Kankhono Kam’madzi Kamene Kamakumba Modabwitsa
Panagona Luso!
Kankhono Kam’madzi Kamene Kamakumba Modabwitsa
● Ngakhale kuti kankhono kamene kali pachithunzipa kamaoneka ngati sikangakhale ndi mphamvu zokwanira zokumbira mumchenga, kamakumba mofulumira mumchenga wogwirana kwambiri. Poona zimenezi, anthu ena anati kakanakhala kuti kamachita nawo mpikisano, bwenzi kakumapambana nthawi zonse. Ngakhale anthu ochita kafukufuku anagoma nako. Pulofesa wina, dzina lake Anette Hosoi, anati: “Titaona tinkhonoti, tinadziwa kuti payenera kukhala zinthu zinazake zodabwitsa zimene timachita.” Kodi chinsinsi cha tinkhono timeneti n’chiyani?
Taganizirani izi: Kankhono kameneka kamavinitsavinitsa phazi lake pokumba mumchenga ndipo kamapanga kadzenje kakang’ono kamene kamadzaza mwamsanga ndi madzi komanso mchenga. Kenako kankhonoka kamakwera m’mwamba ndi kutsika pansi kwinaku kakutsegula ndi kutseka chiganamba chake. Zimenezi zimachititsa kuti padzenjepo pafewe ndipo kenako kamakumba mosavutikira. Kankhonoka kamatha kukumba dzenje lalitali masentimita 70, ndipo pa sekondi iliyonse kamakumba sentimita imodzi. Kakalowa m’dzenjemo, zimakhala zovuta kwambiri kuti munthu akasolole. Ndipotu mphamvu zimene kamagwiritsa ntchito kuti kamatirire kudzenjeko n’zochepa kwambiri kuyerekeza ndi mphamvu zimene nangula amafunika kuti amatirire pansi. Nangula amafunika mphamvu zowirikiza ka 10 kuyerekeza ndi mphamvu za kankhonoka.
Akatswiri a zopangapanga anatengera tinkhonoti popanga nangula wamakono kwambiri. Hosoi anati: “Nangula ameneyu amatseguka ndi kutsekeka komanso amatha kukwera m’mwamba ndi kutsika pansi mofanana ndi mmene tinkhono tija timachitira.” Nangula wamphamvu ndiponso wamakono ameneyu angathe kugwiritsidwa ntchito pa sitima zam’madzi zochitira kafukufuku, makina akuluakulu oyandama panyanja okumbira mafuta, komanso zida zophulitsira mabomba a pansi pa nyanja.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti tinkhono timeneti tikhale ndi luso lotha kukumba maenje, kapena alipo amene anatipanga?
[Chithunzi patsamba 23]
Nangula ameneyu anamupanga kuti azigwira ntchito ngati tinkhonoti
[Mawu a Chithunzi]
Razor clams: © Philippe Clement/naturepl.com; “smart” anchor: Courtesy of Donna Coveney, Massachusetts Institute of Technology