Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mwana Wanu Amaopa Akamva za Zimene Zachitika?

Kodi Mwana Wanu Amaopa Akamva za Zimene Zachitika?

“Mwana wanga wamkazi, yemwe ali ndi zaka 11 sakonda kuonera nkhani pa TV. Nthawi zambiri amalota zimene waonera. Tsiku lina anaonera nkhani yonena za munthu wina amene anadula mutu m’bale wake. Usiku umenewo analota munthu wina akumudula mutu.”​—Anatero Quinn.

“Mwana wa alamu anga wa zaka 6 anaonera nkhani pa TV zomwe zinkasonyeza kuti kwina kwake kunachitika chimphepo chowononga. Anakhala akuchita mantha kwa milungu ingapo. Nthawi zina ankandiimbira foni kumandiuza kuti akuona kuti kukubwera chimphepo ndipo chimupha.”​—Anatero Paige.

KODI mwana wanu amachita mantha akamva kapena kuonera nkhani zoopsa? Pakafukufuku wina amene anachitika, anapeza kuti makolo 40 pa 100 alionse, ananena kuti ana awo anachitapo mantha ataonera nkhani ina ndipo ankaopa kuti zimene aonerazo zikhoza kuwachitikira iwowo kapena abale awo.

Koma n’chifukwa chiyani amaopa? Chifukwa choyamba n’chakuti nthawi zambiri ana amaona zinthu mosiyana ndi mmene anthu aakulu amaonera. Mwachitsanzo, ana aang’ono amaganiza kuti ngati akungoonetsa nkhani mobwerezabwereza ndiye kuti zinthuzo zikungochitikabe mobwerezabwereza.

Chifukwa chachiwiri n’chakuti nkhani zoopsa zimene mwana angamaonere tsiku lililonse zingachititse kuti akhale ndi maganizo olakwika pa zimene zikuchitika padzikoli. N’zoona kuti tikukhala m’nthawi “yapadera komanso yovuta” ndipo anthu akukhaladi mwamantha. (2 Timoteyo 3:1) Koma ngati ana atamaonera nkhani zoopsa kawirikawiri akhoza kusokonekera maganizo chifukwa chochita mantha kwambiri. Bungwe lina linanena kuti: “Ana amene amakonda kuonera nkhani pa TV amaona kuti dzikoli ndi loipa kwambiri kuposa mmene lilili.”​—Kaiser Family Foundation.

Kodi mungatani ngati ana anu amachita mantha akamva nkhani zoopsa? Taonani zina zimene mungachite.

Muziwateteza.

Mungasankhe kuti ana anu asamaonere nkhani zina potengera msinkhu wawo komanso ngati mukuona kuti zingamawachititse mantha. Masiku ano pali njira zambiri zodziwira nkhani zambirimbiri, choncho ana amadziwa zimene zikuchitika. Mukhoza kudabwanso kuti ana aang’ono akudziwa zinthu zoti simumayembekezera kuti angazidziwe. Choncho muzichita chidwi ndi ana anu kuti mudziwe zimene zimawachititsa mantha.

Muziwaphunzitsa.

Ana anu akamakula, muzipeza nthawi yoonera limodzi nkhani pa TV ndipo muziwafotokozera zimene mwaonazo. Mungagwiritsenso ntchito mpata umenewu kuwaphunzitsa zina ndi zina. Mwina muziwafotokozera zinthu zabwino zimene azifotokoza mu nkhani imene yachitika. Mwachitsanzo, pakagwa tsoka la chilengedwe mungawafotokozere zimene anthu ena akuchita pofuna kuthandiza anthu amene akhudzidwa ndi tsokalo.

Muziwalimbikitsa.

Mukamva nkhani ya zinthu zoopsa zimene zachitika, muziwafunsa ana anu kuti mudziwe mmene akuonera nkhaniyo. Bambo wina, dzina lake Michael, ananena kuti: “Ine ndi mkazi wanga timapeza nthawi yofotokozera mwana wathu nkhani zimene waonera pa TV. Komanso timamufotokozera zinthu zina zimene tachita pofuna kuti zimene azifotokoza m’nkhaniyo zisatichitikire. Tsiku lina Nathaniel ataonera nkhani yosonyeza nyumba ikupsa anayamba kuchita mantha kuti nyumba yathunso ipsa. Pofuna kumulimbikitsa tinamuonetsa zipangizo zomwe zili m’nyumba mwathu zothandiza kudziwa ngati moto utayamba. Panopa amadziwa pamene zipangizozi zili komanso ntchito yake ndipo zamuthandiza kuti asamachite mantha.”

Musamachite mantha mopitirira malire.

Akatswiri ofufuza anapeza kuti pali anthu ena amene amaona kuti ngati aganizira kwambiri zoopsa ndiye kuti zikhoza kuchitikadi. Mwachitsanzo, ena akamva zoti anthu ena aba mwana amaganiza kuti mwana wawonso abedwa. N’zoona kuti tifunika kusamala kuti tipewe zinthu zoopsa, koma akatswiri amanena kuti chifukwa cha nkhani zimene anthu amaonera kapena kumva, ambiri amachita mantha ndi zinthu zoti sizingachitike n’komwe.​—Miyambo 22:3,13.

Ngati makolo amachita mantha kwambiri ndi nkhani zimene aonera, ana awonso angamachite mantha kwambiri. Mwachitsanzo, mu 2005 mnyamata wina wa ku United States wa zaka 11, anasowa kumapiri a ku Utah. Anthu atayamba kumufunafuna iye ankabisala poganiza kuti anthuwo akufuna amube ndipo anachita zimenezi kwa masiku 4. Pomwe anthu ofufuzawo ankamupeza n’kuti atafooka kwambiri. Ngakhale kuti nkhani za kubedwa kwa ana sizichitika kawirikawiri, mnyamatayu ankachita mantha kwambiri zomwe zinachititsa kuti afooke ndi njala m’malo moti athandizidwe.

“Ana a zaka kuyambira 3 mpaka 7 amachita mantha kwambiri ndi nkhani zokhudza masoka a chilengedwe ndi nkhondo, pomwe ana a zaka kuyambira 8 mpaka 12 amachita mantha kwambiri ndi nkhani zachiwawa komanso za anthu ophwanya malamulo.”​—Kaiser Family Foundation

Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Muzionetsetsa kuti inuyo komanso ana anu musamachite mantha kwambiri ndi nkhani zoopsa zimene mwamva. Dziwani kuti ngati nkhani yafika powonetsedwa pa TV ndiye kuti siichitika kawirikawiri.

Masiku ano sizachilendo kuona anthu akuphwanya malamulo, akuchita zachiwawa komanso kumva za masoka achilengedwe. Koma monga taonera, ngati mutayesetsa kuteteza, kuphunzitsa, kulimbikitsa ana anu komanso kupewa kuchita mantha mopitirira malire, mungathandize ana anu kuti asamachite mantha kwambiri ndi nkhani zoopsa zimene amaonera.