Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
“Anthu asanayambe kugwiritsa ntchito makompyuta, zinali zovuta kwambiri kwa akatswiri oona za maluwa ndi mitengo kuti azifufuza m’mabuku bwinobwino asanapereke dzina la mtengo kapena maluwa atsopano. Zimenezi zinachititsa kuti maluwa ndi mitengo yambiri ikhale ndi mayina ofanana.” Akuti pa mayina 1 miliyoni a mitengo ndi maluwa, mayina 477,601 amatanthauza zinthu zofanana.—SCIENCE, U.S.A.
“Pa anthu 100 alionse a ku China, ndi anthu 6 okha amene amaona kuti amasangalala.” Pa kafukufuku wina anapeza kuti, anthu pafupifupi 39 pa 100 alionse amakhulupirira kuti “chuma ndi chimene chimachititsa kuti anthu akhale osangalala kapena ayi.”—CHINA DAILY, CHINA.
“Kafukufuku wina amene anachitika ku Russia anasonyeza kuti ziwerengero zimene zilipo zokhudza kukula kwa umbava ndi umbanda m’dzikolo ndi n’zosalondola.” Akuti nthambi zoona za malamulo m’dzikolo zili ndi mlandu “woonjezera zinthu zabodza pa nkhani za umbava ndi umbanda” ndiponso wonama kuti achepetsa kwambiri mavuto a umbanda.—RIA NOVOSTI, RUSSIA.
“Pa ana atatu alionse a ku yunivesite mumzinda wa Berlin, ku Germany, mmodzi amaona kuti angayambe uhule [kapena kuvina molaula m’mabala] n’cholinga choti apeze ndalama zolipirira sukulu.”—REUTERS NEWS SERVICE, GERMANY.
Kudzikongoletsa Pokonzekera Kubereka
Masiku ano azimayi amene angobereka kumene akugwiritsa ntchito zipangizo zamakono zofalitsira nkhani. Zaka za m’mbuyomu, azimayi akafuna kudziwitsa ena kuti ali ndi mwana ankalemba makalata. Koma lipoti lochokera ku wailesi ya ku America ya ABC linati: “Azimayi a masiku ano amadziwitsa anzawo kuti ali ndi mwana pogwiritsa ntchito Intaneti.” Iwo amathanso kuika pa Intaneti zithunzi zawo ndi mwanayo atangobadwa kumene. Azimayi ambiri masiku ano, omwe amaona kuti kuoneka bwino ndi nkhani yaikulu, akumadzikongoletsa nkhope komanso kupentetsa zala asanabereke. Lipoti lija linapitirizanso kuti: “Azimayi ena amakonza zoti katswiri wokonza tsitsi adzakhalepo pa nthawi imene iwo akupita kuchipatala kuti akabereke.” N’chifukwa chiyani amachita zimenezi? Dokotala wamkulu pa chipatala china ku America (Boston’s Beth Israel Deaconess Medical Center), dzina lake Toni Golen, anati: “Amachita zimenezi kuti azioneka bwino akamakabereka.”
Muzichita Zinthu Zolimbitsa Thupi
Akatswiri ochita kafukufuku apeza kuti kumangoonerera TV, kukhala pansi kwa nthawi yaitali kuntchito kapena kusukulu kumayambitsa matenda aakulu. Nyuzipepala ina ya ku Canada inati: “Munthu akangokhala, mapulotini amene amathandiza kuti minyewa izichotsa ndi kusungunula mafuta m’thupi mwathu, sagwira ntchito kwambiri.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Anthufe sikuti timangofunika kuti mtima wathu uzigunda basi. Kuti tikhale ndi thanzi labwino, timafunika kuti nthawi zonse tizichita zinthu zolimbitsa thupi. Zimenezi zimathandiza kuti thupi lathu lizigaya bwino chakudya.”