Mapiko a Tombolombo
Panagona Luso!
Mapiko a Tombolombo
● Pali atombolombo ena amene amatha kuuluka osakupiza mapiko awo kwa masekondi 30 popanda kugwa pansi. Kodi chinsinsi chawo n’chotani? Mapiko a kachilomboka anapangidwa moti kasamalimbane kwambiri ndi mphepo pouluka. Ndipo zimenezi n’zosiyana ndi mmene mapiko a ndege zambiri amapangidwira.
Taganizirani izi: Mapiko a kachilomboka ndi opyapyala kwambiri ndipo ali ndi ngalande ngati mmene amakhalira malata a nyumba. Ngalandezi zimachititsa kuti mapiko a kachilomboka asamapindike kakamauluka. Asayansi atulukiranso kuti ngalandezi zimathandiza kuti kachilomboka kazikwera m’mwamba mofulumira kakamayamba kuuluka. Magazini ya New Scientist inati: “Kachilomboka kakamauluka, mphepo ina imadutsa m’ngalandezo ndipo mphepoyi imathandiza kukankhira kachilomboka m’mwamba.”
Katswiri wina wokonza ndege dzina lake Abel Vargas, pamodzi ndi anzake, atafufuza mmene mapiko a tombolombo amagwirira ntchito, anati: “Tikhoza kutengera kapangidwe ka mapiko a zinthu zamoyo popanga mapiko a tindege ting’onoting’ono.” Tindege timene katswiriyu ankanena timakhala tating’ono kwambiri moti munthu akhoza kutiika m’manja. Tindegeti timatha kukhala ndi makamera kapena zipangizo zina, ndipo amatigwiritsa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, amatitumiza kukafufuza zinthu kudera kumene kwachitika tsoka linalake, kapena kutitumiza m’mlengalenga kuti tikaunike mmene mpweya ukuwonongekera m’chilengedwe.
Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti mapiko a tombolombo akhale opyapyala kwambiri komanso akhale ndi ngalande? Kapena kodi alipo amene anawapanga?
[Chithunzi patsamba 25]
Kandege kofanana ndi tombolombo kameneka kamalemera mamiligalamu 120 okha ndipo ndi kotalika masentimita 6 m’lifupi mwake. Kalinso ndi mapiko opyapyala kwambiri omwe amayendera magetsi
[Mawu a Chithunzi]
© Philippe Psaila/Photo Researchers, Inc.