Mfumu ya Nkhalango za ku America
Mfumu ya Nkhalango za ku America
KODI mukuganiza kuti mfumu imeneyi ndi ndani? Mfumu imeneyi ndi nyama inayake yamphamvu kwambiri yomwe imaoneka ngati kambuku. Nyamayi imapezeka m’nkhalango, m’madambo, m’thengo ndiponso m’zipulululu za ku Central ndi South America. Nyamayi imatha kukhala pamtunda ndi m’mitengo ndipo mosiyana ndi mkango, kambuku, nyalugwe ndi nyama zina zamtunduwu, imathanso kukhala m’madzi.
Nyamayi imakhala yaitali mamita awiri, osawerengera mchira wake, ndipo imalemera makilogalamu 120 kapena kupitirira. Imakonda kukhala yokha ndipo imangokumana ndi zinzake ikamafuna yaikazi kapena yaimuna. Yaimuna imayamba kufuna zazikazi ili ndi zaka zitatu kapena zinayi pamene yaikazi imayamba kubereka ili ndi zaka ziwiri. Nyamayi ikatenga bere pamapita miyezi itatu kapena inayi kuti ibereke ndipo nthawi zambiri imabereka ana awiri. Nyamazi akaziweta kumalo osungirako nyama zimatha kukhala zaka zoposa 20.
Nyamazi n’zosowa kwambiri ndipo sizipezeka wamba. Katswiri wina ananena kuti: “Nyamayi imadziwa kubisala moti mukhoza kukhala nayo pafupi kwambiri koma osaiona.” Nyamayi imakhala ndi ubweya wachikasu koma wotuwirako, wokhala ndi mizere yakuda yozungulira, yomwe imakhalanso ndi timadontho takuda pakati pake. Mtundu wakewu ndi umene umathandiza kuti ikabisala zizikhala zovuta kuiona.
Imakonda Kuyenda Yokha Ndipo Imasaka Mwakachetechete
Nyamayi imadziwa kusaka ndipo imadya nyama zamitundu yosiyanasiyana yokwana pafupifupi 85, kuphatikizapo agwape ndi anyani. Popeza nyamayi imakhalanso m’madzi, imagwira nsomba ndi akamba am’madzi mosavutikira. Anthu ena anaonapo nyamayi itapha hatchi yaikulu n’kuikoka mtunda wokwana pafupifupi mamita 80, kenako n’kuwoloka nayo mtsinje.
Nthawi zambiri nyamayi ikafuna kugwira nyama ina, imabisala mumtengo n’kumadikirira mwakachetechete. Mwachitsanzo, pansi pa mtengowo pakamadutsa gulu la nguluwe, imazidumphira n’kugwirapo imodzi. Ikangoluma kamodzi kokha, nguluweyo imaferatu ndipo nyamayi imadumphiranso mumtengo muja. Imadikirira kuti nguluwe zina zija zidutse, kenako imatsikanso n’kukatenga nguluwe yakufa ija.
Koma mosiyana ndi akambuku ndi mikango, nyama imeneyi sikonda kugwira anthu, moti sinayambe yaikidwapo m’gulu la nyama zodya anthu. Ngakhale zili choncho, anthu ndi amene amapha kwambiri nyamazi.
N’chifukwa Chiyani Zilipo Zochepa?
Kale nyamazi zinkapezeka m’dera lalikulu kwambiri, kuyambira kum’mwera kwa dziko la United States mpaka kumayiko a kum’mwera kwa South America. Koma masiku ano, sizikupezekanso m’madera ambiri amene zinkapezeka zaka 100 zapitazo. Mpaka kufika zaka za m’ma 1970, alenje ankapha kwambiri nyamazi kuti apeze zikopa
zake. M’chaka cha 1968 chokha, nyama zokwana 13,500 zinaphedwa n’kutumizidwa kumayiko ena kuchokera ku mayiko a ku America. M’chaka cha 2002, akuti mwina nyama zimenezi zinalipo zosapitirira 50,000. Panopa, mwina nyama zimene zatsala kuthengo zilipo pafupifupi 15,000.Bungwe lina loona zoteteza nyama zakuthengo linati pafupifupi theka la malo onse amene nyamazi zinkakhalako awonongedwa chifukwa cha kudula mitengo mwachisawawa. Mwachitsanzo, akuti ku Mexico, malo okhala nyamazi aakulu ngati bwalo la mpira amawonongedwa mphindi iliyonse. Zimenezi zimachititsa kuti nyamazi zizigwira ziweto kuti zipeze chakudya.
Anthu Akuyesetsa Kuteteza Nyamazi
Mayiko pafupifupi 200 amatsatira malamulo a bungwe linalake lapadziko lonse loletsa kugulitsa nyama zimene zatsala pang’ono kutha, kuphatikizapo nyama zimenezi. Mayiko ena akhazikitsa malo osungirako nyamazi pofuna kuziteteza. M’chaka cha 1986, dziko la Belize linakhazikitsa malo enaake osungirako nyama zimenezi, omwe ndi oyamba padziko lonse lapansi. Ku Mexico nakonso anapatula nkhalango yokwana maekala 370,000 m’kati mwa malo enaake osungirako nyama kufupi ndi nyanja ya Atlantic, kuti azisungirako nyamazi.
N’zosangalatsa kuti anthu akuyesetsa kuteteza “mfumu ya nkhalango” imeneyi, koma sitikudziwa kuti angaiteteze mpaka pati. Komabe, n’zolimbikitsa kudziwa kuti posachedwapa Mlengi wathu wachikondi ‘adzawononga iwo owononga dziko lapansi.’ M’kupita kwa nthawi, anthu ndi nyama adzakhala pa mtendere monga mmene Mulungu anafunira pachiyambi.—Chivumbulutso 11:18; Yesaya 11:6-9.
[Mapu pamasamba 24, 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kumene Nyamazi Zimapezeka
□ Kumene zinkapezeka kale
▪ Kumene zikupezeka panopa
NORTH AMERICA
CENTRAL AMERICA
SOUTH AMERICA