N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zauchigawenga?
N’chifukwa Chiyani Anthu Amachita Zauchigawenga?
JOSEBA, yemwe amakhala ku Spain, atafunsidwa kuti afotokoze zimene zinamuchititsa kuti alowe m’gulu la zigawenga, anati: “Tinkachitiridwa nkhanza komanso zinthu zopanda chilungamo, ndipo zinafika poti sitingazipirirenso. Apolisi ankatha kungobwera mumzinda wa Bilbao umene ndinkakhala, n’kuyamba kumenya komanso kumanga anthu.”
Joseba ananenanso kuti: “Tsiku lina apolisi anandimanga nditawadzudzula chifukwa cha nkhanza zimene ankachita. Atachita zimenezi, ndinakwiya kwambiri moti ndinkangofuna nditachita chinachake choopsa kuti anthufe tikhale pa ufulu.”
Kuponderezedwa
Ngakhale kuti sililimbikitsa anthu kuchita zachiwawa, Baibulo limati: “Kuponderezedwa kumapangitsa munthu wanzeru kuchita zinthu zopanda nzeru.” (Mlaliki 7:7) Ena amachita zachiwawa akaona kuti akuchitiridwa nkhanza chifukwa cha mtundu, chipembedzo kapena dziko lawo.
Mwachitsanzo, Hafeni, yemwe tinamutchula m’nkhani yapita ija, anati: “Tinkaponderezedwa ndi anthu obwera. Nyama sizifuna kuti zizisokonezedwa ndi nyama zimene zalowerera dera lawo, choncho ifenso tinkaona kuti tifunika kumenya nkhondo n’cholinga choti tizikhala mwaufulu m’dziko lathu.” Munthu wina amene anaphulitsa bomba la tinkenawo, ananena zotsatirazi asanafe: “Ngati simusiya kuphulitsa mabomba, kuponya mabomba otulutsa utsi wokhetsa misozi, komanso kumanga ndi kuzunza anthu a mtundu wathu, nkhondo imeneyi siitha.”
Chipembedzo
Ngakhale kuti zinthu zimene zimayambitsa uchigawenga ndi zokhudzana ndi ndale komanso zinthu zina, nthawi zambiri anthu amene amachita zauchigawenga amachita zimenezi m’dzina la chipembedzo. Mtsogoleri winawake wa dziko analandira uthenga kuchokera kwa mneneri wa gulu linalake la zigawenga, wakuti: “Sikuti tapenga kapena tikungofuna udindo wolamulira dziko. Tikuchita zonsezi potumikira Mulungu ndipo n’chifukwa chake nkhondo imeneyi siidzatha.”
Buku limene Daniel Benjamin ndi Steven Simon analemba lokhudza zauchigawenga zimene zimachitika m’dzina la chipembedzo, linati:
“Anthu ambiri padzikoli ayamba kukonda zopemphera ndipo ambiri amene ali m’zipembedzo zikuluzikulu kapena zing’onozing’ono, amakhulupirira kuti kuchita zachiwawa ndi umboni wakuti ndi odzipereka kwa Mulungu.” Munthu wina wochita kafukufuku, atafufuza nkhani zikuluzikulu zokhudza uchigawenga padziko lonse, anati: “Nkhani zonsezi zikusonyeza kuti zigawengazo zimakhulupirira kuti Mulungu amavomereza ngakhalenso kuzithandiza pa zochita zawozo.”Koma magulu ambiri a zigawenga omwe amachita zankhanza m’dzina la chipembedzo, nthawi zambiri amachita zinthu mopitirira malire, zomwe sizigwirizana ndi mfundo za chipembedzo chawo.
Zinakhazikika Mumtima Mwawo
Joseba, yemwe tamutchula kale uja, anazunzidwa kwambiri atamangidwa. Iye anati: “Nkhanza zimene anandichitira atandigwira zinandichititsa kuona kuti sikulakwa kudana nawo moti ndikanalolera kufa n’cholinga chomenyera ufulu.”
Komanso nthawi zambiri zimene anthu amaphunzitsidwa m’gulu lawo n’zimene zimachititsa kuti achite zauchigawenga. Hafeni ananena kuti: “Kumalo a anthu othawa kwawo kumene ndinkakhala, kunkachitika misonkhano yotiuza kuti azungu akufunafuna njira zotiponderezera.” Kodi zotsatira zake zinali zotani?
Hafeni ananena kuti: “Ndinayamba kuona kuti azungu ndi anthu oipa kwambiri. Sindinkakhulupirira mzungu aliyense. Sindinalekere pomwepo. Ndinayambanso kuganiza kuti mtundu wathu uyenera kuchitapo kanthu.”
N’zosangalatsa kuti patapita nthawi Joseba ndi Hafeni anasintha maganizo awo. Iwo anayamba kukondana ndi kukhulupirirana. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti asinthe? Nkhani yotsatira ifotokoza zambiri.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“Nkhanza zimene anandichitira atandigwira zinandichititsa kuona kuti sikulakwa kudana nawo moti ndikanalolera kufa n’cholinga chomenyera ufulu.”—Anatero Joseba