Mapiko a Gulugufe
Kodi Zinangochitika Zokha?
Mapiko a Gulugufe
● Pali mitundu ina ya agulugufe yomwe mapiko ake amasinthasintha mtundu mogwirizana ndi malo amene munthu waima. Mapiko a gulugufeyu amakhala owala kwambiri moti munthu atha kumuona ali patali mamita 805. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti mapiko a gulugufeyu azioneka chonchi?
Taganizirani izi: Timizera ting’onoting’ono topindikira mkati timene timaoneka pamwamba pa phiko la gulugufe wagilini, timaoneka m’mitundu yosiyanasiyana chifukwa cha kuwala. Mwachitsanzo, kuwala kukafika pakati pa kamzera kalikonse pamaoneka mtundu wachikasu ndi gilini, pomwe kuwalako kukafika m’mphepete mwa timizerati, timaoneka tabuluu. Chinanso chimene chimachititsa kuti phikolo lizisinthasintha mitundu ndi chakuti kuwala kukafika pa timizera tija kumabwerera nthawi yomweyo pamene kuwala kumene kumafikira m’mphepete mwa timizerati, kumawalira kaye pa timizera tina. Zimenezi zimachititsa kuti mapikowo azioneka a mitundu yosiyanasiyana.
Asayansi zinawatengera zaka 10 kuti apange phiko lofanana ndi gulugufe wagilini. Iwo akukhulupirira kuti phiko limenelo lidzawathandiza kudziwa mmene angapangire ndalama zamapepala komanso makhadi akubanki oti anthu akuba sangathe kupanga makadi achinyengo potengera makadi amenewa. Komanso akukhulupirira kuti akhoza kupanga zipangizo zopangira magetsi kuchokera ku dzuwa potengera phiko la gulugufe. Komabe, kupanga chinthu chofanana ndi phiko la gulugufe si ntchito yamasewera. Pulofesa Ullrich Steiner, wa pa yunivesite ya Cambridge, anati: “Zinthu zachilengedwe zimatulutsa kuwala kokongola komanso kochititsa chidwi kwambiri moti zipangizo zamakono zotulutsa kuwala zimene akatswiri akupanga, sizingafanane ndi mmene zinthu zachilengedwezi zimachitira.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti gulugufe akhale ndi phiko lotere, kapena pali winawake amene analipanga?
[Chithunzi patsamba 24]
Gulugufe wagilini
[Chithunzi patsamba 24]
Phiko la gulugufe mukamaliona pogwiritsa ntchito chipangizo choonera zinthu zing’onozing’ono
[Mawu a Chithunzi patsamba 24]
Butterfly: Faunia, Madrid; microscopic view: © Eye of Science/Photo Researchers, Inc.