Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
“Anthu amene sasuta, amene amachita masewera olimbitsa thupi, amene samwa mowa mopitirira muyezo ndiponso amene amadya zipatso zosiyanasiyana zisanu patsiku kapena masamba, amakhala ndi moyo wautali, mwina zaka 14, kuyerekeza ndi anthu amene sachita zimenezi.” Kafukufukuyu anachitika kwa zaka 11, ndipo anali wokhudza anthu 20,000.—UC BERKELEY WELLNESS LETTER, U.S.A.
“Kuwerenga kumathandiza kwambiri kuthetsa nkhawa. . . . Ngakhale kuwerenga mphindi 6 zokha n’kokwanira kuti muthetse nkhawa.”—INDIA TODAY INTERNATIONAL, INDIA.
Anthu Akutaya Mabwato Awo
Nyuzipepala ya The New York Times inanena kuti: “Mavuto a zachuma akuchititsa kuti anthu ambirimbiri ku United States azitaya mabwato awo. Eni mabwatowa akufututa maina awo pa mabwatowa, kuchotsa nambala puleti, ndipo kenako n’kungowasiya penapake kapena kuwaponya m’madzi. Nthawi zina amachita zimenezi n’cholinga choti apatsidwe ndalama za inshuwalansi. Kodi n’chiyani chikuchititsa zimenezi? “Ena . . . akuchita zimenezi chifukwa ali ndi ngongole zambiri zoti abweze. Mabwatowa akawonongeka pamafunika ndalama zambiri kuti akonzedwe, choncho eni ake akuona kuti akungowawonongera ndalama.” Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Eni mabwatowa sangawagulitse chifukwa pali mabwato ambiri amene akugulitsidwa koma anthu ogula ndi ochepa. Kusungitsanso mabwatowa kumafuna ndalama zambiri. Komanso kuti awataye motsatira ndondomeko yake sangakwanitse chifukwa kumafunanso ndalama zambirimbiri.”
Ana Akuda Nkhawa ndi Mmene Akuonekera
Nyuzipepala ya ku Sydney ya Sunday Telegraph inanena kuti ana azaka zinayi “akuyesetsa kuti asinthe maonekedwe awo n’cholinga choti azioneka monga mmene anthu ambiri amafunira.” Kafukufuku wokhudza zakudya zimene anawa amadya komanso masewera amene amakonda kuchita anasonyeza kuti anawa amada nkhawa kwambiri ndi thupi lawo. Ana aakazi amafuna kuchepa thupi kwambiri pamene aamuna amafuna kuoneka ngati akatswiri onyamula zitsulo. Anthu amene anachita kafukufukuyu ananena kuti: “Zikuoneka kuti anawa amafuna kuchepa thupi chifukwa chotengera maganizo a amayi awo, omwe sasangalala ndi mmene amaonekera.”
Ana Akugula Zinthu pa Intaneti Makolo Awo Osadziwa
Nyuzipepala ya The Daily Telegraph ku London inanena kuti: “Mwana mmodzi pa asanu alionse [ku United Kingdom] akugula zinthu pa Intaneti popanda chilolezo cha makolo ake, ndipo theka la ana amenewa amagwiritsa ntchito makadi a ngongole a makolo awo.” Ana ambiri amadziwa kumene angapeze zimene akufuna pa Intaneti ndiponso manambala achinsinsi amene makolo awo amagwiritsa ntchito akafuna kugula zinthu pa Intaneti. Manambala achinsinsi amenewa amathandizanso anawo kuti asavutike kupeza manambala a makadi a ngongole a makolo awo. Makolo ambiri amaganiza kuti ana awo sangagule zinthu pa Intaneti iwo osadziwa. Nyuzipepalayi inanena kuti makolowo amaganiza kuti ana awo akudziwa zinthu zochepa kwambiri, pamene anawo amadziwa zinthu zambiri zedi. Zimenezi zikuchititsa mavuto ambiri monga kuberedwa ndi anthu achinyengo. Nyuzipepalayi inalangiza makolo amene amagula zinthu pa Intaneti kuti: “Musamasunge zinsinsi zanu zokhudza makadi anu a ndalama pa Intaneti, mukamagwiritsa ntchito Intaneti, musamangoti uku mwapita ukunso mwapita, ndipo mukamaliza muzitseka adiresiyo.”