Ngakhale Ana Aang’ono Akhoza Kuphunzira
Ngakhale Ana Aang’ono Akhoza Kuphunzira
● Izi n’zimene mayi wina wa ku California, m’dziko la America, analemba zokhudza nkhani inayake imene inafotokozedwa m’buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Iye anati: “Mlungu watha tinapita kuchipatala ndi mwana wathu wamwamuna wazaka zitatu, dzina lake Javan. Kuchipatalako, adokotala anafunsa ineyo ndi mwamuna wanga ngati tinakambirana kale ndi mwana wathuyo za momwe angadzitetezere kwa anthu ofuna kumuseweretsa maliseche. Ndinasangalala kuwauza kuti tili ndi buku la Mphunzitsi Waluso, lomwe limathandiza makolo kufotokozera ana kuti sayenera kulola munthu wina aliyense kuwaseweretsa maliseche. Adokotalawo anagoma kwambiri kumva kuti tinakambirana kale zimenezi ndi mwana wathu.”
Mayiyu ananenanso kuti: “Bukuli limafotokoza nkhani imeneyi m’njira yabwino kwambiri.” Nkhani imene mayiyu ankanena ndi yamutu wakuti, “Mmene Yesu Anatetezedwera.” Mutuwu umafotokoza mmene Atate a kumwamba a Yesu anamutetezera kwa Herode, mfumu yoipa imene inkafuna kumupha ali khanda loti silikanatha kudziteteza lokha. (Mateyu 2:7-23) Kenako mutuwu umafotokozanso momwe ngakhale ana aang’ono kwambiri angadzitetezere ngati munthu wina akufuna kuwachita zachipongwe.
Mukhoza kuitanitsa buku la masamba 256 la zithunzi zokongola limeneli, lomwe masamba ake ndi aakulu mofanana ndi masamba a magazini ino. Kuti muitanitse, lembani zofunika m’munsimu ndipo tumizani ku adiresi yoyenera pa maadiresi amene ali patsamba 5 m’magazini ino.
□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.
□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.