Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Konzekerani Kukumana ndi Mavuto

Konzekerani Kukumana ndi Mavuto

Konzekerani Kukumana ndi Mavuto

“Ndinaganiza zosiya kusuta n’cholinga choti ndisawononge thanzi la mwana wathu wakhanda. Choncho, ndinaika m’nyumba mwathu chikwangwani chakuti ‘Osasuta Fodya.’ Koma patangopita ola limodzi ndinali ndi chibaba champhamvu kwambiri, ndipo ndinayatsa ndudu n’kuyamba kusuta.”—Anatero Yoshimitsu, wa ku Japan.

ZIMENE zinachitikira Yoshimitsu zikusonyeza kuti anthu amene amafuna kusiya kusuta amakumana ndi mavuto. Kafukufuku akusonyeza kuti anthu 90 pa 100 alionse amene amafuna kusiya, akangosiya kwa nthawi yochepa, amayambiranso kusuta. Komabe, ngati mukuyesetsa kuti musiye kusuta, muyenera kukonzekera kukumana ndi mavuto. Kodi mavuto ena amene mungakumane nawo ndi otani?

Chibaba: Munthu amakhala ndi chibaba champhamvu pambuyo pa masiku angapo akangosiya kusuta, koma zimenezi zimayamba kuchepa pakangodutsa milungu iwiri. Munthu wina amene anasiya kusuta ananena kuti mkati mwa masiku amenewa “chilakolako chofuna kusuta chimasinthasintha, nthawi zina chimakhala champhamvu nthawi zina chochepa.” Ngakhale patapita zaka zambiri, nthawi zina chibaba chofuna kusuta chimafika mwadzidzidzi. Ngati zimenezi zitakuchitikirani, musapupulume. Muyenera kudikira kaye mwina mphindi zisanu kapena kuposa, kenako mungaone kuti chibabacho basi chatha.

Mavuto ena obwera chifukwa chosiya kusuta: Koyambirira, munthu amalephera kuchita zinthu mochangamuka kapena mokhazikika ndiponso amanenepa kwambiri. Nthawi zinanso amamva kupweteka ndi kuyabwa m’thupi, sachedwa kuchita thukuta, amasokomola, ndiponso sachedwa kupsa mtima kapena kukhumudwa. Koma mavutowa amatha pakapita milungu 4 kapena 6.

Panthawi yovuta imeneyi, pali zinthu zingapo zimene zingakuthandizeni. Mwachitsanzo:

● Muzigona nthawi yaitali.

● Muzimwa madzi ndiponso madzi azipatso ambiri. Komanso muzidya chakudya cha magulu onse.

● Muzichita masewera olimbitsa thupi.

● Muzipuma mokoka mpweya ndipo muziganizira kuti tsopano mwayamba kupuma mpweya wabwino kuyerekezera ndi umene munkapuma poyamba.

Zinthu zoyambitsa chibaba. Muyenera kusiya kuchita zinthu kapena kuganizira zinthu zimene zimakuyambitsirani chibaba. Mwachitsanzo, mwina kale munkakonda kusuta mukamamwa mowa kapena zakumwa zina. Choncho, ngati mukufuna kusiya kusuta muyeneranso kusiya kumwa zakumwazo. M’kupita kwa nthawi mukhoza kuyambiranso kumwa.

Akatswiri amanena kuti ngakhale mutasiya kusuta, maganizo ofuna kusuta amakhalapobe. Mwachitsanzo, Torben yemwe tamutchula koyambirira uja, anati: “Papita zaka 19 kuchokera pamene ndinasiya kusuta, komabe nthawi zina ndikamamwa khofi, maganizo ofuna kusuta amandibwerera.” Komabe dziwani kuti nthawi zambiri maganizo amenewa amachepa pakapita nthawi.

Koma mowa ndi wosiyana ndi zakumwa zina. Panthawi yonse imene mukuyesetsa kusiya kusuta, mungachite bwino kusiya kumwa mowa komanso kupewa malo amene anthu amamwerako mowa. Anthu ambiri amene amayambiranso kusuta, amachita zimenezi chifukwa chakuti anamwa mowa. Kodi n’chiyani chimachititsa zimenezi?

