Kodi Tiyenera Kupemphera kwa “Oyera”?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Tiyenera Kupemphera kwa “Oyera”?
Marie ndi Theresa ankayesetsa kutsatira zonse zimene tchalitchi chawo cha Katolika chimaphunzitsa. Onse ankakhulupirira “oyera.” Marie ankakhulupirira kuti kupemphera kwa “oyera” kungamuthandize pa mavuto ake. Theresa ankapemphera nthawi zonse kwa “woyera” amene ankamukhulupirira kuti amasamalira ndi kuteteza mudzi wawo. Ankapempheranso kwa “woyera” wina amene anali ndi dzina lofanana ndi lake.
MOFANANA ndi Marie ndi Theresa, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse amapemphera kwa oyera awo kuti awadalitse. Buku lina lachikatolika linati ‘oyera amakhala ngati amkhalapakati a anthu ndi Mulungu. Ndipo “ndi zabwino komanso zothandiza” kupemphera kwa iwowa tikafuna kuti Mulungu atidalitse.’—New Catholic Encyclopedia.
Koma kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani imeneyi? Kodi iye amaona kuti n’zoyenera kupemphera kwa “oyera” monga amkhalapakati athu? Taonani zimene Baibulo limanena.
Kodi Ndi Bwino Kupemphera kwa “Oyera”?
Palibe paliponse m’Baibulo pamene pamanena kuti munthu wina wolambira Mulungu mokhulupirika anapempherapo kwa “oyera.” N’chifukwa chiyani? Buku lachikatolika lija linanenanso kuti: “Kuyambira m’zaka za m’ma 200 A.D. m’pamene anthu anayamba kuona kuti kupemphera kwa oyera ngati amkhalapakati awo n’kothandiza.” Apa n’kuti patadutsa zaka zoposa 200 kuchokera pamene Khristu anamwalira. Choncho chiphunzitso chimenechi sichinachokere kwa Yesu kapena kwa anthu amene anauziridwa kulemba za utumiki wake m’Baibulo. N’chifukwa chiyani iwo sanaphunzitse zimenezi?
Baibulo limatiuza kuti tiyenera kupemphera kwa Mulungu yekha, kudzera mwa Yesu Khristu. Yesu anati: “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.” (Yohane 14:6) Mawu omveka bwino amenewa akugwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa, zolembedwa pa Mateyu 6:9-13. Pofotokoza nkhani ya pemphero, Yesu anauza otsatira ake kuti: “Muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’” (Mateyu 6:9) Apa n’zoonekeratu kuti tiyenera kupemphera kwa Atate wathu wakumwamba yekha. Mfundo imeneyi ikuchokera pa mfundo ina yofunika kwambiri ya m’Baibulo.
Pemphero ndi Mbali ya Kulambira
Buku lina linati: ‘Pemphero limatanthauza mawu aulemu kapena maganizo amene munthu amauza Mulungu, milungu, ndi zinthu zina zimene anthu amazilambira. . . . Pemphero ndi njira yofunika kwambiri yolambirira pafupifupi m’zipembedzo zonse za padziko lapansi.’ (The World Book Encyclopedia) Dzifunseni kuti, ‘Kodi n’zoyenera kuti munthu agwade n’kumapemphera kwa munthu wina m’malo mopemphera kwa Mlengi wathu amene anatipatsa moyo?’ (Salimo 36:9) Yesu anati: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Baibulo limanenanso kuti Mlengi wathu amafuna kuti “anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.”—Deuteronomo 4:24; 6:15.
Taganizirani chitsanzo cha mtumwi wachikhristu Yohane. Ataona masomphenya ochititsa chidwi amene iye anadzawalemba m’buku la Chivumbulutso, mtumwiyo anachita mantha ndipo ‘anagwada n’kuwerama kuti alambire pamapazi a mngelo amene anali kumuonetsa zinthu zimenezi.’ Kodi mngeloyo anatani? Anamuuza kuti: “Samala! Usatero ayi! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, ndi wa abale ako . . . Lambira Mulungu.” (Chivumbulutso 22:8, 9) Apanso Baibulo likutilimbikitsa kuti tiyenera kulambira Yehova Mulungu yekha.
Mogwirizana ndi mfundo zimenezi, Mulungu yekha ndi amene amatchedwa “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Komanso popeza ndi Wamphamvuyonse, iye yekha ndi amene ali ndi ulamuliro, nzeru ndi mphamvu zoyankha mapemphero. (Yobu 33:4) Ngakhale Yesu Khristu anavomereza kuti pali zinthu zina zimene iye sangathe kuchita. (Mateyu 20:23; 24:36) Komabe, iye wapatsidwa udindo waukulu, kuphatikizapo wotumikira monga mkhalapakati wa anthu ndi Mulungu.
Mkhalapakati Wachifundo
Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Iye akhoza kupulumutsa kwathunthu anthu amene akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye, chifukwa adzakhalabe ndi moyo nthawi zonse ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.” (Aheberi 7:25) Zimenezi zikutanthauza kuti Yesu akhoza kukhala mkhalapakati wachifundo wa anthu amene “akufika kwa Mulungu kudzera mwa iye.” Koma sizikutanthauza kuti tizipemphera kwa Yesu kuti atifikitsire mapemphero athuwo kwa Mulungu. M’malomwake, tiyenera kupemphera kwa Mulungu m’dzina la Yesu, posonyeza kuti tikuzindikira ulamuliro wake. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ali Mkhalapakati wabwino kwambiri?
Chifukwa chimodzi n’chakuti Yesu anakhalapo munthu padziko lapansi ndipo zimenezi zinamuthandiza kuti azimvetsetsa bwino mavuto amene anthu amakumana nawo. (Yohane 11:32-35) Ndiponso iye anasonyeza kuti amakonda anthu pochiritsa odwala, kuukitsa akufa, ndi kuphunzitsa zinthu zauzimu kwa anthu onse omwe ankabwera kwa iye. (Mateyu 15:29, 30; Luka 9:11-17) Iye ankakhululukiranso anthu machimo awo. (Luka 5:24) Zimenezi zimatilimbitsa mtima chifukwa timadziwa kuti tikachimwa, “tili ndi mthandizi wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.”—1 Yohane 2:1.
Tiyenera kuyesetsa kutsanzira chikondi ndi chifundo cha Yesu. N’zoona kuti ifeyo sitinapatsidwe udindo wokhala amkhalapakati. Komabe tikhoza kupempherera anthu ena. Ndipotu chikondi chiyenera kutichititsa kufuna kupempherera anzathu. Yakobo analemba kuti tiyenera “kupemphererana . . . Pembedzero la munthu wolungama limagwira ntchito mwamphamvu kwambiri.”—Yakobo 5:16.
Marie ndi Theresa anadziwa mfundo zabwino za choonadi ataphunzira Baibulo. Mboni za Yehova zikukupemphani kuti inunso mutero. Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, “omulambira [Mulungu] ayenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.”—Yohane 4:24.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
● Kodi Yesu anati tizipemphera kwa ndani yekha?—Mateyu 6:9.
● Kodi Yesu ali ndi udindo wotani?—Aheberi 7:25.
● Kodi ndi bwino kupempherera anthu ena?—Yakobo 5:16.