ZITHUNZI ZAKALE
Robert Boyle
Anthu ambiri okonda kuphunzira za mbiri yakale amamudziwa Robert Boyle kuti ndi wasayansi amene anatulukira zambiri zokhudza mmene gasi amagwirira ntchito. Asayansi ambiri akhala akutulukira zinthu zambiri potengera zimene Boyle anatulukirazi. Boyle ankadziwikanso kuti ankakhulupirira kuti kuli Mulungu komanso ankakhulupirira Mawu ake, Baibulo.
BOYLE anabadwa m’chaka cha 1627. Anabadwira m’banja lolemera ku nyumba yachifumu ya ku Lismore, m’dziko la Ireland. Imeneyi inali nthawi yomwe asayansi ena anayamba kufufuza zinthu n’cholinga choti anthu asamangokhulupirira zinthu zopanda umboni. Boyle anali m’gulu la asayansi amenewo. Moti pofotokoza za moyo wake ali wamng’ono ananena kuti anadzipatsa yekha dzina lakuti “Philaretus” kutanthauza kuti “Wokonda Choonadi.”
Boyle ankati akafufuza zinthu zinazake zatsopano, ankakonda kuuza aliyense zomwe watulukira. Iye analemba mabuku ambirimbiri ndipo zimene analembazo zinathandiza asayansi ambiri a m’nthawi yake, kuphatikizapo wasayansi wodziwika kwambiri, Sir Isaac Newton. M’chaka cha 1660, Boyle anakhala m’modzi mwa anthu amene anayambitsa bungwe lasayansi lotchedwa Royal Society, lomwe lidakalipo mpaka pano mu mzinda wa London m’dziko la England.
ANKAKONDA KWAMBIRI SAYANSI
Ena amakhulupirira kuti Boyle ndi amene anayambitsa sayansi yokhudza mmene zinthu zimapangidwira. Koma iye ankachita zosiyana ndi zimene asayansi ambiri ankachita nthawi imeneyo. Asayansi ambiri ankati akatulukira zinazake, ankazibisa kapena kuzilemba m’njira yoti anthu odziwa sayansi okha ndi amene angazimvetse, pomwe Boyle ankafalitsa zimene watulukira. Komanso m’malo mongokhulupirira zimene anthu ena ankanena, iye ankafufuza bwinobwino kenako n’kutsimikizira zoona zake.
Zimene Boyle anafufuza zinasonyeza kuti mfundo yoti chinthu chilichonse chinapangidwa ndi tizinthu ting’onoting’ono tolumikizana mosiyanasiyana ndi yoona.
Mfundo yoti asayansi asamangokhulupirira zinthu asanafufuze, anailemba m’buku lake lodziwika bwino lakuti The Sceptical Chymist. M’bukuli analembamonso kuti asayansi asamangokakamira mfundo zawo komanso azivomereza akalakwitsa. Iye analimbikitsanso asayansi ena omwe ankakakamira kuti mfundo zawo ndi zolondola, kuti azitha kusiyanitsa pakati pa zimene akudziwa kuti ndi zoona ndi zimene akungoganiza kuti ndi zoona.
Boyle analimbikitsa asayansi ena omwe ankakakamira kuti mfundo zawo ndi zolondola kuti azitha kusiyanitsa pakati pa zimene akudziwa kuti ndi zoona ndi zimene akungoganiza kuti ndi zoona.
ANKAKHULUPIRIRA MULUNGU
Boyle ankafufuzanso pa nkhani zokhudza Mulungu. Atafufuza za zinthu zodabwitsa zachilengedwe anayamba kukhulupirira kuti payenera kukhala winawake amene anazilenga. Zimenezi zinachititsa kuti asamagwirizane ndi anthu amene ankadziona ngati anzeru omwe ankakhulupirira kuti kulibe Mulungu. Boyle ananena kuti munthu wanzeru zake sanganene kuti kulibe Mulungu.
Komabe, Boyle ankaona kuti munthu payekha sangadziwe zoona pa nkhani zokhudza Mulungu. Ankaona kuti ndi Mulungu amene angamuthandize kuti adziwe zoona zake. Iye ananena kuti Mawu a Mulungu, omwe ndi Baibulo, ndi amene angatithandize kudziwa zoona za Mulunguyo.
Boyle ankamva chisoni chifukwa anthu ambiri sankadziwa zimene Baibulo limanena komanso ankangokhulupirira chilichonse chimene awauza kutchalitchi kwawo popanda umboni. Iye ankadabwa kuti, “Zingatheke bwanji kuti munthu azingokhulupirira zinazake chifukwa chotengera makolo ake.” Zimenezi zinachititsa kuti Boyle ayambe kufunafuna njira zothandizira anthu kulidziwa bwino Baibulo.
Choncho, Boyle anapereka ndalama zothandizira pa ntchito yomasulira Baibulo m’zinenero zambiri. Zina mwa zinenero zimenezi zinali Chiarabu, Chiairishi, Chimalaya, Chitheki ndi zinenero zina za ku North America. Robert Boyle anali munthu wanzeru koma wodzichepetsa. Iye ankafunitsitsa kudziwa zoona pa nkhani ina iliyonse komanso ankafunitsitsa kuthandiza anthu ena kuti nawonso adziwe zoona.