakhale kuti m’mayiko ambiri mudakali vuto la kusowa chakudya. Mmodzi mwa anthu ochita kafukufuku wodziwika bwino, dzina lake Majid Ezzati, ananena kuti zimenezi zili ngati, “anthufe tachoka m’dziko losowa chakudya limene tinkakhala zaka 20 zapitazo, n’kusamukira m’dziko la zakudya zambiri koma zosapatsa thanzi. Zakudyazi zikutidwalitsa ndipo izi zikuchitika ngakhale m’mayiko osauka.”
Midway Island
Mbalame ina ya mtundu wa Laysan albatross yomwe ndi “mbalame yakale kwambiri padziko lonse,” yaswanso mwana wina. Mu 1956 mbalameyi inali ndi zaka 5, kusonyeza kuti panopa ili ndi zaka zoposa 60. Pa zaka zimene mbalame imeneyi yakhala ndi moyo, yauluka mtunda wamakilomita pafupifupi 4 miliyoni. Mtunda umenewu ndi wofanana ndi kuyenda ulendo wochoka padzikoli kupita kumwezi n’kubwerera, maulendo 6.
South Africa
Kafukufuku wina anasonyeza kuti azimayi a ku South Africa amasambira sopo komanso kudzola mafuta oyeretsa n’cholinga choti akhale ndi khungu loyera. Koma zinthu zoyeretsazi n’zoopsa ndipo n’zoletsedwa m’mayiko ambiri. Kuopsa kwina kwa zinthu zimenezi n’koti zimayambitsa khansa, vuto la impso, matenda ovutika maganizo, nkhawa, tizilonda tapakhungu komanso zipsera.