● Mowa, ngakhale wochepa kwambiri, umachititsa kuti munthu akamasuta azimva bwino.

● M’malo ambiri omwera mowa, mumakhala anthu ambiri osuta fodya.

● Munthu akaledzera amalephera kudziletsa. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: ‘Vinyo amawononga nzeru za munthu.’—Hoseya 4:11.

Anthu ocheza nawo: Muzisankha anthu abwino ocheza nawo. Musamakonde kucheza ndi anthu amene amasuta kapena amene angakulimbikitseni kusuta. Komanso muzipewa anthu amene angamakunyozeni chifukwa chakuti mwasiya kusuta.

Kukhumudwa kapena kukwiya: Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu awiri mwa anthu atatu aliwonse amene amayambiranso kusuta amachita zimenezi chifukwa chokhumudwa kapena kukwiya. Ngati zinthu zimenezi zingakuchititseni kuti mukhale ndi chibaba chofuna kusuta, muyenera kusintha zimene mukuchita n’kuyamba kuchita zinthu zina monga kumwa madzi, kutafuna chingamu, kapena kupita kokayenda. Muziyesetsa kuganizira zinthu zabwino zokhazokha. Mungapemphere kwa Mulungu kapena kuwerenga Baibulo.—Salmo 19:14.

Musamapeze Zifukwa Zodzikhululukira.

Ndingosuta kamodzi kokha.

Zoona zake: Ngakhale kusuta kamodzi kokha kungachititse kuti fodya akhale mu ubongo wanu kwa maola atatu. Ndipo zimenezi zingakuchititseni kuti musute kangapo.

Kusuta kumandithandiza kwambiri ndikakhumudwa.

Zoona zake: Kafukufuku akusonyeza kuti fodya amachititsa kuti munthu asamachedwe kukhumudwa. Anthu amene asiya kusuta fodya, koyambirira angamakhumudwe koma m’kupita kwa nthawi vutoli limatha. Choncho, ngati munthu amene wangosiya kumene kusuta atayambiranso kusuta, angamaone kuti fodya akumuthandiza kuti asamakhumudwe.

Posiya kusuta panadutsa.

Zoona zake: Maganizo akuti simungathe kusiya kusuta ndi ofoola. Baibulo limati: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Choncho, pewani maganizo akuti ndinu munthu wolephera. Munthu aliyense amene akufunadi kusiya kusuta ndipo amatsatira mfundo zothandiza ngati zimene tafotokoza m’magazini ino, angakwanitse kusiya.

Sindingathe kupirira mavuto amene angabwere chifukwa chosiya kusuta.

Zoona zake: N’zoona kuti kusiya kusuta kungabweretse mavuto aakulu, koma pakangopita milungu ingapo akhoza kuchepa. Choncho, muyenera kulimba mtima. Ngati chibaba cha fodya chitabweranso patapita miyezi kapena zaka zingapo, sichingachedwe kutha ngati inuyo mutatsimikiza kuti musasute.

Ndili ndi matenda ovutika maganizo.

Zoona zake: Ngati muli ndi matenda ovutika maganizo, muyenera kupempha dokotala wanu kuti akuthandizeni kusiya kusuta. Ngati atadziwa kuti mwasiya kusuta, iye angaone mmene angakuthandizireni, mwina angasinthe mankhwala amene akukupatsani.

Ndikayambiranso kusuta, ndimaona kuti ndine wokanika.

Zoona zake: Anthu ena amayambiranso pambuyo posiya kusuta, choncho mukayambiranso musaganize kuti ndinu wokanika. Munthu akagwa sizitanthauza kuti ali ndi vuto. Koma ngati atagwa n’kungokhala pansi pomwepo osadzuka, tingati munthuyo ali ndi vuto. Ngati mutayesetsabe, m’kupita kwa nthawi mudzakwanitsa kusiya kusuta.

