Mawotchi Amakedzana
Mawotchi Amakedzana
● Ku China n’kumene kunayambira mawotchi ochita kudyetsera, zaka zoposa 900 zapitazo. Kuyambira nthawi imeneyo, mawotchi akhala akusintha. Koma anasintha kwambiri pakatikati pa zaka za m’ma 1600, pamene anayamba kuikidwa kachitsulo kopita uku ndi uku. Chifukwa cha kachitsulo kameneka, mawotchi anayamba kukhala olondola kwambiri moti anakhala ndi muvi wa maminitsi, umene kale analibe. Mawotchi atsopanowa, okhala ndi kachitsulo kopita uku ndi uku komanso zitsulo zina zolemera, ankafunika kuwamangira kanyumba kabwino kuti azikhazikika bwino. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu ayambe kupanga mawotchi ataliatali, amene katswiri wina wa mawotchi anawafotokoza kuti ndi “mawotchi odalirika komanso osunga nthawi kwambiri, ngakhale nyengo ikhale yoipa.”
Poyamba, mawotchi amtengo wapatali amenewa ankapangidwa m’mizinda ikuluikulu yokha ya ku Ulaya, monga ku London ndi ku Paris. Koma pang’ono ndi pang’ono, anayambanso kupangidwa m’mayiko ambiri a ku Ulaya. Mawotchiwa anayamba kukongoletsedwa m’njira zosiyanasiyana, mogwirizana ndi dera limene apangidwa. Mawotchiwo ankatha kukhala owongoka kapena opindika, ndiponso ankatha kukhala owonda kapena onenepa. Kanyumba kake kankapangidwa ndi matabwa a mitengo yosiyanasiyana monga paini, phingo, mlombwa ndi mitengo ina, ndipo kankakhala kopanda chokongoletsa chilichonse kapenanso ankakakongoletsa kwambiri. Choncho mawotchiwa anafala kwambiri chifukwa ankasunga kwambiri nthawi komanso ankachititsa kuti m’nyumba muzioneka mokongola komanso molemekezeka.
N’kutheka kuti palinso chifukwa china chimene chimachititsa kuti anthu azikopekabe ndi mawotchiwa. Mwina chifukwa chake n’chakuti mawotchiwa amaoneka ngati munthu. Wochita kafukufuku wina wa ku Finland dzina lake Dr. Sinikka Mäntylä anati: “Mawotchiwa ndi aatali mofanana ndi msinkhu wa munthu ndipo ali ndi nkhope yofananirako ndi ya munthu.” Komanso kulira kwa wotchiyi kumamveka ngati kugunda kwa mtima wa munthu. Masiku ano, kuli mawotchi otchipa komanso olondola kwambiri amene alowa m’malo mwa mawotchi ataliatali amakedzanawa. Koma ngakhale kuti anthu akukhala moyo wotanganidwa kwambiri masiku ano, munthu akaona wotchi yamakedzanayi imamukhazika mtima pansi. Buku lina linanena kuti: “Mawotchiwa amatikhazika mtima pansi chifukwa cha kulira kwawo kwapang’onopang’ono ndipo amatikumbutsa za nthawi imene anthu ankakhala mwabata kwambiri.”—Keeping Time—Collecting and Caring for Clocks.
[Chithunzi patsamba 19]
Wotchi imene mwina inapangidwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800. Akaidyetsera imatha masiku 9 isanayambe kutaya