Guluu wa Nyongolotsi Yam’madzi
Kodi Zinangochitika Zokha?
Guluu wa Nyongolotsi Yam’madzi
● Madokotala amatha kulumikiza mafupa amene athyoka pogwiritsa ntchito masingano, zitsulo ndi timisomali. Koma zinthu zimenezi sizithandiza kwenikweni polumikiza timafupa ting’onoting’ono. M’mbuyomu, akatswiri ofufuza sankadziwa kuti angatani kuti apange guluu wolimba kwambiri amene sangasungunuke akamatira mafupa. Koma ataphunzira mmene nyongolotsi inayake yam’madzi imapangira guluu, iwo anaona kuti akhoza kupanga guluu wolimba kwambiri.
Taganizirani izi: Nyongolotsi imeneyi imamanga nyumba yake m’madzi pogwiritsa ntchito timichenga ndi tiziganamba ting’onoting’ono. Iyo imalumikiza zinthu zimenezi ndi guluu wolimba kwambiri amene amapangidwa pa khosi pake. Guluu ameneyu ndi wolimba kwambiri kuposa guluu aliyense amene anthu amagwiritsa ntchito masiku ano. Guluuyu ali ndi mapulotini enaake amene amati akaphatikizana, amauma mofulumira kwambiri ngakhale ataikidwa m’madzi. Nyongolotsi imeneyi imadziwika kuti ndi katswiri wodziwa kumanga. Russell Stewart, yemwe ndi mphunzitsi payunivesite ya Utah, ananena kuti kanyongolotsi kameneka kathandiza asayansi kupeza nzeru zopangira guluu wolimba kwambiri.
Akatswiri ochita kafukufuku ayamba kupanga guluu wosiyanasiyana potengera guluu wa nyongolotsi yam’madzi imeneyi. Koma akuti guluu amene akupangayu ndi wolimba kwambiri kuposa guluu wa nyongolotsiyi. Guluu amene azidzagwiritsidwa ntchito polumikiza mafupa amene athyoka, adzakhala woti azidzasungunuka fupalo likamapola. Ngati guluu ameneyu azidzathandizadi kwambiri m’zipatala, madokotala adzasangalala kwambiri.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti nyongolotsi yam’madzi imeneyi izipanga guluu wolimba kwambiri chonchi, kapena zimenezi ndi umboni wakuti alipo amene anaipanga?
[Chithunzi patsamba 26]
Akatswiri ochita kafukufuku ali ndi chiyembekezo chakuti azidzalumikiza mafupa othyoka popanda kugwiritsa ntchito zitsulo
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Sandcastle worm: © Peter J. Bryant, University of California, Irvine