Taganizirani zimene zinachitikira Romualdo, yemwe anakhala akusuta fodya kwa zaka 26 ndipo anasiya kusuta zaka 30 zapitazo. Iye analemba kuti: “Ndikasiya kusuta, nthawi zambiri ndinkayambiranso. Ndipo ndinachita zimenezi kambirimbiri. Nthawi iliyonse imene ndasuta, ndinkaona kuti ndataika. Komabe, kenako ndinatsimikiza zokhala paubwenzi ndi Yehova Mulungu ndipo ndinkamupempha mobwerezabwereza kuti andithandize. Pamapeto pake ndinasiyiratu kusuta.”

Nkhani yotsatira ifotokoza zinthu zinanso zimene mungachite kuti musiye kusuta n’kukhala ndi moyo wosangalala.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 7]

FODYA AMAPHA

Fodya amagwiritsidwa ntchito m’njira zambiri. Nthawi zina amaikidwa m’zakudya kapena m’mankhwala azisamba. Komabe, Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena kuti “kaya waikidwa mu chiyani, fodya amapha.” Izi zili choncho chifukwa chakuti fodya amayambitsa matenda oopsa monga khansa ndiponso matenda a mtima. Ngakhale amayi oyembekezera omwe amasuta amatha kuvulaza mwana wawo wosabadwa. Anthu amakonda fodya wa wamitundu yotsatirayi:

Tindudu ting’onoting’ono topichira pamanja, tomwe n’tofala kwambiri ku mayiko a ku Asia. Tindudu timeneti n’toopsa kwambiri chifukwa timatulutsa phula, nikotini, komanso mpweya woipa wambiri kuposa fodya wamba.

Fodya wopichiridwa patsamba la fodya kapena papepala lopangidwa kuchokeranso ku fodya. Ndudu zimenezi zikangoikidwa pakamwa, ngakhale zisanayatsidwe, fodyayo amalowerera m’thupi.

Fodya wosakaniza ndi timbewu tinatake tonunkhira. Fodya wotereyu amatulutsa phula, nikotini, komanso mpweya wakupha wambiri kuposa fodya wamba.

Kaliwo. Ena amaganiza kuti kugwiritsa ntchito kaliwo posuta fodya n’kosaopsa. Koma anthu amene amachita zimenezi, amatha kudwala khansa ndi matenda ena.

Fodya wosatulutsa utsi. M’gulu limeneli muli fodya wochita kutafuna, kufwenkha ndiponso fodya winawake yemwe ndi wofala kum’mwera chakum’mawa kwa Asia wotchedwa gutkha. Mankhwala oipa a mu fodya ameneyu amalowa m’thupi kudzera mkamwa. Fodya wosatulutsa utsi ndi woopsa mofanana ndi fodya wina aliyense.

Ena amagwiritsa ntchito chipangizo chimene chimachititsa kuti utsi wa fodya uzidutsa m’madzi, asanaumeze. Komabe, zimenezi sizichepetsa matenda amene amayambitsidwa ndi fodya monga khansa ndi matenda ena a m’mapapu.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

MUNGATHANDIZE BWANJI MUNTHU WINA KUSIYA KUSUTA FODYA?

Muzimulimbikitsa. Kulimbikitsa ndiponso kuyamikira munthu amene akuyesetsa kusiya kusuta n’kofunika kwambiri kuposa kumangomudzudzula komanso kum’patsa malangizo. Ndi bwino kunena kuti, “Ndikuganiza kuti mutayesanso mukwanitsa,” m’malo monena kuti “Mwalepheranso?”

Muzikhululuka. Munthu amene akuyesetsa kuti asiye kusuta akachita zinthu zosonyeza kuti wakwiya kapena wakhumudwa nanu, muzimukhululukira. Muzilankhula naye mokoma mtima. Mwachitsanzo, munganene kuti, “Ndikudziwa kuti n’zovuta, koma ndikusangalala kuti mumayesetsa.” Pewani kunena kuti, “Panopa ndiye mwawonjeza, ndipo zinaliko bwino panthawi yomwe munkasuta.”

Muzimukonda nthawi zonse. Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Choncho, muziyesetsa kuchita zinthu moleza mtima ndiponso mwachikondi “nthawi zonse” ndi munthu amene akufuna kusiya kusuta fodya, kaya munthuyo akuchita zotani panthawiyo.