“Choonadi Chidzakumasulani”
“Choonadi Chidzakumasulani”
MAWU amenewa, amene analankhulidwa ndi Yesu Khristu ndipo amapezeka m’Baibulo pa Yohane 8:32, ndi oona ndipo adzakhalabe oona mpaka kalekale. Kudziwa choonadi kumatimasula ku miyambo ndi zikhulupiriro zimene sizisangalatsa Mulungu, ndiponso zimene zikhoza kutiika m’mavuto. Nkhani zotsatirazi zikusonyeza momwe choonadi cha m’Baibulo chamasulira anthu a m’mayiko osiyanasiyana ku miyambo ina yolemetsa yokhudzana ndi Khirisimasi.
Choonadi cha m’Baibulo Chinawamasula
Argentina Oscar anati: “Banja lathu lamasuka ku mavuto amene tinkakumana nawo chifukwa cha kudya ndi kumwa mopitirira muyezo. Komanso tasiya kuvutika kugula mphatso zomwe tinkakakamizika kugula poyamba.”
Mario anaona kuti wamasuka ataphunzitsidwa kuti Khirisimasi inachokera ku zinthu zabodza zokhazokha. Iye anati: “Panopa ndimasangalala chifukwa
ndimapatsa anthu mphatso pa nthawi iliyonse imene ndingakonde komanso pamene ndili ndi ndalama zokwanira zochitira zimenezo.”Canada Elfie analemba kuti: “Ndimakonda kupatsana mphatso ndi anthu. Koma sindisangalala ndi mphatso zopereka mokakamizika. Banja lathu litasiya kukondwerera Khirisimasi, tinapuma, ndipo tinamva ngati kuti tatula chimtolo cholemera.”
Ulli, mmodzi wa ana aakazi a Elfie, anati: “Makolo athu atasiya kukondwerera Khirisimasi, ankatikonzera zinthu zosiyanasiyana zosangalatsa zoti tichite komanso ankatipatsa mphatso pa masiku amene sitinali kuyembekezera, ndipo ankachita zimenezi nthawi ina iliyonse pa chaka. Zimenezi zinkatisangalatsa kwambiri. Anzathu a m’kalasi akatifunsa kuti tikukondwerera chiyani, tinkangowayankha monyadira kuti, ‘Palibe!’ Komabe, sizinali zophweka kwa makolo athu kuti asinthe n’kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo, chifukwa achibale awo ankalimbana nawo kwambiri. Koma iwo sanagonje. Ndinaona kuti iwo anali ofunitsitsa kulambira Yehova Mulungu m’njira imene iye amafuna, ndipo zimenezi zinandipatsa chitsanzo chabwino kwambiri.”
Silvia ananena kuti anapeza mpumulo atasiya kukondwerera Khirisimasi. Iye anati: “Pambuyo pake, ndinayamba kusangalala kwambiri. Ndinkadziwa kuti ndikukondweretsa Yehova Mulungu, ndipo zimenezi zinandichititsa kumva bwino kwambiri kuposa mmene munthu angamvere atachita maphwando a Khirisimasi maulendo masauzande ambiri.”
Kenya Peter analemba kuti: “Pamene ndinkakondwerera Khirisimasi, ndinkakongola ndalama zambiri zogulira mphatso komanso zakudya zambirimbiri zodula. Kuti ndikwanitse kubweza ngongolezi, ndinkafunika kugwira ntchito kwa nthawi yaitali, ndipo sindinkakhala ndi nthawi yocheza ndi banja langa. Ndinasangalala kwambiri pamene ndinamasuka ku mavuto onsewa.”
Carolyne ananena kuti: “Ndimapatsana mphatso ndi achibale anga ndi anzanga nthawi ina iliyonse. Ndimaona kuti mphatso zimene sukuziyembekezera komanso zimene munthu amapereka mochokeradi pansi pa mtima, n’zimene munthu amasangalala nazo kwambiri.”
Japan Hiroshi ndi Rie anati: “Ana athu sayembekezera kuti tiziwapatsa mphatso nthawi zonse, zimene zingawapangitse kuti asamayamikire mphatsozo. Ifeyo monga makolo awo timasangalala kwambiri tikaona kuti anawo akumvetsa kuti munthu ayenera kupereka mphatso kuchokera pansi pa mtima.”
Keiko anati: “Kale banja lathu linkakondwerera Khirisimasi. Tikaona kuti mwana wathu wagona, ine ndi mwamuna wanga tinkaika mphatso pafupi ndi bedi lake. Tsiku lotsatira tinkamuuza kuti; ‘Popeza wasonyeza kuti ndiwe mwana wabwino, Father Christmas wakubweretsera mphatso.’ Koma titaphunzira za chiyambi cha Khirisimasi, ndinamuuza mwana wanga zimene ndinaphunzirazo. Iye anadabwa kwambiri ndipo analira chifukwa anazindikira kuti takhala tikumunamiza. Apa ndinazindikira kuti mabodza amene anthu amanena pa Khirisimasi si nkhani yamasewera ngati mmene amaganizira. Ndinamva chisoni kwambiri ndipo ndinazindikira kuti sindinkachita bwino kunamiza mwana wanga.”
Philippines Dave anati: “N’zovuta kufotokoza chimwemwe chimene Yehova amatithandiza kukhala nacho kudzera m’choonadi chopezeka m’Baibulo. Anthu a m’banja lathu akapatsa munthu mphatso, sayembekezera kuti munthuyo awapatsenso mphatso. Ndipo timapereka mochokera pansi pa mtima.”
Anthu amene tawatchulawa ndi ena chabe mwa anthu mamiliyoni ambiri amene adzionera okha kuti choonadi cha m’Baibulo chimamasula. Komanso, chinthu china chofunika n’chakuti tikamatsatira mfundo za choonadi, timasangalatsa mtima wa Mulungu. (Miyambo 27:11) Yesu Khristu anati: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Kodi Mulungu akayang’ana mumtima mwanu, amaona kuti mumalakalaka mutadziwa choonadi? Sitikukayikira kuti yankho lanu ndi lakuti, inde.
[Chithunzi patsamba 9]
Akhristu amapatsana mphatso nthawi ina iliyonse pa chaka ndipo amachita zimenezi chifukwa cha chikondi