Zoti Banja Likambirane
Zoti Banja Likambirane
Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?
Werengani 2 Mafumu 5:1, 9-16, 20-27. Kenako yang’anani chithunzichi. Tchulani zinthu zimene zikusowekapo. Lembani mayankho anu m’munsimu. Malizitsani kujambula chithunzichi polumikiza timadonthoto, ndipo chikongoletseni ndi chekeni.
1. ․․․․․
2. ․․․․․
3. ․․․․․
[Chithunzi]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
KAMBIRANANI:
Kodi Gehazi ananena mabodza awiri ati?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mafumu 5:22, 25.
Ndani ankadziwa kuti Gehazi akunama?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani 2 Mafumu 5:25, 26; 2 Mbiri 16:9; Aheberi 4:13.
N’chifukwa chiyani muyenera kupewa bodza?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Miyambo 12:22; Yohane 8:44.
ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:
Werengani nkhaniyi pamodzi m’Baibulo. Ngati n’kotheka, sankhani munthu mmodzi kuti akhale munthu wofotokoza nkhaniyo, wina akhale Elisa, wina akhale Namani, ena akhale anyamata a Namani, ndipo wina akhale Gehazi.
Sungani Kuti Muzikumbukira
Dulani, pindani pakati n’kusunga
KHADI LA BAIBULO 8 HEZEKIYA
MAFUNSO
A. Kodi Hezekiya anakhala mfumu ya Yuda ali ndi zaka zingati?
B. Kodi Yehova anatalikitsa moyo wa Hezekiya ndi zaka zina zingati?
C. Lembani mawu amene akusowekapo. Chifukwa cha pemphero limene Hezekiya anapereka komanso kukhulupirika kwake, Yehova anatumiza mngelo n’kupha asilikali a Asuri okwana ․․․․․ .
[Tchati]
4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.
Kulengedwa kwa Adamu Anakhala ndi moyo Baibulo limalizidwa cha m’ma 700 B.C.E. kulembedwa
[Mapu]
Ankakhala ku Yerusalemu
ASURI
Yerusalemu
HEZEKIYA
ANALI NDANI?
Mfumu yokhulupirika yomwe inakonza ndi kutsegulanso kachisi wa Mulungu, kuchotsa mafano, ndi kulimbikitsa anthu kuti azikumbukira Pasika. (2 Mafumu 18:4; 2 Mbiri 29:3; 30:1-6) Ngakhale kuti bambo ake, Mfumu Ahazi, anali munthu woipa, Hezekiya “anapitiriza kumamatira Yehova.”—2 Mafumu 18:6.
MAYANKHO
A. Zaka 25.—2 Mafumu 18:1, 2.
B. Zaka 15.—2 Mafumu 20:1-6.
C. 185,000.—2 Mafumu 19:15, 19, 35, 36.
Anthu ndi Mayiko
4. Mayina athu ndi Kyrl ndi Sheen. Tili ndi zaka 6 ndi 9. Timakhala m’dziko la Philippines. Kodi mukudziwa kuti ku Philippines kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 62,000; 126,000 kapena 172,000?
5. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko, ndipo kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi dziko la Philippines.
A
B
C
D
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 20
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31
1. Galeta la Namani.
2. Matumba a matalente a siliva.
3. Zovala.
4. 172,000.
5. D.