Muzinyadira Khungu Lanu
Muzinyadira Khungu Lanu
● Anthu ena ku Africa, Asia, Caribbean ndiponso ku Middle East amaona kuti munthu akakhala ndi khungu loyera ndiye kuti ndi wotsogola ndiponso wachuma. Choncho, amuna ndi akazi ena m’madera amenewa amadzola mafuta oyeretsa khungu koma nthawi zina zimenezi zimawabweretsera mavuto.
Mafuta ena oyeretsa khungu amakhala ndi mankhwala enaake otchedwa hydroquinone. Kuipa kwa mankhwalawa n’koti amachititsa kuti maselo a pakhungu amene amapanga mtundu wa khungu lathu asakule, ndipo zikatere khungu limalephera kudziteteza ku cheza choipa chochokera kudzuwa. Komanso mankhwalawa amalowerera mkati mwa khungu ndipo nthawi zina amawononga maselo ena a m’thupi. Zimenezi zimachititsa kuti khungu lizioneka lokalamba. Nthawi zinanso mankhwalawa amayambitsa matenda a khansa. Mafuta ena amakhala ndi mankhwala otchedwa mercury, omwenso ndi oopsa kwambiri.
Komanso munthu akadzola mafutawa kwa nthawi yaitali, amatha kutuluka zilonda pakhungu. Komanso khungu limafewa kwambiri ndipo ngati munthuyo atavulala, khungulo limavuta kusoka. Mankhwalawa akalowa m’magazi, amatha kuwononga chiwindi, impso, kapena ubongo ngakhalenso kupangitsa kuti ziwalo zina m’thupi zisiye kugwira ntchito.
N’zochititsa chidwi kuti pamene anthu ena amafuna kuti khungu lawo liyere, anthu enanso amene ali ndi khungu loyera amafunitsitsa kuti khungu lawo lizioneka loderapo ndipo amachita zimenezi pokhalitsa pa dzuwa. Dzuwa ndi lofunika chifukwa limatipatsa vitamini D, koma kukhalitsa pa dzuwa makamaka masana n’koopsa kwambiri. Ngati khungu lanu layamba kuda ndiye kuti lawonongeka kale ndipo kudako ndi chizindikiro chakuti likuyesetsa kudziteteza kuti lisapitirire kuwonongeka. Komatu sikuti lingapitirize kudziteteza kwa nthawi yaitali. Ena amaganiza kuti ngati atadzola mafuta odziteteza ku dzuwa, khungu lawo silingawonongeke. Koma mafuta amenewa ndi osathandiza kwenikweni, chifukwa ngati mutapitiriza kukhala pa dzuwapo, khungu lanu likhoza kuwonongeka kwambiri ndipo mungathe kudwala khansa.
Choncho, Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse likulimbikitsa anthu kuti “azifalitsa uthenga wakuti aliyense azisangalala ndi khungu lake” chifukwa kuchita zimenezi “n’kofunika kwambiri kuti anthu apewe matenda a pakhungu.” Choncho, anthu anzeru sadandaula kwambiri ndi kaonekedwe ka khungu lawo, chifukwa amadziwa kuti chofunika kwambiri ndi “munthu wa mkati, wa mu mtima,” yemwe kukongola kwake kumawonjezereka m’kupita kwa nthawi pamene khungu limakalamba.—1 Petulo 3:3, 4; Miyambo 16:31.