Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khoti Lina ku Spain Linagamula Kuti Mayi Wina Ali ndi Ufulu Wolera Ana Ake

Khoti Lina ku Spain Linagamula Kuti Mayi Wina Ali ndi Ufulu Wolera Ana Ake

Khoti Lina ku Spain Linagamula Kuti Mayi Wina Ali ndi Ufulu Wolera Ana Ake

● Kodi mungamve bwanji ngati mutaimbidwa mlandu wakuti simukulera bwino ana anu? Bwanji ngati munthu wina atanena kuti ana anu amalephera kukhala bwino ndi anthu, sangathe kusiyanitsa chabwino ndi choipa ndipo sakhoza kusukulu chifukwa cha mmene mumawalerera?

Zimenezi n’zimene zinachitikira Rosa López, mayi wa ku Spain yemwe ali ndi ana aakazi awiri. Bambo wa anawa, yemwe ukwati wake ndi Rosa unatha, anapita kukhoti n’cholinga choti akapatsidwe chilolezo cholanda mayiyo anawo. Rosa ndi wa Mboni za Yehova ndipo mwamunayo ananena kuti chipembedzo cha mayiyo chikuwononga anawo. Iye ananena kuti zimene anawo amaphunzira kuchipembedzo chawo zikuwalepheretsa kukhala bwino ndi anthu, kukhoza bwino kusukulu, komanso kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Khoti laling’ono litamuuza kuti mfundo zake n’zosamveka, mwamunayo anakadandaula ku khoti lalikulu.

Pa nkhani yokhudza kulera ana, khoti limayesetsa kuunika nkhaniyo bwinobwino. Sililowerera m’nkhani za chipembedzo kapena kulimbana ndi zimene munthu amakhulupirira. M’malomwake, limangoona zinthu ngati izi: Kodi mwanayo akupatsidwa ufulu wake? Kodi kholo limene likukhala ndi mwanayo likumulera bwino? Kodi ndi kholo liti limene lingakwanitse kusamalira bwino mwanayo?

Pofufuza nkhaniyi, khotili linapeza dokotala wodziwa za maganizo kuti afunse mafunso anawo ndi makolo awo. Kodi dokotalayo anapeza zotani? Dokotalayo anapeza kuti anawo akukula bwinobwino, ngakhale kuti analeredwa ndi mayi awo kwa zaka 6. Anawo ankakhoza bwino kusukulu ndiponso ankakhala bwino ndi anthu a m’banja lawo komanso ndi anthu ena. Pogwiritsa ntchito zimene dokotalayo anapeza komanso zimene makolowo ananena, khotilo linanena kuti palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti “anawo asokonezedwa maganizo kapena khalidwe mwanjira iliyonse chifukwa chokula ndi anthu a Mboni za Yehova.” Khotilo linanenanso kuti zimene mwamunayo ankanena “zinali zongopeka ndipo zinalibe umboni uliwonse.”

Chifukwa chodana ndi chipembedzo cha Mboni za Yehova kapena chifukwa chouzidwa mabodza, anthu ena amanena kuti ana a Mboni za Yehova saleredwa bwino ndipo amamanidwa zinthu zimene ana onse amayenera kukhala nazo. Koma zoona zake n’zakuti kulera ana mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo si kuwazunza. Anawo akakula, amadzakhala anthu achikondi, anzeru, ndiponso odziwa kukhala bwino ndi anthu.—Aefeso 6:4; 2 Timoteyo 3:15-17.

[Chithunzi patsamba 14]

Khoti linalamula kuti Rosa López apitirize kukhala ndi ana ake