Ulendo Wokaona Anyani a Chiyendayekha
M’KATIKATI mwa nkhalango ya ku Central African Republic mumapezeka anyani amtundu wa chiyendayekha, omwe anthu ambiri sanawaonepo. Tinayenda kwa maola 12 mumsewu wafumbi kuti tikafike kunkhalango yotetezedwa ya Dzanga-Ndoki. Nkhalangoyi ili pakati pa dziko la Cameroon ndi la Republic of Congo ndipo ili ndi nyama za mitundu yosiyanasiyana. Ulendowu unali wokaona nyani winawake dzina lake Makumba pamodzi ndi banja lake.
Mayi amene ankatitsogolera pa ulendowu anatichenjeza kuti tisatayane komanso kuti tiziyenda mosamala chifukwa njira imene tinkadutsayo mumakonda kudutsa njovu zofunafuna zakudya. Koma panali nyama zina zimene tinafunika kusamala nazo kwambiri. Wotsogolerayo anatiuza kuti: “Nyani wa chiyendayekha akayamba kukuthamangitsani musathawe. Mungoima n’kuyang’ana pansi, musaphane naye maso. Mukatero sangakuvulazeni ndipo azingopanga phokoso basi. Ineyo ndimaona kuti ndibwino kungotsinzina.”
Pa ulendowu tinalinso ndi munthu wina wa mtundu wa BaAka, ndipo anthu ake amakhala afupiafupi kwambiri. Munthuyu anali ndi luso lodziwa kumene kuli nyama poona mapazi komanso zizindikiro zina za nyamazo. Munthu waluso limeneli amatha kudziwa kumene kuli nyama zomwe sizipezeka kawirikawiri. Iye amatha kumva fungo kapena phokoso la nyamazo ngakhale ali patali. Pomwe tinkayenda, njuchi zinkangotiulukiraulukira. Tinkavutika kuyenda m’nkhalangomo pomwe munthu waluso lolondola nyama uja ankangoyenda ndawala.
Ndiyeno munthu uja anayamba kulowera kumbali ina ya nkhalangoyi komwe azungu ambiri anali asanapiteko. Kenako tinangoona ataima n’kutilozera pamalo amene panali zizindikiro zosonyeza kuti ana aanyani amasewerapo. Pamalopo panali powandikawandika komanso nthambi zokhadzukakhadzuka zosonyeza kuti anyaniwo anali atangochokapo kumene. Pamenepa mitima yathu inali phaphapha kuti tatsala pang’ono kuona anyaniwo.
Titayenda ulendo wamakilomita 3, munthu uja anayamba kuyenda pang’onopang’ono chifukwa anaona kuti anyaniwo ali pafupi. Kuti asawadzidzimutse, anayamba kuchita phokoso ndi lilime lake, ngati limene anyani amapanga. Chapafupi tinkamva anyaniwa akudumpha m’mitengo kwinaku akupanga phokoso. Kenako mayi uja anatikodola kuti tifike pafupi n’kutiuza kuti tisachite phokoso lililonse. Anatiuza kuti tinjute kenako anatilozera pamene panali Makumba, amene ndi nyani yemwe tinkafuna kukamuona uja. Nyaniyu anali pamtunda wamamita 8 okha kuchokera pamene tinali.
Aliyense anangoti zii, chifukwa tinkachita mantha kuti akhoza kutivulaza akationa. Koma atationa, Makumba anatiyang’anitsitsa kenako n’kungoyasamula basi. Chimenechi chinali chizindikiro chosonyeza kuti watilandira. Pamenepa mitima yathu inakhala m’malo.
Mu chinenero cha Chiaka, dzina lakuti Makumba limatanthauza “Waliwiro.” Koma panthawi yonse imene tinkamuona, Makumba sankathamanga, ankangodya mtima uli m’malo. Chapafupi pake panali tiana tiwiri tikugirigishana n’kumagwetserana pansi. Panalinso kamwana kena dzina lake Sopo ndipo kankasewera pafupi ndi mayi ake dzina lake Mopambi. Kanyanika kanali ndi maso akuluakulu ndipo kanali kogulugusha moti kankati kakafuna kuchoka pali mayi akepo, mayiyo ankakakoka kuti kabwerere. Anyani enawo anali akuthyola masamba ndi nthambi za mitengo kapena kuthamangitsanathamangitsana. Ankati akatiyang’ana kwa nthawi yochepa, ankayambiranso kusewera.
Patatha ola limodzi, tinaganiza zobwerera. Nayenso Makumba anali atatopa nafe, choncho anangodzuma, kenako n’kudzuka kuyamba kulowera mbali ina ya nkhalangoyo. Pasanapite nthawi, anyani onsewo sanaonekenso. Ngakhale kuti anyaniwa tinangowaona kwa nthawi yochepa, ulendo umenewu sitidzauiwala mpaka kalekale.