Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Zoti Banja Likambirane

Gwirizanitsani chithunzi ndi vesi lake

Werengani Mlaliki 2:3-10. Lembani mzere wolumikiza chithunzi chilichonse ndi vesi la m’Baibulo limene likugwirizana nalo. (Zithunzizo sizinaikidwe m’ndondomeko yake.) Malizitsani kujambula zithunzizi pozikongoletsa ndi chekeni.

1. Vesi 3

2. Vesi 4

3. Vesi 5

4. Vesi 6

5. Vesi 7

6. Vesi 8

A

B

C

D

E

F

KAMBIRANANI:

Kodi Solomo analidi wosangalala chifukwa cha zinthu zimene anakwanitsa kuchita pamoyo wake?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mlaliki 2:11.

Kodi Solomo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti zonse zinali “zachabechabe ndi kungosautsa mtima”? Kodi mungachite chiyani kuti mukhaledi wosangalala?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Luka 6:38; Machitidwe 20:35.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Werengani Mlaliki 3:1-8. Uzani aliyense m’banja lanu kuti alembe papepala chochitika chimodzi chotchulidwa m’mavesi amenewa. Ndipo ikani mapepalawo m’bokosi. Kenako uzani munthu aliyense kuti atolemo pepala limodzi, ndipo popanda kulankhula ayerekezere kuchita zimene zalembedwa papepalapo. Ndiyeno enanu muzinena chinthu chimene chikuyerekezeredwacho.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 11 YOSEFE

MAFUNSO

A. Lembani mawu amene akusowekapo. Azichimwene ake a Yosefe ankamutchula kuti “․․․․․ uja,” ndipo anamugulitsa ndi ndalama zasiliva zokwana ․․․․․.

B. Ataumirizidwa ndi mkazi wa Potifara kuti agone naye, Yosefe anakanitsitsa ndipo ananena kuti, “Ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi . . . ”?

C. N’chifukwa chiyani Farao anamusankha Yosefe kukhala wachiwiri kwa wolamulira wa ku Iguputo?

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa kwa Adamu Anakhala ndi moyo Baibulo

m’ma 1700 B.C.E. linamalizidw

kulembedwa

[Mapu]

Kuchoka ku Dotani kupita ku Iguputo

Dotani

IGUPUTO

YOSEFE

ANALI NDANI?

Mwana woyamba wa Yakobo wobadwa kwa Rakele. (Genesis 35:24) Abale ake ankamuchitira nsanje ndipo anamugulitsa ku Iguputo, komwe anakhala kapolo kwa zaka 13. M’malo mobwezera, iye anawakhululukira abale akewo. (Genesis 50:15-21) Ngakhale kuti anapita kudziko lachilendo, iye analemekeza Yehova komanso anapitirizabe kukhala wokhulupirika ndi wolimbikira ntchito.—Genesis 39:1-23.

MAYANKHO

A. Wolota, 20.—Genesis 37:19, 28.

B. “. . . n’kuchimwira Mulungu?”—Genesis 39:9.

C. Anadziwa kuti mzimu wa Mulungu unam’chititsa Yosefe kukhala wanzeru ndi wozindikira.—Genesis 41:38-41.

Anthu ndi Mayiko

7. Dzina langa ndine Anietie. Ndili ndi zaka 7, ndipo ndimakhala ku Nigeria. Kodi mukuganiza kuti ku Nigeria kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 190,000; 290,000 kapena 390,000?

8. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako lembani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Nigeria.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magaziniyi. Fotokozani chimene chikuchitika pachithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti, “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa Webusaiti ya www.isa4310.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 15

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. 1 likugwirizana ndi F.

2. 2 likugwirizana ndi E.

3. 3 likugwirizana ndi A.

4. 4 likugwirizana ndi C.

5. 5 likugwirizana ndi B.

6. 6 likugwirizana ndi D.

7. 290,000.

8. C.