Kuthana ndi Vuto la Kunenepa Kwambiri
NTHAMBI ya boma yoona za umoyo ku United States, inanena kuti, chiwerengero cha achinyamata komanso ana onenepa kwambiri chinawonjezeka kwambiri kuyambira mu 1980 mpaka mu 2002. Achinyamata komanso ana oterewa m’kupita kwa nthawi amadzadwala matenda othamanga magazi, shuga, mtima komanso mitundu ina ya khansa. *
Ana ambiri amanenepa pa zifukwa zosiyanasiyana monga kumangokhala osagwira ntchito iliyonse, kukopeka ndi zimene otsatsa malonda amanena ponenerera zakudya, komanso chifukwa chodya zakudya zonenepetsa kwambiri. Bungwe linanso la ku United States loona za kapewedwe ka matenda linanena kuti: “Ana ambiri amanenepa kwambiri chifukwa chodya zakudya zonenepetsa komanso kusachita masewera olimbitsa thupi.”
Ana, achinyamata komanso achikulire ayenera kuonanso bwino zomwe amadya. Njira zochitira zimenezi n’zosavuta. Mwachitsanzo, mnyamata wina dzina lake Mark, anazindikira kuti kusintha zimene amadya kunamuthandiza kwambiri kukhala ndi thanzi labwino komanso kuti azisangalala. Iye anati: “Poyamba ndinkakonda kudya zakudya zonenepetsa zokhazokha.” Mtolankhani wa Galamukani! anacheza ndi Mark kuti adziwe zimene anachita kuti asinthe zakudya zimene ankadya.
Kodi vuto lanu linayamba liti?
Linayamba nditangomaliza kumene sukulu ya sekondale. Nthawi imeneyo sindinkakonda kudya pakhomo chifukwa pafupi ndi kumene ndinkagwira ntchito panali malesitanti awiri moti ndinkakadya kumeneko pafupifupi tsiku lililonse. Ndinkaona kuti kuli bwino ndikadye kulesitanti kusiyana n’kuti ndiphike ndekha.
Nanga munatani mutayamba kukhala nokha?
Eee, zinthu zinafika poipa chifukwa sindinkatha kuphika komanso sindinkakhala ndi ndalama zambiri. Koma pafupi ndi nyumba imene ndinkakhalayo, panali lesitanti yomwe ankagulitsa zakudya zotchipa. Choncho ndinkaona kuti ndi bwino kumakangodya kumeneko. Komanso vuto lina linali lakuti ndinkadya kwambiri. Sindinkakhuta ndikadya mbale imodzi ya chakudya choncho ndinkaitanitsa mbale ina, ndinkagula chibotolo chachikulu cha zakumwa ndi zakudya zina zambiri.
Ndiye munasintha bwanji?
Nditangokwanitsa zaka 20, ndinayamba kuganizira kwambiri za thanzi langa chifukwa ndinali nditanenepa kwambiri. Ndinaona kuti ndinafunika kusintha chifukwa nthawi zonse ndinkakhala waulesi komanso ndinkadziona wachabechabe.
Ndiyeno munkatani kuti musamadye kwambiri?
Ndinayamba kusintha pang’onopang’ono. Ndinayamba kumadya pang’ono. Ndinkadziuza kuti: “Sikuti ichi ndi chakudya changa chomaliza. Ndikhoza kudyanso china mawa.” Nthawi zina ndinkachita kuchisiya chakudya patebulo. Koma ndinkasangalala chifukwa ndinkaona kuti ndayamba kuthana ndi vutolo.
Kodi pali zinthu zina zikuluzikulu zimene munafunika kusintha?
Pali zinthu zina zomwe ndinasiyiratu. Mwachitsanzo, ndinasiya kumwa zakumwa zoziziritsa kukhosi moti ndinkangomwa madzi basi. Zimenezi zinali zovuta kwambiri chifukwa ndinkakonda kwambiri zakumwa zoziziritsa kukhosi ndipo ndinkadana ndi madzi. Nthawi imeneyo ndinkati ndikamwa madzi ndinkamwanso juwisi kuti m’kamwa muzitsekemera. Koma kenako ndinayamba kukonda madzi.
Palinso zina zomwe munachita?
Eya. Nditasiya zakudya zonenepetsa ndinayamba kudya zakudya zina monga maapozi, nthochi ndi mavwende. Ndinayambanso kudya zakudya zokhala ndi mapulotini monga nyama ya nkhuku kapena nsomba. Patapita nthawi ndinayamba kukonda kwambiri zakudya zimenezi. Komanso ndimayesetsa kudya kwambiri masamba. Panopa ndinasiyiratu kudya zakudya zonenepetsa komanso ndimaona kuti ndikatolera tizakudya tina topatsa thanzi nthawi ya chakudya isanafike, zimathandiza kuti ndisadye kwambiri.
Ndiye kuti munasiyiratu kupita kulesitanti?
Ayi, ndimapita mwa apo ndi apo. Koma ndikapita ndimayesetsa kuti ndisadye kwambiri. Ngati andipatsa zakudya zambiri, ndimapempha kuti andipatse kabokosi koti ndiikemo zakudya zotsala kuti ndipite nazo kunyumba. Koma ndisanayambe kudya, ndimagawa chakudyacho pakati. Hafu ina ndimaika m’bokosimo kenako ndimadya hafu inayo. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndisamangodya n’cholinga choti ndimalize zimene zili m’mbale.
Kodi kusintha kumeneku kwakuthandizani bwanji?
Panopa sindine wonenepa kwambiri komanso ndine wamphamvu. Sindidzionanso ngati mmene ndinkadzionera kale. Komanso ndine wosangalala chifukwa ndimadziwa kuti ndimasamalira thanzi langa, zomwe zimasonyeza kuti ndimalemekeza mphatso ya moyo imene Mulungu anandipatsa. (Salimo 36:9) Poyamba ndinkaona kuti munthu akamasamalira thanzi lake amadzimana zinthu zambiri. Koma panopa ndaona kuti kusamalira thanzi langa n’kofunika kwambiri. *
^ ndime 2 Akatswiri azachipatala amanena kuti ana omwe ndi onenepa kwambiri akhoza kudzakhalanso onenepa kwambiri akadzakula.
^ ndime 20 Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu zochita pa nkhani ya zakudya. Aliyense ayenera kusankha yekha zakudya zoti azidya komanso angafunse adokotala zakudya zimene ayenera kudya. Pewani kumangodya zakudya zimene anthu ambiri otchuka amanena kuti n’zabwino koma zili zowononga thanzi lanu.