“Anthu Asiyiratu Kukhulupirirana”
“Anthu Asiyiratu Kukhulupirirana”
Ku West Africa, mnyamata wina wa zaka 12 anagonekedwa m’chipatala atamwa mankhwala achabechabe a malungo amene mayi ake anagula ku sitolo yogulitsa mankhwala yovomerezedwa ndi boma. Dokotala wina anati: “Kwa zaka 15, takhala tikupeza mankhwala achinyengo akugulitsidwa m’malo osiyanasiyana.” *
Makolo a mwana wongobadwa kumene ku Asia anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti mkaka umene ankapatsa mwana wawo, womwe ankati umawonjezera mavitamini, unali ndi mankhwala enaake oopsa. Kenako mwanayo anamwalira chifukwa cha mkaka umenewu.
Munthu wina wabizinezi ku America, yemwe anthu ankamukhulupirira kwambiri, anapezeka kuti ndi wachinyengo ndipo ankabera anthu ndalama zambirimbiri. Anthu ambiri anakhumudwa atazindikira kuti ndalama zawo za penshoni zimene ankasungitsa kwa mkuluyu zalowa m’madzi. Ndipo akatswiri azachuma akuti zimene mkuluyu wakhala akuchita ndi “chinyengo chachikulu chomwe sichinachitikeponso m’zaka 100 zapitazi.”
PAFUPIFUPI munthu aliyense anakhumudwitsidwapo ndi munthu amene ankamukhulupirira kwambiri, munthuyo atamuchitira zachinyengo. Malinga ndi nyuzipepala ya ku France ya Le Monde, mavuto azachuma omwe ali padziko lonse anayamba makamaka chifukwa chakuti “anthu asiyiratu kukhulupirirana.”
Kodi n’chiyani chachititsa kuti anthu ‘asiye kukhulupirirana’ masiku ano? Kodi pali munthu amene mungamukhulupirire?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 2 Nkhaniyi inalembedwa m’nyuzipepala ya Le Figaro, yomwe imasindikizidwa ku Paris, m’dziko la France.